Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 5/8 tsamba 12-14
  • Kodi Ndani Amene Amagwidwa Nako, Ndipo Nchifukwa Ninji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndani Amene Amagwidwa Nako, Ndipo Nchifukwa Ninji?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mankhwala ndi Zakumwa Zoledzeretsa
  • Vuto la Kadyedwe
  • Ndingatani Makolo Anga Akamaledzera Kapena Kumwa Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kugonjetsa Kumwerekera ndi Zinthu Zoledzeretsa
    Galamukani!—1994
  • Pamene Zochita Zikhala Zomwerekeretsa
    Galamukani!—1994
  • Mmene Kumwa Mowa Mopitirira Muyeso Kumakhudzira Thanzi la Munthu
    Galamukani!—2005
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 5/8 tsamba 12-14

Kodi Ndani Amene Amagwidwa Nako, Ndipo Nchifukwa Ninji?

PAMENE mukuyendetsa galimoto lanu mumsewu waukulu, mukumva kulira kosokosa kwachilendo mu injini. Kodi mudzachita motani? Kodi mudzatsegula boneti ndi kuyang’ana mu injiniyo kuti muone vuto lake? Kapena kodi mudzangotsegula kwambiri wailesi yanu ya m’galimoto kuti musamve phokoso la mu injiniyo?

Yankho lake nlachionekere, komabe anthu amene ali omwerekera amapanga zosankha zolakwa nthaŵi zonse—osati ndi galimoto zawo, koma ndi miyoyo yawo. Mwa kudzimwerekeretsa ndi zinthu zonga mankhwala oledzeretsa, zakumwa zoledzeretsa, ndi chakudya, ambiri amayesayesa za kuiŵala mavuto awo mmalo mwa kulimbana nawo mwachipambano.

Kodi ndimotani mmene munthu angadziŵire ngati iyeyo ali womwerekera? Dokotala wina akufotokoza zimenezi mwanjira iyi: “Kwakukulukulu, kugwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa kapena zochita kuli kumwerekera ngati mupitirizabe kukuchita mosasamala kanthu za mavuto amene kungadzetse m’moyo wanu.”

Pamene zili choncho, kaŵirikaŵiri munthuyo amakhala ali ndi vuto lalikulu kwambiri, limene limafunikira kupendedwa, kuti khalidwe la kumwerekerako lisinthidwe.

Mankhwala ndi Zakumwa Zoledzeretsa

Kodi nchiyani chimene chimayambitsa munthu kumwerekera ndi mankhwala ndi zakumwa zoledzeretsa? Chitsenderezo cha ausinkhu wofanana ndi chidwi kaŵirikaŵiri nzimene zimachita mbali yaikulu, makamaka kwa achichepere. Ndithudi, chifukwa chimene anthu ambiri amamwerekerera ndicho mayanjano awo oipa ndi awo amene amagwiritsira ntchito molakwa zakumwa zoledzeretsa ndi mankhwala. (1 Akorinto 15:33) Zimenezi mwina zingafotokoze mapendedwe a ku United States amene anavumbula kuti 41 peresenti ya akusukulu ya sekondale a kalasi lotsiriza amaledzera ndi moŵa milungu iŵiri iliyonse.

Komabe, pali kusiyana pakati pa kugwiritsira ntchito molakwa ndi kumwerekera. Ambiri amene amagwiritsira ntchito molakwa zinthu sali omwerekera.a Ameneŵa akhoza kuleka kugwiritsira ntchito molakwako ndiyeno osakhalanso ndi chikoka cha kubwereranso kumkhalidwewo. Koma awo amene ali omwerekera amapeza kuti sangathe kuleka. Ndiponso, chisangalalo chilichonse cha kupeza bwino chimene poyamba anapeza chimaphimbidwa ndi chisoni. Buku lakuti Addictions limafotokoza kuti: “Njira yeniyeni ya omwerekera njakuti, panthaŵi ina yake m’moyo wawo, amayamba kudzida, ndipo amakhala ovutika mtima kwambiri chifukwa cha mphamvu imene kumwerekera kwawo kuli nayo.”

Ambiri amene amadalira pazakumwa zoledzeretsa kapena pamankhwala oledzeretsa amazigwiritsira ntchito monga njira zopulumukira pamavuto a malingaliro. Mavuto otero ngofala kwambiri lerolino. Ndipo zimenezi siziyenera kutidabwitsa kwenikweni, popeza kuti Baibulo limasonyeza ano kukhala “masiku otsiriza” a dongosolo lino la zinthu, pamene kudzakhala “nthaŵi zowawitsa.” Baibulo linaneneratu kuti anthu akakhala “okonda ndalama,” “odzikuza,” “osayera mtima,” “aukali,” “achiwembu,” ndi “otukumuka mtima.” (2 Timoteo 3:1-4) Mikhalidwe imeneyi yapanga malo amene ali oyanja kwambiri kumwerekera.

Mavuto a m’malingaliro a Susan anakhalapo chifukwa cha kuchitiridwa nkhanza muubwana wake. Motero iye anatembenukira pa kugwiritsira ntchito mankhwala a cocaine. “Anandipatsa lingaliro lonyenga la kudzilamulira ndi kudziona kukhala kanthu,” iye akutero. “Anandipatsa lingaliro la kukhala ndi mphamvu zimene ndinalibe tsiku ndi tsiku.”

Kupenda kwina kofalitsidwa kochitidwa pa anyamata osinkhuka omwerekera kunasonyeza kuti oposa chigawo chimodzi mwa zitatu anali atachitiridwa nkhanza mwakuthupi. Kupenda kwina kwa achikulire achikazi 178 omwerekera ndi moŵa kunasonyeza kuti 88 peresenti inachitiridwa nkhanza m’njira zosiyanasiyana. Baibulo pa Mlaliki 7:7 limati: “Nsautso iyalutsa wanzeru.” Munthu wovutika ndi malingaliro chifukwa cha zokumana nazo zina zoipa m’moyo m’kupita kwa nthaŵi angatembenukire pamankhwala kapena pazakumwa zoledzeretsa popanda kulingalira bwino kuti apeze mpumulo.

Koma mankhwala oledzeretsa ndi zakumwa sindizo zomwerekeretsa zokha zimene zilipo.

Vuto la Kadyedwe

Vuto la kadyedwe (kamene anthu ena odziŵa amakatcha kumwerekera) nthaŵi zina kamatumikira monga choiŵalitsa malingaliro osakondweretsa. Mwachitsanzo, ena amagwiritsira ntchito kunenepetsa monga chochititsa zogwiritsa mwala za munthu mwini. “Nthaŵi zina ndimaganiza kuti ndiyenera kukhalabe wonenepa chifukwa chakuti zinthu zonse zimene zili zolakwika m’moyo wanga zikhoza kugwirizanitsidwa nako,” akutero Jennie. “Mwanjira imeneyi ngati wina samandikonda, nthaŵi zonse ndikhoza kuimba mlandu kunenepa kwanga.”

Kwa ena, chakudya chimapereka lingaliro lonyenga la kudzilamulira.b Chakudya chingakhale mbali yokha ya moyo imene munthu angaone kukhala ndi ulamuliro uliwonse. Ambiri amene ali ndi vuto la kadyedwe amaganiza kuti mwina ngolemala. Kuti akulitse malingaliro akudziŵerengera, iwo amayesayesa kupondereza chikhumbo cha thupi lawo cha kufuna chakudya. Mkazi wina anati: “Umachititsa thupi lako kukhala ufumu wa iwe mwini mmene iweyo umakhala wotsendereza wake, wolamulira wankhanza weniweni.”

Zochitika zotchulidwa pamwambapozo sindizo zokha zochititsa kumwerekera ndi mankhwala, zakumwa zoledzeretsa, ndi chakudya. Pangakhale mitundu yosiyanasiyana ya zochititsa imene ingaphatikizidwepo. Akatswiri ena amaperekadi lingaliro la kufanana kwa majini kukumachititsa ena kukhala pangozi ya kumwerekera koposa ena. “Zimene tikuona ndiko kuloŵerana kwa maumunthu, malo okhala, zaumoyo ndi kuvomerezedwa m’chitaganya,” akutero Jack Henningfield wa National Institute on Drug Abuse. “Sitikufuna kupusitsidwa mwa kungopenda chochititsa chimodzi chokha.”

Mulimonse momwe zingakhalire, palibe munthu womwerekera—mosasamala kanthu za chomchititsa kumwerekerako—amene ali wogonjetsedwa mwathupi kapena mwamalingaliro. Chithandizo chilipo.

[Mawu a M’munsi]

a Zowonadi, kugwiritsira ntchito molakwa zakumwa zoledzeretsa kapena mankhwala ena—kaya kochititsa kumwerekera kapena ayi—nkodetsa ndipo kuyenera kukanidwa ndi Akristu.—2 Akorinto 7:1.

b Chidziŵitso china chowonjezereka pa vuto la kadyedwe chingapezedwe m’makope a Awake! December 22, 1990 ndi Galamukani! February 8, 1992.

[Bokosi patsamba 14]

Mliri wa Dziko Lonse wa Kumwerekera

◼ Kufufuza kochitidwa m’Mexico kunasonyeza kuti munthu 1 pa 8 pakati pa azaka za 14 ndi 65 ndi chidakwa chomwerekera.

◼ Wogwira ntchito zaumoyo wa anthu Sarita Broden akusimba za kufalikira kwa kadyedwe kosalongosoka ku Japan. Iye akuti: “Pakati pa 1940 ndi 1965, anthu okhala ndi kadyedwe kosalongosoka anawonjezereka mopitirizabe ndiyeno pambuyo pake kukwera mofulumira ponse paŵiri kwa odwala ogonekedwa m’chipatala ndi ogona kunyumba pakati pa 1965 ndi 1981. Komabe chiyambire 1981, kuwonjezereka kwa odwala anorexia ndi bulimia kwakhala kwakukulu.”

◼ Mu China chiŵerengero cha ogwiritsira ntchito mankhwala a heroin chikuonekera kukhala chikukula mofulumira. Dr. Li Jianhua, amene amagwira ntchito pa Kunming Drug Abuse Research Center, akunena kuti: “Mankhwala a heroin afalikira kuyambira kudera la kumalire kuloŵa mkati, kuchokera kumidzi kuloŵa m’mizinda, ndi kufikira kwa achichepere mpaka kwa ana aang’ono kwambiri.”

◼ Mu Zurich, Switzerland, msika wapoyera wa mankhwala oledzeretsa wa cholinga chofuna kupenda unatha mogwiritsa mwala. “Tinalingalira kuti tikapeza ogulitsa ake, koma tinalephera,” akutero Dr. Albert Weittstein, akumadandaula kuti iwo anali kungokopa ogwiritsira ntchito ake ochokera kutali.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena