Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 8/8 tsamba 16-19
  • Ndine Womwerekera! Kodi Ndingaleke Bwanji Kutchova Juga?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndine Womwerekera! Kodi Ndingaleke Bwanji Kutchova Juga?
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kumwerekera m’Kutchova Juga—Zotulukapo Zake
  • Chifuno cha Kuleka
  • Kufika Paphata la Vutolo
  • “Kanthu Kena Kabwino Kwambiri”
  • Oseŵera Juga Atsopano—Achichepere!
    Galamukani!—1995
  • Kodi Kutchova Njuga Kuli Ndi Vuto Lanji?
    Galamukani!—2002
  • Kodi Kutchova Juga ndi kwa Akristu?
    Galamukani!—1994
  • Omwerekera ndi Juga Kwawo ndi Kuluza Basi
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 8/8 tsamba 16-19

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Ndine Womwerekera! Kodi Ndingaleke Bwanji Kutchova Juga?

“NDINAYAMBA kuseŵera makina otchovera juga a pamene ndinali ndi zaka 13,” anaulula motero David. “Ndinafika pakuti sindinkatha kungopyola malo a juga popanda kuyamba ndaloŵamo ndi kuseŵera makina otchovera juga.” “Ndinafikira ngakhale pakuba ndalama za anzanga, zabanja, ndi anzanga akuntchito kuti ndichilikizire chizoloŵezi changa. Ndinkatchova juga ya mtundu uliwonse,” akuvomereza motero yemwe anali wotchova juga, wotchedwa Thomas.

David ndi Thomas yemwe analeredwa monga Akristu. Onsewo anamwerekera ndi juga—anagwidwa mumsampha wa chikoka chakupha. Akatswiri ofufuza akunena kuti chiŵerengero chochititsa mantha cha achichepere chakhala mikhole ya machitachita onyengerera malingaliro amene amakopa achichepere kuti atchove juga. Magazini a Time akunena kuti: “Akatswiri ofufuza nkhani ya kutchova juga akunena kuti pakati pa omwerekera ndi juga 8 miliyoni mu Amereka, okwanira 1 miliyoni ndiachichepere.” Ena amakhulupirira kuti mu United States, kuyambira pa 4 kufikira pa 6 peresenti ya achichepere onse ali otchova juga omwerekera.

Achichepere amatsatira mipangidwe yambiri yosiyanasiyana yoluluzika imeneyi. Ku Japan, mosasamala kanthu za malamulo okhwima amene amaletsa ana kutchova juga, achichepere “adziŵika chifukwa cha kupezeka kwawo [pabwalo lampikisano] ndi m’nyumba zobetchera, m’chizoloŵezi chovutitsa maganizo chomakulakula,” malinga ndi kunena kwa Mainichi Daily News. Kuchita lotale, kutchova juga ya wopambana pamaseŵera, ndi kutchova juga ya makadi kulinso njira zotchuka pakati pa achichepere zogonjera kuchisonkhezero cha kutchova juga.

Kumwerekera m’Kutchova Juga—Zotulukapo Zake

Gordon Moody, wa Gamblers Anonymous (gulu lothandiza anthu omwerekera ndi juga), akunena kuti: “Choyamba, [kutchova juga] nkokondweretsa, monga ngati kuti watulukira chinthu chatsopano kapena kukonda kanthu kena. . . . Kufunafuna mwaŵi nkokondweretsa ndi kokopa.” (Quit Compulsive Gambling) Inde, kwa anthu ambiri nkokondweretsa kukhala ndi chidwi chofuna kupambana. Komatu munthu sangathe kupambana nthaŵi zonse. Potsirizira pake, wotchova jugayo amalephera. Ndipo ngongole ndi kusoŵa ndalama zimangokhala kuyamba kwa mavuto ake.

Kumwerekera ncholinga cha kungotaya nthaŵi, mofanana ndi kumwerekera kwenikweni, kungawononge mkhalidwe wauzimu, ndi makhalidwe abwino mosaneneka. Kukhoza kuyambitsa mwa inu chimene Gordon Moody akuchitcha “mkhalidwe wonyenga umene . . . potsirizira pake, udzakuikani muukapolo.” Pankhaniyi, timakumbutsidwa za mawu a mtumwi Paulo akuti: “Kodi simudziŵa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye?” (Aroma 6:16) Matembenuzidwe ochitidwa ndi J. B. Phillips amafotokoza vesili motere: “Mumalamulidwa ndi mphamvu imene mumasankha kuimvera.” Tangoyerekezerani, kukhala muukapolo wa chizoloŵezi chimene simungalamulire!

Chifukwa chakuti kaŵirikaŵiri wachichepere amatembenukira pakunama, chinyengo, ndi kuba kuti achilikize chizoloŵezi chake, unansi wa banja lake umawonongekanso. Magazini a ku Britain otchedwa Young People Now akunena kuti: “Pamene ufikira pakuzindikira kuti wakhala mbala, wabodza, ndi vuto, kwa anthu amene umakonda ndi amene amakukonda, kudzilemekeza kwako kumatsika.” Mosadabwitsa, The Harvard Mental Health Letter ikusimba kuti otchova juga omwerekera amakhala pangozi ya “kupsinjika maganizo kwakukulu, nkhaŵa,” ndi zovuta zina zambiri zakuthupi, monga ngati “kubindikira m’mimba, kusoŵa tulo, kupweteka kwa mutu, kuthamangitsa kwa mwazi, mphumu, kupweteka kwa msana, kupweteka kwa pachifuwa.”

Komabe, chotulukapo choipitsitsa koposa zonse ndicho kuwonongeka kwa mkhalidwe wauzimu wa munthu. Baibulo limatsutsa kusirira ndi kukondetsa ndalama. (1 Akorinto 5:10, 11; 1 Timoteo 6:10) Mofanana ndi kumwerekera kwina kulikonse, kumwerekera m’juga ndiko “chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu.” (2 Akorinto 7:1) Pamene mutchova juga mowonjezereka, ndipamenenso mumawononga chikumbumtima chanu ndi unansi wanu ndi Mulungu.—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 4:2.

Chifuno cha Kuleka

Kodi mungawonjoke bwanji m’chizoloŵezi chonga msampha chimenechi? Choyamba, muyenera kufunadi kuleka chizoloŵezi chimenechi. “Palibe kumwerekera kulikonse kumene kungagonjetsedwe kusiyapo ngati womwerekerayo akufunadi kusintha,” akutero Liz Hodgkinson m’buku lake lakuti Addictions. Zimenezi zikutanthauza kuphunzira ‘kuda choipa,’ kunyansidwa ndi kutchova juga. (Salmo 97:10) Motani? Mwa kuganizira, osati zosangalatsa zake, koma zotulukapo zake. Kodi ‘kukhala nazo zokondweretsa za zoipa zakanthaŵi’—chisangalalo cha kupambana maseŵera ena—nkoyenerera kutayikiridwa ndi moyo wosatha? (Ahebri 11:25) Kuganiza mwanjira yotero kungakuthandizeni kukulitsa chitsimikiziro cha kuleka.

Komabe, wofufuzayo Liz Hodgkinson akunena kuti: “Mtundu uliwonse wa kumwerekera ukhoza kukhala wozika mizu mwa munthu kwakuti kuuchotsamo kumangofanana ndi kudula chiŵalo.” Koma Yesu anati: “Ngati diso lako lamanja likulakwitsa iwe, ulikolowole, nulitaye; pakuti nkwabwino kwa iwe, kuti chimodzi cha ziŵalo zako chiwonongeke, losaponyedwa thupi lako lonse m’gehena.” (Mateyu 5:29) Kanthu kalikonse koika paupandu unansi wanu ndi Mulungu kayenera kuchotsedwa m’moyo wanu!

Zimenezi zimatanthauza kukulitsa kudziletsa. Mtumwi Paulo anali ndi zikhumbo zoipa zofika mumtima kaŵirikaŵiri zimene zikanamgonjetsa, koma anakana kukhala kapolo wa zikhumbo zake. Iye anati, “Ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo.” (1 Akorinto 9:27) Nanunso muyenera kudziumira mtima, osalola zikhumbo zanu kukulamulirani.

Kufika Paphata la Vutolo

Komabe, kuti munthu apambane nkhondoyi, kudzafunikira zoposa kufuna chabe. Kaŵirikaŵiri kumwerekera kumasonyezanso mavuto ena aakulu. Womwerekera m’juga wina wotchedwa Dick akuti: “Ubwana wanga unali wosazolowereka. Sindinali kukondedwa konse ndi a m’banja langa. . . . Ndinkachita manyazi nthaŵi zonse. Ndinkadziona kukhala wosanunkha kanthu.” Monga chotulukapo cha kupsinjika maganizo kotero, analoŵa m’kutchova juga.

Anthu ambiri othandiza odwala maganizo tsopano amagwirizanitsa kumwerekera kosiyanasiyana ndi malingaliro a kuvutika ndi nkhanza zapaubwana ndi kunyalanyazidwa. Mulimonse mmene zingakhalire, kufika paphata pavuto lanu kungakuthandizeni kugonjetsa vutolo. Wamasalmo anapemphera kuti: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziŵe mtima wanga; mundiyese nimudziŵe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nawo mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.” (Salmo 139:23, 24) Kukambitsirana zolingalira zanu ndi Mkristu wachikulire mwauzimu, mwinamwake mkulu wa mumpingo, kungachite zambiri kukuthandizani kuzindikira chifukwa chake mumatchova juga ndi zimene muyenera kuchita kuti musinthe kaganizidwe kanu ndi njira za chizoloŵezi chanucho.a

“Kanthu Kena Kabwino Kwambiri”

Malinga nkunena kwa buku lakuti Quit Compulsive Gambling, kuleka “kwangokhala [njira] yoyamba polimbana ndi vutolo.” Masinthidwe aakulu m’moyo wanu adzafunikira kupangidwanso. Kuti musabwererenso kumkhalidwewo, muyenera kupeŵa mabwenzi akale otchova nawo juga ndi kupeŵa kufika kumalo otchovera juga, monga ngati kumalo a casino, maholo obetcheramo, ndi zina zotero. (Miyambo 13:20) Zimenezi sizikutanthauza kuti mudzipatule. (Miyambo 18:1) Yesayesani kukulitsa ubwenzi wamphamvu mkati mwa mpingo Wachikristu. Dzitanganitseni ndi ntchito yopindulitsa, ntchito zauzimu, ndi kusanguluka kwabwino.

Komabe, Hodgkinson akutikumbutsa kuti, munthu womwerekerayo adzapambana nkhondo yake kokha pamene afikira “pakuzindikira kuti pali kanthu kena kabwino kwambiri—kuti moyo uli nzambiri koposa kuyesayesa kukhutira ndi kumwerekerako.” Eya, kodi nchiyani chimene chingakhale chabwino kwambiri kuposa chiyembekezo chimene Baibulo limapereka?

Mwamuna wina wotchedwa Roddy anapeza zimenezi kukhala zowona. Iyeyu akudzifotokoza kuti anali “wotchova juga womwerekera kotheratu” kwa zaka 25, kuyambira pamene anali wachichepere. Roddy anayesa mtundu wa juga uliwonse—kubetchera mpikisano wa akavalo, agalu, mpira, ndi kubetcha m’nyumba za casino. Komano anayamba kugwiritsira ntchito chowonadi cha m’Mawu a Mulungu chimene anaphunzira kwa Mboni za Yehova. “M’miyezi itatu yokha,” akutero Roddy, “ndinapanga kusintha kwakukulu.” Analeka kutchova juga, ndipo lerolino akutumikira monga mkulu mumpingo Wachikristu.

Komabe, mwinamwake inu muli kale ndi chidziŵitso cha ziphunzitso za Baibulo. Mofanana ndi David ndi Thomas, otchulidwa poyambapo, kufikira pano mungakhale mutalephera kupanga chowonadi cha Baibulo kukhala chanu. Ngati ndichoncho, bwanji osayesa ‘kuzindikira chimene chili chifuno cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa’ mwa kuphunzira Baibulo mwakhama? (Aroma 12:2) Pamene David ndi Thomas anayamba kugwiritsira ntchito zimene anaphunzira ndi kukulitsa chikhulupiriro chenicheni ndi chikhutiro, anali okhoza kugonjetsa kumwerekera m’juga. Nanunso mukhoza!

Kugwiritsira ntchito kwanu zimene Baibulo limaphunzitsa kudzachititsa chiyembekezo cha m’Baibulo cha mtsogolo—kanthu kena kabwino kwambiri kuposa juga—kukhala chenicheni kwa inu. Panthaŵi imodzimodziyo, kudzakuthandizani kukulitsa unansi wanu ndi Mulungu. Motero mudzadziona kukhala womasuka ‘kupemphera mosalekeza’ kwa iye kaamba ka chithandizo, muli ndi chidaliro chakuti amadziŵa malingaliro anu. (1 Atesalonika 5:17; Salmo 103:14) Adzafupa zoyesayesa zanu zakhamazo mwa kukupatsani nyonga yofunika kupambana nkhondo ya kuleka kumwerekera m’kutchova juga.—Agalatiya 6:9; Afilipi 4:13.

[Mawu a M’munsi]

a Anthu ochuluka amene amathandiza odwala nthenda zamaganizo amakhulupirira kuti kulangizidwa ndi akatswiri nkofunika kotero kuti muwonjoke m’chizoloŵezi cha kumwerekeracho. Ngati Mkristu asankha njira yochiritsira imene simaombana ndi malamulo a mkhalidwe a Baibulo, imeneyi ndinkhani ya munthu mwini.

[Chithunzi patsamba 16]

Kaŵirikaŵiri otchova juga amatembenukira pakunama ndi kuba kuti achilikize chizoloŵezi chawo cha kutchova juga

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena