Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 5/8 tsamba 18-20
  • Pamene Zochita Zikhala Zomwerekeretsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Zochita Zikhala Zomwerekeretsa
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kumwerekera ndi Ntchito
  • Kumwerekera ndi Wailesi Yakanema
  • Kumwerekera ndi Kutchova Juga
  • Wonjokanimo
  • Ndine Womwerekera! Kodi Ndingaleke Bwanji Kutchova Juga?
    Galamukani!—1993
  • Oseŵera Juga Atsopano—Achichepere!
    Galamukani!—1995
  • Kugonjetsa Kumwerekera ndi Zinthu Zoledzeretsa
    Galamukani!—1994
  • Omwerekera ndi Juga Kwawo ndi Kuluza Basi
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 5/8 tsamba 18-20

Pamene Zochita Zikhala Zomwerekeretsa

KUMWEREKERA ndi zinthu zoledzeretsa ndi kumwerekera ndi zochita kuli ngati masitima aŵiri olondolana panjanji imodzimodziyo omka kumalo amodzi.a Kulikonse kuli ndi chonulirapo kapena cholinga chimodzimodzicho: kusintha mkhalidwe ndi kuphimba malingaliro opweteka. Tiyeni tilingalire zitsanzo zina za kumwerekera ndi zochita.

Kumwerekera ndi Ntchito

Kumwerekera ndi ntchito kwatchedwa kuti kumwerekera kolemekezeka. Ndi iko komwe, omwerekera ndi ntchito amakhala olembedwa ntchito abwino koposa. Komabe, mumtima mwawo amalingalira kukhala osakhutira. Ntchito ingakhale choiŵalitsa malingaliro opweteka kapena njira yomkitsa yofunira chiyanjo.

Madzi oundana pamwamba pa madzi amatetezera wotsetserekapo kuti asamire m’madzi; zochita zimatetezera womwerekera ndi ntchitoyo kuti asamire m’malingaliro opweteka. Mofanana ndi wotsetsereka pamadzi oundana, womwerekera ndi ntchito akhoza kugwira ntchito mochititsa chidwi. Koma zonsezo ndi zachiphamaso chabe. Kodi nchiyani chimene kaŵirikaŵiri chili chobisika pansi pake? Phungu wina wanthenda zaubongo Linda T. Sanford akulemba kuti: “Pamene womwerekera ndi ntchito ali wosatanganitsidwa kwambiri ndi ntchito, angachulukiridwe ndi malingaliro oipa a kutsenderezeka, nkhaŵa, mkwiyo, kuthedwa nzeru ndi kupanda pake.”

Chisonkhezero chozika mizu cha omwerekera ndi ntchito chimapereka lingaliro lakuti ndiwo mchitidwe umene wakhalapo nthaŵi yaitali, mwinamwake wozika mizu m’maleredwe a munthu. Zimenezi zinali choncho ndi mkazi wina amene tidzamutcha Mary. Kuyambira pausinkhu wa zaka zisanu ndi chimodzi anayesayesa kuti akondedwe ndi atate wake auchidakwa mwa kuwaphikira ndi kuchita ntchito ya m’nyumba. “Kunakhala kwachikoka,” iye akutero. “Ndinalingalira kuti ngati nditachita zambiri kapena ngati nditachita bwino kwambiri, akandikonda. Mmalo mwake ndinangosulizidwa.”

Monga munthu wachikulire Mary akali kulimbanabe ndi kalingaliridwe kolakwa kameneka. “Ndimamvabe mkati mwanga kukhala wopanda pake,” iye akuulula motero. “Ndimalingalirabe kuti ndifunikira kupezabe chikondi, kuti ndili wopanda pake kufikira nditachita kanthu kena. Pomacheza ndimadzitangwanitsa ndi kuphika ndi kutumikira, monga ngati kuti ndikuyesayesa kupeza kuyenera kwanga kwa kukhala pamenepo.”

Kwa awo onga Mary, lingaliro lachikatikati pantchito nlofunika. Baibulo limalimbikitsa za kugwira ntchito zolimba. (Miyambo 6:6-8; 2 Atesalonika 3:10, 12) Yehova Mulungu mwiniyo amachita ntchito zambiri. (Salmo 104:24; Yohane 5:17) Koma sali womwerekera. Yehova anaona ubwino m’ntchito zake zolenga osati pamene zinamalizidwa pokha komanso mkati mwa kulengako.—Genesis 1:4, 12, 18, 21, 25, 31; yerekezerani ndi Mlaliki 5:18.

Mmisiri Wamkulu wa Yehova Mulungu, Mwana wake,Yesu, mofananamo anasonyeza chikhutiro chake m’ntchito yake. (Miyambo 8:30, 31) Yesu analonjeza otsatira ake kuti nawonso akapeza mpumulo mwa kugwira naye ntchito. Onsewo pamodzi anagaŵana m’ntchito yofunika kwambiri. Koma zimenezi sizinawaletse kupuma.—Mateyu 11:28-30; Marko 6:31; yerekezerani ndi Mlaliki 4:6.

Mwinamwake kholo lanu linapereka lingaliro lakuti kufunika kwanu kumadalira pakachitidwe kena ka zinthu kapena kuti simukakondedwa kufikira mutachitapo kanthu kuti mupeze chikondicho. Mudzakhala otonthozedwa kudziŵa kuti limeneli silili lingaliro la Yehova la kulera ana. Mawu ake amalangiza kuti: “Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima [“angalingalire kukhala onyozeka,” The Amplified Bible].” (Akolose 3:21) Yehova simunthu amene amamana chikondi chake kufikira pamene munthu atachitapo kanthu. Chikondi chake sichili kanthu kena kamene amapereka kokha pambuyo pakuti munthu wayamba kumkonda ndi kumtumikira. Ndithudi, Baibulo limatiuza kuti “anayamba iye kutikonda,” inde, ngakhale “pamene tinali chikhalire ofoka,” Mulungu anayamba kutikonda. (1 Yohane 4:19; Aroma 5:6-8) Ndiponso, Yehova samasuliza zoyesayesa zathu zowona mtima za kuchita chifuniro chake. Chifukwa chake, utumiki wathu kwa iye umakhala chisonyezero chathu chowona cha kumkonda kwathu.

Kumwerekera ndi Wailesi Yakanema

Ena amatcha kuonerera kopambanitsa TV kuti kumwerekera. “Mofanana ndi mankhwala oledzeretsa ndi zakumwa zoledzeretsa,” akulemba motero Marie Winn mu The Plug-In Drug, “kuonerera wailesi yakanema kumachititsa woonererayo kutuluka m’dziko lenilenili mwamalingaliro ndi kuloŵa m’mkhalidwe wamaganizo wamphwayi wokondweretsa.”

Ndithudi, palibe cholakwika chilichonse ndi kuiŵala mathayo a moyo—kwakanthaŵi. Koma oonerera ena samabwereranso ku zenizeni. Mwamuna wina wokwatira amene mwadzidzidzi sanathe kuonerera TV pamene inawonongeka anaulula kuti: “Ndikuona kuti maganizo anga anagodomalitsidwa kotheratu zaka zonsezi. Ndinamwerekera pamakina amenewo ndipo sindinakhoze kuchokapo,” Wachichepere wina wotchedwa Kai akufotokoza za kumwerekera kofananako kuti: “Sindimafuna kuonerera wailesi yakanema kwambiri monga momwe ndimachitira koma sindimatha kudziletsa. Iyo imandilamulira kuionerera.”

Kuonerera TV kopambanitsa kumafooketsa mphamvu ya kuganiza. Baibulo limavomereza kusinkhasinkha, kumene kumafuna mlingo wina wa kukhala wekha. (Yoswa 1:8; Salmo 1:2, 3; 145:5; Mateyu 14:23; Luka 4:42; 5:16; 1 Timoteo 4:15) Kumeneku kumachititsa mantha anthu ambiri. Iwo amafikira kukhala achinthenthe pamene ali mumkhalidwe wabata. Amawopa kusinkhasinka ali okha. Amafunafuna mwamphamvu chinthu china chilichonse choti chizadze kupanda kanthuko. TV imakhala mankhwala ake ofulumira. Komabe, ngakhale ingakuchitireni zabwino kwambiri, TV yangokhala choloŵa mmalo chabe cha zochitika zenizeni za moyo.

Kumwerekera ndi Kutchova Juga

Kutchova juga nkozikika mu umbombo. Koma kumwerekera ndi kutchova juga kaŵirikaŵiri kumachitidwa ndi zolinga zambiri kuposa za ndalama chabe.b “Ndinafuna ‘kuchangamuka’ kuti ndibisalire zowona zenizeni za moyo,” akutero Nigel. “Kunali kofafanadi kwambiri ndi kugwiritsira ntchito mwankhwala oledzeretsa.” Kwa wotchova juga womwerekera, kaŵirikaŵiri mchitidwe wa kutchova jugawo mwa iwo wokha umakhala mfupo. Zotulukapo zake nzosakondweretsa. Nigel anatayikiridwa ndi mabwenzi ake. Ena amatayikiridwa ndi mabanja awo. Ambiri amataya thanzi lawo labwino. Ndipo pafupifupi onsewo amataya ndalama zawo. Koma ochepa chabe ndiwo amaleka, popeza kuti kupata kapena kutayikiridwa sindiko nkhaniyo. Kuseŵera maseŵerowo ndiko—maseŵeredwe ake—kumene kumasintha khalidwe ndi kuchititsa mwa munthu kuchangamuka konga kwa mankhwala oledzeretsa.

Kutchova juga kungakhale chophimbira mavuto a moyo, koma sikudzawathetsa. Munthu wovulala kwambiri amafunikira zambiri koposa mankhwala ongoletsa kupweteka. Zilonda zake ziyenera kusamaliridwa. Ngati pali zilonda zimene zachititsa munthu kutchova juga, ayenera kuzidziŵa ndi kuzisamalira. Zimenezi zimafuna kulimba mtima, koma potsirizira pake ndi zofupa.

Wonjokanimo

Kuti muwonjoke m’kumwerekera kulikonse, kuvutika mtima kumene kaŵirikaŵiri kumasonkhezera kumwerekerako sikunganyalanyazidwe. Womwerekerayo ayenera kuyesayesa kuthetsa vutolo kuyambira pachimake. Limeneli lili thayo lalikulu. “Sumangoleka mosavuta kugwiritsira ntchito mankhwala ndi zakumwa zoledzeretsa kwa zaka 30 kumeneko,” akutero wina amene kale anali womwerekera, “makamaka pamene kumwerekera kwako kunali kubisa vuto lina lalikulu kwambiri.”

Komabe, kuwonjoka m’kumwerekera nkoyenerera kuyesayesako. Mary, wantchito womwerekera wotchulidwa payambayo, akufotokoza bwino zimenezi. “Kwa zaka zambiri,” iye akutero, “ndinkapeŵa kuyang’anizana ndi zinthu zimene zinandichititsa mantha. Koma tsopano popeza kuti ndayang’anizana ndi zinthu zimenezo, zimandidabwitsa kuziona mmene zakhalira zazing’ono.”

Zakhala motero kwa ena ambiri amene agonjetsa kumwerekera. Mmalo mwa kupitirizabe monga “akapolo a zizolowezi zowononga,” iwo apempherera “ukulu woposa wamphamvu” kuti ayang’anizane ndi mavuto a kugonjetsa kumwerekerako.—2 Petro 2:19, Today’s English Version; 2 Akorinto 4:7.

[Mawu a M’munsi]

a Pali kukutsutsana kwakukulu ponena za chimene chingatchedwe kumwekera ndi chimene sichingatchedwe kumwerekera. Ena amakonda kutcha kumwerekera ndi zochita kuti “zikoka.” M’nkhani zino tafotokoza mbali ya kumwerekera monga “njira yopulumikira.” Popeza kuti zochita zingagwiritsiridwe ntchito kaamba ka cholinga chimodzimodzicho, munomo tidzazitchulanso kuti “kumwerekera.”

b Mosiyana ndi ntchito ndi kuonerera TV, Akristu amapeŵa kotheratu kutchova juga, m’mitundu yake yonse. (Yerekezerani ndi Yesaya 65:11.) Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka, onani Awake!, June 8, 1992, masamba 3-11.

[Mawu Otsindika patsamba 18]

‘Liwu lakuti kumwerekera likhoza kugwiritsiridwa ntchito pamitundu yonse ya chizoloŵezi chachikoka.’—Dr. J. Patrick Gannon.

[Chithunzi patsamba 19]

Kwa womwerekera ndi ntchito, ntchitoyo imaonekera kukhala yofunika kwambiri kuposa banja

[Chithunzi patsamba 19]

Kutchova juga kungasinthe mkhalidwe wa munthu ndi kuchititsa kuchangamuka konga kwa mankhwala oledzeretsa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena