Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 5/8 tsamba 15-17
  • Kugonjetsa Kumwerekera ndi Zinthu Zoledzeretsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugonjetsa Kumwerekera ndi Zinthu Zoledzeretsa
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoyesayesa Zopitirizabe Nzofunika
  • Kufunafuna Chochititsa
  • Kulimbana ndi Malingaliro Amphamvu
  • Kuthetsa Vuto
  • Kudziŵerengera
  • Pamene Zochita Zikhala Zomwerekeretsa
    Galamukani!—1994
  • Kodi Ndani Amene Amagwidwa Nako, Ndipo Nchifukwa Ninji?
    Galamukani!—1994
  • Ndingatani Makolo Anga Akamaledzera Kapena Kumwa Mankhwala Osokoneza Bongo?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Kupambana m’Nkhondo Yolimbana ndi Uchidakwa
    Nsanja ya Olonda—1993
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 5/8 tsamba 15-17

Kugonjetsa Kumwerekera ndi Zinthu Zoledzeretsa

KULEKA kumwerekera kuli ngati kusamuka m’nyumba imene munaleredweramo. Ngakhale ngati nyumbayo ili yakale ndi yowonongeka, kuisiya nkovuta. Inali nyumba yanu.

Ngati muli womwerekera, mwachionekere kumwerekerako kwakhala nyumba yanu ya malingaliro. Ngakhale kuti mosakayikira iyo yakhala yosalongosoka, iyo njozoloŵereka. “Ndazoloŵera kuledzera. Kusaledzera nkondivuta,” akutero Charles, chidakwa chimene chikuchira. Kuleka kumwerekera kudzakhala kovuta, koma nkoyenerera kukumenyera nkhondo.

Sitepe loyamba ndilo kusiya zinthu zomwerekeretsa.a Musachedwe kapena kulonjeza za kuleka pang’ono ndi pang’ono. Tayani zoledzeretsa zonse ndi zipangizo zake nthaŵi yomweyo. Padzatsatira nyengo yaifupi yakubwevuka, imene panthaŵi zina ingapyoledwe bwino koposa pansi pa kuyang’aniridwa ndi dokotala. Uku ndiko kuyamba kwa kuleka kwa moyo wonse. Koma musaganize kuti kuleka kumeneku nkosatheka. Yambani mwa kuika zonulirapo zimene mungazifikire: kuleka kwa mwezi umodzi, mlungu, kapena tsiku limodzi. Pamapeto a nyengo iliyonse, pangani chitsimikizo chinanso chatsopano popanda kubwereranso ku zoledzeretsazo.

Uku nkuyamba chabe kwa kusintha m’khalidwe la kumwerekera. Baibulo limatifulumiza ‘kudzikonzera tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu.’ (2 Akorinto 7:1) Kumwerekera nkoposa chidetso cha thupi. Mzimu, kapena chikhoterero cha maganizo, chimayambukiridwanso. Kodi nchiyani chimene chingakuthandizeni kuchira, kuthupi ndi mumzimu momwe?

Zoyesayesa Zopitirizabe Nzofunika

“Kumwerekera ndiko kusokonezeka kwa mkhalidwe wonse wa munthu,” akutero Dr. Robert L. DuPont. Chifukwa chake, kugonjetsa kumwerekera kuyenera kuchita ndi umoyo wonse wa munthu. Kuyenera kusintha khalidwe lanu lonse. Zimenezi zimatenga nthaŵi yaitali. Palibe njira yachidule yochirira. Kupereka lonjezo lililonse la kuchira kofulumira kudzangochititsa kubwereranso muvutolo.

Nkhondo ya kuchita chabwino njopitirizabe. Mtumwi Wachikristu Paulo analemba kuti: “Ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, [“m’kulimbana kopitirizabe ndi,” Phillips] lamulo la mtima wanga.” (Aroma 7:23) Iye analembanso kuti Akristu ayenera “kukwaniritsa chiyero.” (2 Akorinto 7:1, NW) Buku lotchedwa Word Pictures in the New Testament likunena kuti liwu lakuti “kukwaniritsa” panopa limapereka lingaliro lakuti, “kupezedwa kwa chiyero chotheratu kosakhala kwa nthaŵi yomweyo, koma mchitidwe wopitirizabe.” Motero kugonjetsa kumwerekera kuyenera kuchitidwa mwapang’onopang’ono.

Kufunafuna Chochititsa

Kwa ambiri, kumwerekera ndiko kuyesayesa kuiŵala zochitika zopweteka zakale. “Vuto la bulimia [vuto la kadyedwe] linandichititsa kuiŵala zakale,” akutero Janis. “Linakhala njira yanga yopulumukira.” Kwa Janis, kunyalanyaza zakale kunangopitiriza kumwerekera kwakeko. Kuzindikira zifukwa za khalidwe lakelo kunathandiza Janis kusintha chizoloŵezi chake cha kumwerekeracho.

Ena amasintha zizoloŵezi zawo zakale ndipo amakhala okhoza kulimbana mwachipambano popanda kupenda zochitika zawo zakale. Ena amapeza kuti malingaliro a kuipidwa ndi mkhalidwe wawo wakale amapitirizabe kusonkhezera chikhumbo cha kumwerekera. Iwo angalingalire mofanana ndi wamasalmo Davide, amene analemba kuti: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga; mundiyese nimudziŵe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nawo mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.”—Salmo 139:23, 24.

Kulimbana ndi Malingaliro Amphamvu

Kodi munayamba mwatulukira mwachindunji m’kuunika kwadzidzidzi kwa dzuŵa kuchokera m’nyumba yamdima? Inu mukhoza kutsinzina chifukwa cha kuŵala kwakukuluko. Mofananamo, pamene muyamba kulimbana ndi kumwerekera, mungapeze kuti mwadzidzidzi ndi mopweteka mukukanthidwa ndi malingaliro amphamvu ambiri osiyanasiyana. Chikondi, mkwiyo, kunyada, nsanje, mantha, kuipidwa, ndi malingaliro ena amphamvu amene akhala ali ophimbidwa kwa nthaŵi yaitali tsopano amaonekera poyera.

Nkhaŵa ingakusonkhezereni kubwereranso ku mdima wozoloŵereka wa kugwiritsira ntchito molakwa zinthu zoledzeretsa. Komatu simufunikira kunyalanyaza malingaliro anuwo. Iwo angakupatseni chidziŵitso chothandiza. Kaŵirikaŵiri malingaliro amphamvu amangokhala chizindikiro chakuti kanthu kena kafunikira chisamaliro. Chotero ngati nkotheka, pendani malingaliro amphamvu anuwo. Kodi akukuuzani chiyani? Ngati uthenga wake uli wosadziŵika bwino kapena ngati malingaliro amphamvuwo akuonekera kukhala olemetsa, akambitsiraneni ndi bwenzi lokhwima m’maganizo. (Yobu 7:11) Simufunikira kulimbana ndi malingaliro anu nokhanokha.—Yerekezerani ndi Miyambo 12:25.

Kumbukirani kuti malingaliro sali kwenikweni adani anu. Yehova Mulungu mwiniyo ali ndi malingaliro amphamvu aakulu, ndipo munthu—wolengedwa m’chifanizo chake—amachita mofananamo. (Genesis 1:26; Salmo 78:21, 40, 41; 1 Yohane 4:8) Mofanana ndi kuŵala kwamwadzidzidzi kwa dzuŵa, choyamba malingaliro amphamvuwo angakhale opweteka. Koma m’kupita kwa nthaŵi adzakhalanso, mofanana ndi kuŵala kwa dzuŵa, magwero a chitsogozo ndi chikondi.

Kuthetsa Vuto

Kuyenda pachingwe nkowopsa kwambiri kwa munthu amene amawopa kukwera pamalo aatali. Kwa munthu womwerekera amene akungoyamba kumene kuchira, moyo ungaonekere kukhala ngati kuyenda pachingwe kowopsa. Mathayo ofuna kusamaliridwa molama maganizo angadzetse mantha a kukwera pamalo aatali, titero kunena kwake. Chiyembekezo cha kulephera chingakuchititseni kulingalira kuti: ‘Inetu ndidzagwa basi. Bwanji ndingogweratu tsopano lino?’

Koma kumbukirani, mavuto samalondola inu monga mdani wanuwanu. Angokhala mikhalidwe imene imafunikira kuiwongolera. Chotero musathedwe nzeru. Limbanani ndi mavuto anu limodzi ndi limodzi. Zimenezi zidzakuthandizani kuwalingalira bwino.—1 Akorinto 10:13.

Kudziŵerengera

Marion, yemwe akuchira pauchidakwa, anafunikira kulimbana ndi lingaliro lake la kusadziŵerengera. “Pansi pamtima,” iye akutero, “nthaŵi zina ndinalingalira kuti ngati akanandidziŵa, [anthu] sakanandikonda.”

Kuwonjoka m’kumwerekera kumafuna kuti muphunzire—mwinamwake kwa nthaŵi yoyamba—kudziŵerengera kwanu monga munthu. Zimenezi nzovuta ngati moyo wanu wadodometsedwa kwambiri ndi kumwerekera. Kodi nchiyani chimene chingathandize?

Baibulo ndilo buku limene limapereka chitonthozo kwa opsinjika mtima. Lingakuthandizeni kukulitsa kudzilemekeza kwabwino. (Salmo 94:19) Mwachitsanzo, wamasalmo Davide analemba kuti anthu anavekedwa korona wa “ulemerero ndi ulemu.” Iye ananenanso kuti: “Chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwiza.” (Salmo 8:5; 139:14) Ndi mawu abwino kwambiri chotani nanga amenewo ochititsa munthu kudziŵerengera!

Ŵerengerani thupi lanu, ndipo mudzalisamalira mumzimu wa lemba ili: “Munthu sanadana nalo thupi lake ndi kale lonse; komatu alilera nalisunga.” (Aefeso 5:29) Inde, inu mukhoza kuyang’anizana ndi zovuta za kuchira pa kumwerekera.b

[Mawu a M’munsi]

a Zowonadi, awo amene ali ndi vuto la kadyedwe sangasale chakudya. Komabe, akhoza kuleka kugwiritsira ntchito chakudya monga chosinthira mzimu wawo. Njira zodyera chakudya mopambanitsa, kudzipha ndi njala, kudzisanzitsa kapena kudzitsegula m’mimba, ndi kuganiza mopambanitsa ponena za chakudya kungaloŵedwe mmalo ndi kadyedwe koyenera.

b Kuti akhalebe mumkhalidwe wa kusiya ndi kupitirizabe kuchira, ena afunafuna programu yobwezeretsa pamkhalidwe wakale. Pali malo ambiri opereka chithandizo, zipatala, ndi malo ena amene amalamulira kulandira maprogramu otero. Galamukani! samavomereza chithandizo chamankwala chamtundu uliwonse. Awo amene akukhumba kukhala mogwirizana ndi malamulo a mkhalidwe a Baibulo adzafuna kukhala osamala kuti asadziloŵetse m’zochitika zimene zikawachititsa kulolera molakwa pamalamulo a mkhalidwe Amalemba.

[Mawu Otsindika patsamba 15]

“Kuchira kumalowetsamo zoposa kungosintha mkhalidwe [wa munthu] wa maganizo kulinga ku chabwino ndi choipa.”—Dr. Robert L. DuPont.

[Chithunzi patsamba 16]

Sitepe loyamba ndilo kuleka kugwiritsira ntchito zinthu zomwerekeretsa

[Chithunzi patsamba 17]

Pamene malingaliro alemetsa mtima wanu, akambitsiraneni ndi wina

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena