Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 2/8 tsamba 29-30
  • Kodi Nkusudzula kwa Mtundu Wotani Kumene Mulungu Amada?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nkusudzula kwa Mtundu Wotani Kumene Mulungu Amada?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Musachite Mosakhulupirika”
  • Chitsanzo cha Mulungu Mwiniyo
  • Kusudzulana
    Galamukani!—1999
  • Tizilemekeza “Chimene Mulungu Wachimanga Pamodzi”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Zimene Baibulo Limanena pa Nkhani Yothetsa Banja ndi Kupatukana
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Kodi Ukwati Wanu Umakondweretsa Yehova?
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 2/8 tsamba 29-30

Lingaliro la Baibulo

Kodi Nkusudzula kwa Mtundu Wotani Kumene Mulungu Amada?

“MAVUTO amene chisudzulo changa chinadzetsa anali ambiri,” analemba motero mkazi wina Wachikristu amene mwamuna wake anali wosakhulupirika. “Nyengo ya kusintha siili nthaŵi yofeŵa. Ndinafunikira kusintha osati mwamalingaliro okha komanso m’zandalama ndi mwauzimunso. Ndinakayikira ngati kuti Yehova akadalitsa chosankha changa, podziŵa kuti Malemba amati iye amada chisudzulo. Imeneyi inali nkhaŵa yanthaŵi zonse.”

Pamene ukwati utha, zovuta sizimatha. Mavuto ambiri atsopano amabuka mwadzidzidzi. Malingaliro—a tondovi, kusungulumwa, liwongo—amene amangobuka mwadzidzidzi. Kulimbirana kuyenerera kwa kusunga ana. Mwana wamkazi kapena wamwamuna akumalirira Amayi wake kapena Atate wake. Mavuto azandalama amene amapanikiza. Kuyesayesa kupirira chikhumbo cha mtundu wa chikondi wopezeka muukwati mokha.

Ndiyeno pali lingaliro la Mulungu loyenera kuliganizira. Baibulo limati Mulungu ‘amada kusudzula.’ (Malaki 2:16, NW) Kodi mawu ameneŵa amatanthauza kuti Mulungu amada kusudzula kulikonse? Motero, kodi Mkristu, ayenera kukhala waliwongo chifukwa cha kufuna chisudzulo pamene mnzake wa muukwati wakhala wosakhulupirika? Kuti tipeze mayankho, tiyeni tipende mikhalidwe ya m’tsiku la Malaki imene inachititsa Mulungu kunena kuti amada chisudzulo.

“Musachite Mosakhulupirika”

Malaki analosera pambuyo pa 443 B.C.E., pafupifupi zaka zana limodzi andende Achiyuda atabwerako ku Babulo. Mikhalidwe yonyansa inali itabuka m’Yuda, makamaka pakati pa ansembe. (Malaki 2:7-9) Machitachita onga kunama, chigololo, chinyengo, ndi kutsendereza zinali zofala pakati pa Aisrayeli ambiri. (Malaki 3:5) Mikhalidwe imeneyi inabutsa kukayikira kwambiri moti ena anati: “Kutumikira Mulungu nkwachabe.”—Malaki 3:14.

Kunyansa kwa chipembedzo ndi makhalidwe kwa m’tsiku la Malaki kunasonyezedwanso ndi kutha kwa ulemu wa ukwati. Amuna ambiri Achiisrayeli anali kusudzula akazi aunyamata wawo, mwimamwake kuti akwatire akazi achicheperepo achikunja. Guwa la nsembe la Yehova linadzala ndi misozi ya akazi okanidwawo amene anadza kukachisi kudzalira ndi kuusa moyo pamaso pa Mulungu.—Malaki 2:13-15.

Kodi Yehova anamva motani ponena za kusudzulana koteroko? Kupyolera mwa Malaki anachenjeza kuti: “Sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense. Pakuti ndidana nako kuleka [“kusudzula,” NW] kumene, ati Yehova Mulungu wa Israyeli . . . chifukwa chake sungani mzimu wanu kuti musachite mosakhulupirika.” (Malaki 2:15, 16) Malinga ndi kunena kwa Theological Wordbook of the Old Testament, liwu Lachihebri lotembenuzidwa ‘kuchita monyenga’ limatanthauza “kuchita mosaona mtima mwachinyengo, (kuchita) mosakhulupirika.” Pa Salmo 59:5, liwu lina la verebu yofananayo latembenuzidwa kuti “onyenga.”

Polingalira mikhalidwe yoteroyo, tikhoza kumvetsetsa mawu a pa Malaki 2:16: “Ndidana nako [kusudzula].” Yehova amada kusudzula kumene kumaloŵetsamo kuleka mosayenerera mnzanu wa muukwati kotero kuti mukwatire wina. Mwachitsanzo, mwamuna amene achita chigololo kenako nkusudzula mkazi wake wopanda chifukwa mosiyana ndi chifuniro cha mkaziyo kapena amkakamiza kuti asudzule mwamuna wake kotero kuti mwamunayo akwatire mkazi wina kulidi kuchita mosakhulupirika ndi mkazi wake. Mchitidwe wonyenga, wosakhulupirika umenewo kwa mnzanu wa muukwati wopanda chifukwayo uli tchimo lalikulu pamaso pa Mulungu. Mwamuna amene atsiriza zaka zabwino koposa za moyo wa mkazi ndiyeno ndikumtaya, mwinamwake chifukwa cha mkazi wina wachicheperepo, alidi wonyenga.a

Bwanji nanga, za wamuukwati amene asankha kusudzula mnzake amene wachita chigololo? Kodi Mulungu amadanso zisudzulo zotero?

Chitsanzo cha Mulungu Mwiniyo

Kodi Mulungu angadziŵedi mmene kumamvekera kuyang’anizana ndi chosankha chakuti kaya musudzule mnzanu wa muukwati wachigololoyo kapena ayi? Kunena mophiphiritsira, Yehova anadzilingalira kukhala wokwatira mtundu wakale wa Israyeli mwa pangano lake kwa iwo. (Yesaya 54:1, 5, 6; 62:1-6; Yeremiya 31:31, 32) Monga mwamuna, Yehova anali wokhulupirika nthaŵi zonse, sanatembenuzire chikondi chake kwa mitundu ina. (Salmo 147:19, 20; Amosi 3:1, 2) Koma bwanji ponena za Israyeli? Kodi mtunduwo unadzisonyeza kukhala mkazi wotani?

Monga mtundu wonse, unakhaladi wosakhulupirika mobwerezabwereza papangano lija, potsirizira pake anafika pamkhalidwe wofotokozedwa m’pemphero lolembedwa pa Danieli 9:5, 6 kuti: “Tachimwa, tachita mphulupulu, tachita zoipa, tapanduka, kupambuka ndi kusiya maneno anu ndi maweruzo anu; sitinamvera atumiki anu aneneri, amene ananena m’dzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu, ndi anthu onse a m’dziko.” Pamaso pa Yehova, kusakhulupirika koteroko kunali ngati kuchita chigololo kwa mkazi wokwatiwa.—Yeremiya 3:1.

Pambuyo pa zaka mazana ambiri za chipiriro ndi kuleza mtima, kodi Yehova anachitanji? Mwa kuchitapo kanthu mwamphamvu mwachiweruzo, choyamba akumatulutsa mafuko akumpoto kenako mafuko akummwera m’dziko lawo kupita kundende, Yehova, kwenikweni, anadzisudzula iye mwini kwa mtundu umenewo. (Yeremiya 3:8; Danieli 9:11, 12) Motero polingalira chitsanzo chake, kodi Yehova Mulungu angade motani zimenezo pamene wamuukwati wosalakwa asankha kusudzula mnzake yemwe wakhala wosakhulupirika pa choŵinda chaukwati?

Ukwati uli makonzedwe opatulika pamaso pa Mulungu, ndipo awo amene amaloŵamo sayenera kuona mopepuka choŵinda chimene achiŵinda. (Ahebri 13:4) Koma ngati wamuukwati akhala wosakhulupirika pa choŵinda mwakuchita “dama,” Mulungu amapatsa wosalakwayo kuyenera kwa kusankha kaya kumkhululukira kapena kumsudzula. (Mateyu 19:9) Chimenecho nchosankha chovuta, chimene wosalakwa yekhayo ndiye ayenera kuchipanga. Ngati wosalakwayo asankha kuthetsa ukwatiwo, sayenera kudzimva kukhala waliwongo chifukwa cha kufuna chisudzulo. Kumbukirani kuti Yehova amada, osati kusudzula konse, koma mtundu wa kusudzula kumene kumaloŵetsamo kuleka wina wamuukwati kotsutsana ndi malemba kotero kuti akwatire wina.b

[Mawu a M’munsi]

a M’Malemba onse, Yehova Mulungu amanena ponena za iyemwini kuti amada maganizo ndi makhalidwe auchimo. (Deuteronomo 16:22; Miyambo 6:16-19; 8:13; Yesaya 1:14; 61:8) Polingalira zimenezi, kusudzula konenedwa pa Malaki 2:16 kuyeneranso kukhala kwa mtundu wauchimo pamaso pake.

b Kusudzula kuti muchoke kwa mnzanu wamuukwati wachigololo kuli chosankha chaumwini. Kuti muone mafotokozedwe a mfundo zosiyanasiyana zimene wamuukwati wosalakwa ayenera kuzipenda posankha kuti kaya ayenera kupeza chisudzulo cha Malemba, chonde onani makope a Nsanja ya Olonda a August 15, 1993, tsamba 5, ndi May 15, 1988, masamba 4 mpaka 7.

[Mawu a Chithunzi patsamba 29]

Historic Costume in Pictures/ Dover Publications, Inc., New York

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena