Pamene Ubwana Ukhala Tsoka
NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! MU SPAIN
Lerolino—patsiku limodzi lenileni m’ma 1990—ana zikwi 200 adzamenya nkhondo yachiŵeniŵeni, ana amsinkhu wopita kusukulu mamiliyoni 100 sadzapita kusukulu, ana mamiliyoni 150 adzagona ndi njala, ana mamiliyoni 30 adzagona m’makwalala, ndipo ana zikwi 40 adzafa.
NGATI ziŵerengero zapamwambazi zikuonekera kukhala zowopsa, nkhope za oŵerengedwawo zimaswetsa mtima. Pansipa pali nkhani zachidule za ana asanu amene mavuto awo othetsa nzeru amatithandiza kuzindikira tanthauzo la ziŵerengero zomvetsa chisoni zimenezi.
Mwana wachisilikali. Mohammad ali ndi zaka 13 chabe, koma ali kale msilikali wokhwima kummwera koma chakummaŵa kwa Asia, wamenya nkhondo zisanu ndi ziŵiri. Iye anali kuŵeta mbuzi asanapite kunkhondo—ali wazaka khumi. Tsopano, Mohammad amagwiritsira ntchito mfuti yosakaza yotchedwa AK-47, imene samazengereza kuigwiritsira ntchito. M’kulimbana kwina iye anapha asilikali achidani aŵiri mwa kuwawombera mfuti ali pafupi naye kwambiri. Pamene anafunsidwa mmene anamverera powapha, iye anati: “Ndinakondwera chifukwa ndinawapha.” Ana amakhala asilikali abwinopo, ofesala wake akutero, “chifukwa sachita mantha.”
Mwana wantchito. Woodcaby wa zaka zinayi amakhala m’nyumba ya zidutswa za matabwa pa chisumbu cha Caribbean. Iye amadzuka 6:00 a.m. kuti agwire ntchito zake zapanyumba za masiku onse: kuphika, kutunga madzi, ndi kusesa m’nyumba ya mbuye wake. Samapatsidwa malipiro aliwonse ndipo mwinamwake sadzapita konse kusukulu. Woodcaby amanena kuti amalakalaka makolo ake, koma sadziŵa kumene ali. Tsiku lake limatha 9:30 p.m., ndipo ngati wachita mwaŵi, samagona ndi njala.
Mwana wanjala. M’mudzi wa mu Afirika wa Comosawha, mtsikana wa zaka 11 zakubadwa amatha tsiku lonse akufukula zomera. Zipatso zobulungika monga anyezi zimenezo—zomera zokhazo m’nthaka youma imeneyo—zikupulumutsa moyo wake ndi wa banja lake. Zipatsozo amaziphika kapena kuzikanda ndiyeno nkuzikazinga. Tsoka lophatikiza chilala ndi nkhondo yachiŵeniŵeni ladzetsa njala yowopsa kwa apamudzipo.
Mwana wa m’khwalala. Edison ali mmodzi wa zikwi zambiri za ana a m’khwalala mu mzinda wina waukulu wa ku South America. Iye amapeza ndalama pang’ono mwa kupukuta nsapato, ndipo amagona pachiunda chakonkili pafupi ndi siteshoni ya basi, pamodzi ndi ana ena amene amatsamirana m’nthaŵi yausiku yozizira. Nthaŵi zina iye amaba zinthu kuti awonjezere ndalama zimene amapeza monga wopukuta nsapato. Wamenyedwa kaŵiri ndi apolisi, ndipo wakhalapo miyezi itatu m’ndende. Edison akutsimikiza kuti tsopano “walekeratu” mankhwala oledzeretsa ndi kusuta glu. Amakhumbira kukhala makanika, amakhumbira kuphunzira ntchito.
Imfa ya mwana. Uli mmaŵa wa mame ndi wozizira, pa phiri la Dugen ku Middle East. Mwana, wokulungidwa m’nsalu yakumanda, waikidwa m’manda aafupi. Khandalo linamwalira ndi nthenda ya kupaza—imene imapha ana kwambiri. Amayi ake anathaŵa nkhondo kwawo ndipo mkaka wawo unauma mkati mwa ulendo wotopetsa wothaŵira kumalo achisungiko. Posoŵa chochita iye anadyetsa mwana wakeyo shuga ndi madzi, koma madziwo anali amatenda, ndipo khandalo linamwalira. Mofanana ndi ana ena okwanira 25,000 omwe anaikidwa m’manda tsiku limodzimodzilo, iye sanathe ndi chaka chomwe.
Kwa nthaŵi zikwi zambiri, nkhani zamatsoka zimenezi zimasonyeza mmene moyo ulili kwa ana ambiri padziko. Ubwana, nthaŵi yophunzira ndi kukulira m’nyumba ya banja lachikondi, wakhala tsoka kwa ana ameneŵa limene kwa ochuluka silidzatha konse.
Peter Adamson, mkonzi wa lipoti lakuti The State of the World’s Children, analengeza mu 1990 kuti: “Imfa ndi kuvutika pamlingo umenewu sizilinso zofunikira; motero sizili zololekanso. Munthu ayenera kusunga makhalidwe abwino chifukwa chakuti ali wokhoza kutero.”
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Photo: Godo-Foto