Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 8/8 tsamba 31
  • Mabomba Otchera Pansi—Chiwopsezo cha Dziko Lonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mabomba Otchera Pansi—Chiwopsezo cha Dziko Lonse
  • Galamukani!—1994
  • Nkhani Yofanana
  • Kupenda Mavuto Odza ndi Mabomba Okwirira
    Galamukani!—2000
  • Pang’onong’ono N’kanafa
    Galamukani!—2000
  • Mmene Nkhondo Zimasakazira Ana
    Galamukani!—1997
  • Mantha—Ofala Tsopano Koma Osati Kwamuyaya!
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 8/8 tsamba 31

Mabomba Otchera Pansi—Chiwopsezo cha Dziko Lonse

ZIKWI zopanda liwongo za amuna, akazi, ndi ana m’maiko oposa 60 akulemazidwa, ndipo ena akuphedwa, mwezi ndi mwezi, ndi mabomba otchera pansi. Kukuyerekezeredwa kuti mabomba olinganiziridwa kuvulaza anthu apha kapena kuvulaza anthu ambiri kuposa nkhondo za makemikolo, za tizirombo toyambitsa matenda, ndi za nyukliya. Malinga ndi kunena kwa bungwe lofufuza la Human Rights Watch, anthu pafupifupi 30,000 alemazidwa ndi mabomba otchera pansi mu Cambodia mokha.

Mabomba aang’ono amenewa akwiriridwa pansi panthaŵi za nkhondo zosiyanasiyana, ndipo ambiri a iwo sanachotsedwe. Kukuyerekezeredwa kuti pafupifupi mamiliyoni 100 a iwo adakali okwiriridwa m’maiko oposa 60. Iwo angaphulitsidwe mwakungopondapo ndipo amagwiritsiridwa ntchito kwambiri mu nkhondo chifukwa n’ngosakwera mtengo komabe ali ovulaza kwambiri. Mtundu umodzi umagulidwa ndi $3 chabe. Wina, umene umabalalitsa machaka 700 ndi kupha pa mtunda wa mamita 40 mbali zonse, umagulidwa ndi $27 chabe. Akufunidwa ndi ochuluka kwambiri, The New York Times ikuchitira lipoti, kwakuti maiko 48 tsopano amapanga ndi kugulitsa mitundu yosiyanasiyana 340 ya iwo. Ndipo ambiri akukwiriridwa pansi tsiku ndi tsiku kuposa amene amafumulidwa ndi antchito zochotsa mabomba otchera pansi.

Kuchotsa mabomba otchera pansi kuli kovuta ndiponso kowonongetsa ndalama, popeza kuti magulu ankhondo ambiri samaika chizindikiro pamalo amene mabomba otchera akwiriridwa; ndipo mowonjezerekawonjezereka mabomba akupangidwa ndi mtengo, mapulasitiki, ndi zopangira zina zimene sizimazindikiridwa ndi ziwiya zofufuzira chitsulo. Chiwalo cha bungwe lopanga malamulo la United States Patrick Leahy, amene anaika chiletso cha kutumiza zidazi ku maiko ena, anati: “Mu Netherlands, anthu akumaphedwabe ndi mabomba otchera pansi a German a mu Nkhondo Yadziko II. Taganizirani mmene kulili koipirapo mu Afghanistan, Cambodia, Angola, Bosnia ndi maiko ena onse amene ali ndi mabomba otchera ambirimbiri m’nthaka.”

Ndi dziko latsopano la Mulungu likudzalo lokha limene lidzathetsa mavuto a mtundu umenewo. Mawu ake amalonjeza kuti: “[Mulungu] aletsa nkhondo kumalekezero a dziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magaleta [ankhondo] ndi moto.”—Salmo 46:9.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena