Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w95 10/15 tsamba 5-8
  • Mantha—Ofala Tsopano Koma Osati Kwamuyaya!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mantha—Ofala Tsopano Koma Osati Kwamuyaya!
  • Nsanja ya Olonda—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifukwa Chomveka Chowopera Nkhondo
  • Kuwononga Dziko Lapansi ndi Zamoyo Zake Kowonjezereka
  • Kodi Zidzaipiraipirabe Kapena Zidzakhala Bwino?
  • Kupenda Mavuto Odza ndi Mabomba Okwirira
    Galamukani!—2000
  • Mabomba Otchera Pansi—Chiwopsezo cha Dziko Lonse
    Galamukani!—1994
  • Pang’onong’ono N’kanafa
    Galamukani!—2000
  • Mmene Nkhondo Zimasakazira Ana
    Galamukani!—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1995
w95 10/15 tsamba 5-8

Mantha​—Ofala Tsopano Koma Osati Kwamuyaya!

OPHUNZIRA a Mawu a Mulungu sakudabwa kuona kuti mantha ali ofala kwambiri. Monga mmene Mboni za Yehova zafalitsira ponseponse mu utumiki wawo, pali umboni wochuluka wakuti tikukhala m’nthaŵi yapadera m’mbiri ya anthu. Mukudziŵa kuti pali mantha ofala. Koma kalekale Yesu anazindikiritsa, kapena anasonya ku, nthaŵi yathu. Iye anali kuyankha mafunso a atumwi ake ponena za kukhalapo kwake ndi chimaliziro cha dongosolo la zinthu, kapena ‘mapeto a dziko.’​—Mateyu 24:3.

Nazi zina za zimene Yesu ananeneratu:

“Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina: ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m’malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zowopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba.”​—Luka 21:10, 11.

Kodi mwamvetsera ndemanga yake ponena za “zowopsa”? Pambuyo pake mu yankho limodzimodzilo, Yesu ananenanso ndemanga ina yapadera ponena za mantha imene imakhudza kwambiri inuyo ndi okondedwa anu mwachindunji. Koma tisanafike kumeneko, tiyeni tipende mwachidule maumboni ena owonjezerapo akuti tikukhala m’masiku otsiriza.​—2 Timoteo 3:1.

Chifukwa Chomveka Chowopera Nkhondo

Nkhondo zasiya mbali zambiri za dziko lapansi zili zowonongedwa. Mwachitsanzo, magazini a Geo anati migodi ya mafuta imene inasiyidwa ikuyaka pambuyo pa nkhondo ya ku Middle East yaposachedwapa ndiyo “kuwononga malo kwakukulu koposa kochitidwa ndi dzanja la munthu.” Nkhondo zapha kapena kulemaza anthu mamiliyoni makumi. Pambali pa mamiliyoni a imfa za asilikali ndi anthu wamba mu Nkhondo Yadziko I, mamiliyoni 55 anaphedwa mu Nkhondo Yadziko II. Kumbukirani kuti monga mbali ya chizindikiro chakuti mapeto a dziko ali pafupi, Yesu ananena kuti “mtundu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina.”

Sitingasiyenso kuyesayesa kwa munthu kupululutsa mitundu​—kuwononga fuko lonse kapena mtundu. Imfa za mamiliyoni a Aarmeniya, Akambodiya, Ayuda, Arwanda, Aukraniya, ndi ena zawonjezera liwongo la mwazi la anthu mkati mwa zaka za zana la 20. Kuphana kumeneku kukupitirizabe kumaiko kumene udani wautundu umalimbikitsidwa ndi anthu oyaluka ndi chipembedzo. Inde, nkhondo zikunyowetsabe dziko lapansi ndi mwazi wa anthu.

Nkhondo zamakono zimalemaza kapena kupha anthu ambiri ngakhale pambuyo pa kumenyanako. Mwachitsanzo, talingalirani za kutchera mabomba pansi kosasankha. Malinga ndi lipoti la gulu lofufuza la Human Rights Watch, “mabomba otchera pansi pafupifupi 100 miliyoni kuzungulira dziko lonse lapansi aika anthu wamba pangozi.” Mabomba otereŵa akupitirizabe kukhala angozi kwa amuna, akazi, ndi ana opanda mlandu nthaŵi yaitali pambuyo pa nkhondo imene anagwiritsiridwamo ntchito. Kwanenedwa kuti mwezi uliwonse anthu zikwi zambiri amalemazidwa kapena kuphedwa ndi mabomba otchera pansi m’maiko oposa 60. Kodi nchifukwa ninji chinthu choika moyo ndi ziŵalo pachiswe chimenechi sichikuchotsedwapo kotheratu? The New York Times inati: “Mabomba ambiri amatcheredwa tsiku lililonse kuposa amene amachotsedwa pantchito yochotsa mabomba otchera, motero chiŵerengero cha anthu ovulazidwa ndi ophedwa chikukwera.”

Nkhani imeneyo ya mu nyuzipepala ya mu 1993 inanena kuti kugulitsa mabomba ameneŵa kwakhala malonda amene “amapanga $200 miliyoni pachaka.” Amaloŵetsamo “makampani ndi magulu oimira boma pafupifupi 100 m’maiko 48” amene “akhala akugulitsa kunja mitundu yosiyanasiyana 340” ya mabomba. Mwauchiŵanda, mabomba ena apangidwa moti amaoneka ngati zoseŵeretsa kuti azikopa ana! Tangolingalirani, kupangira ana zimenezo mwadala kuti alemale ndi kuwonongedwa! Nkhani ina ya mutu wakuti “Mabomba 100 Miliyoni” inanena kuti mabomba otchera “apha kapena kulemaza anthu ambiri kuposa nkhondo zogwiritsira ntchito mpweya wakupha, nkhondo zogwiritsira ntchito tizilombo topatsa matenda ndi nkhondo za nyukiliya.”

Koma mabomba otchera pansi sindiwo katundu waimfa wokha wogulitsidwa m’malonda a padziko. Ochita malonda a zida zankhondo aumbombo akuchita malonda opezetsa chuma cha dzaoneni pa dziko lonse lapansi. The Defense Monitor, yofalitsidwa ndi Centre for Defense Information, ikunena kuti: “Mkati mwa zaka khumi zapitazo [dziko lina lomveka] linagulitsa kunja zida zofika pa $135 Biliyoni.” Dziko lamphamvu limenelinso “linaloleza kugulitsa zida zankhondo, milimo ya zankhondo, ndi maphunziro a zankhondo kwa maiko 142 zofika pa $63 Biliyoni.” Motero mbewu zikubzalidwa za nkhondo ndi kuvutika kwa anthu kwa mtsogolo. Malinga ndi The Defense Monitor, mu “1990 mokha, nkhondo zinachititsa anthu 5 miliyoni kuphunzira kugwiritsira ntchito zida mu nkhondo, mtengo wake unapyola pa $50 Biliyoni ndipo zinapha anthu [250,000], ambiri a iwo anthu wamba.” Mukhoza kuganiza za nkhondo zambiri zimene zaulika kuyambira chakacho, zikumachititsa mantha ndi imfa kwa mamiliyoni owonjezereka!

Kuwononga Dziko Lapansi ndi Zamoyo Zake Kowonjezereka

Profesa Barry Commoner akuchenjeza kuti: “Ndikhulupirira kuti kuipitsa dziko kopitirizabe, ngati sikuletsedwa, m’kupita kwa nthaŵi kudzawononga kuyenera kwa dziko lapansi monga malo a moyo wamunthu.” Iye akupitiriza kunena kuti vuto si umbuli ayi koma umbombo wadala. Kodi muganiza kuti Mulungu wathu wachilungamo ndi wachikondi adzalekerera mkhalidwewu kwamuyaya, akumatisiya m’mantha owonjezereka a kuipitsa? Kuwonongedwa kwa dziko lapansi kukufuna kuŵerengera mlandu wa oliwonongawo ndiyeno Mulungu kukonzanso dziko. Iyi ndi mbali ya zimene Yesu ananena mu yankho lake kwa atumwi ponena za ‘mapeto a dziko.’

Tisanakambitsirane za mmene Mulungu adzachitira kuŵerengera mlanduko, tiyeni tipange kusanthula kwina kwa mbiri ya munthu. Ngakhale zinthu zochepa zowononga zimene munthu wachita nzochititsa chisoni: mvula ya asidi ndi kudula mitengo kwaumbombo kumene kukuwononga nkhalango zathunthu; kutaya mosasamala zinyalala za nyukiliya, makemikolo a poizoni, ndi ndoŵe zaziŵisi za munthu; kufoketsa muyalo wotetezera wa ozoni; ndi kugwiritsira ntchito mosasamala mankhwala ophera zomera ndi ophera tizilombo.

Kufuna phindu m’ntchito zamalonda kukuipitsa dziko lapansi m’njira zina. Miyulumiyulu ya zinyalala zikuponyedwa m’mitsinje, m’nyanja, m’mphepo, ndi panthaka tsiku ndi tsiku. Asayansi akudetsa mlengalenga ndi zinyalala za mumlengalenga, osazitola pochoka, titero kunena kwake. Dziko lapansi mofulumira likukhala lozingidwa ndi zinyalala zomalizungulira mumlengalenga. Pakanapanda njira za chilengedwe zopangidwa ndi Mulungu kuti dziko lizidzikonza, mudzi wathu wa dziko lapansili sukanachirikiza moyo, ndipo munthu mwachionekere akanapuya kalekale ndi zinyalala zake.

Munthu amadziipsa ngakhale iyemwini. Mwachitsanzo, talingalirani za fodya ndi anamgoneka ena. Ku United States, kugwiritsira ntchito zinthu zotere kwatchedwa “vuto laumoyo loyambirira la mtunduwo.” Kumawonongetsa dzikolo ndalama $238,000,000,000 pa chaka, mwa zimene $34,000,000,000 amaziwonongera pa “kusamalira thanzi kosafunika.” Kodi muganiza kuti fodya amawononga ndalama ndi miyoyo ingati kumene mumakhala?

Makhalidwe olekerera ndi aupandu, amene ambiri amaumirira kuti ngoyenera kuwachita, abala matenda a kupha owopsa opatsirana mwa kugonana, akumachititsa ambiri kufa asanakalambe. Kwaonedwa kuti madanga olembapo za akufa okondedwa m’manyuzipepala a m’mizinda yaikulu akusonyeza chiŵerengero chomawonjezereka cha omwalira m’zaka zawo za m’ma 30 ndi 40. Chifukwa ninji? Kaŵirikaŵiri nchifukwa chakuti amatuta zotulukapo za makhalidwe awo oipa. Kuwonjezereka kowopsa kotere kwa matenda opatsirana mwa kugonana ndi matenda ena kumagwirizananso ndi ulosi wa Yesu, pakuti ananena kuti kudzakhala “miliri m’malo akutiakuti.”

Komabe, kuipitsa kwakukulu kumene kwakhalapo ndi kwa maganizo ndi mzimu, kapena khalidwe la munthu. Mutapenda mitundu yonse ya kuipitsa imene tatchula podzafika pano, kodi si zoona kuti kwambiri kwachitika chifukwa cha maganizo oipitsidwa? Taganizirani za kuwononga kumene anthu a maganizo opotoka amachita monga mbanda, kugwirira chigololo, kulanda, ndi ziwawa zina zochitidwa ndi munthu kwa munthu mnzake. Ambiri amadziŵanso kuti kutaya mimba mamiliyoni kochitidwa pachaka kuli chizindikiro cha kuipitsidwa kwa maganizo ndi kwauzimu.

Timaona zambiri m’makhalidwe a achinyamata. Kusalemekeza ulamuliro wa makolo ndi wa ena kumathandizira kusweka kwa mabanja ndi kuphwanya malamulo. Kupanda mantha abwino a ulamuliro kumeneku kuli chifukwa cha kupanda malingaliro auzimu kwa achichepere. Motero, awo amene amaphunzitsa chisinthiko, kukana Mulungu, ndi maphunziro ena owononga chikhulupiriro ali ndi liwongo lalikulu. Amene alinso ndi liwongo ndi aphunzitsi achipembedzo amene, pofuna kuyesedwa amakono ndi “olondola,” afulatira Mawu a Mulungu. Iwo ndi ena otengeka ndi nzeru ya dzikoli amaphunzitsa mafilosofi otsutsa a anthu.

Zotulukapo zake masiku ano nzosakayikitsa. Anthu samasonkhezeredwa ndi chikondi cha Mulungu kapena cha mnansi, koma ndi dyera ndi udani. Chipatso chake choipa ndicho kufalikira kwa makhalidwe oipa, chiwawa, ndi kupanda chiyembekezo. Momvetsa chisoni, izi zimachititsa mantha anthu oona mtima, kuphatikizapo mantha akuti munthu adzadziwononga iyemwini ndi pulanetili.

Kodi Zidzaipiraipirabe Kapena Zidzakhala Bwino?

Ponena za mantha, kodi patsogolopa padzakhala zotani? Kodi mantha adzapitirizabe kumawonjezereka, kapena kodi adzagonjetsedwa? Tiyeninso tione zimene Yesu anauza atumwi ake.

Iye analoza ku chinachake chimene chili patsogolopa​—chitsautso chachikulu. Nazi zimene ananena: “Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuŵa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuŵala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka: ndipo pomwepo padzaoneka m’thambo chizindikiro cha Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pachifuŵa, nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.”​—Mateyu 24:29, 30.

Motero tingayembekeze kuti chitsautso chachikulu chidzayamba posachedwapa. Maulosi ena a Baibulo amasonyeza kuti mbali yake yoyamba idzakhala kubwezera chilango pa chipembedzo chonyenga kuzungulira dziko lonse. Ndiyeno zochitika zowopsa zimene zangotchulidwa zidzatsatira, kuphatikizapo zodabwitsa zinazake zakumwamba. Kodi mamiliyoni a anthu adzatani?

Chabwino, talingalirani za cholembedwa chofanana cha yankho la Yesu, pamene timapeza ndemanga zaulosi zowonjezereka:

“Kudzakhala zizindikiro pa dzuŵa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi pa dziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkukumo wake wa nyanja ndi mafunde ake; anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza ku dziko lapansi; pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.”​—Luka 21:25-27.

Zimenezo zili mtsogolo mwathu. Koma si anthu onse amene adzakhala m’mantha okomoka nawo. Mosiyana ndi zimenezo, Yesu anati: “Poyamba kuchitika izi, weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiomboledwe chanu chayandikira.”​—Luka 21:28.

Ananena mawu amenewo olimbikitsa kwa atsatiri ake oona. M’malo mwa kukomoka kapena kuziziritsidwa m’nkhongono ndi mantha, iwo adzakhala ndi chifukwa cha kuŵeramutsa mitu yawo mopanda mantha, ngakhale kuti akudziŵa kuti chisautso chachikulu chili pafupi kufika pachimake. Chifukwa ninji adzakhala opanda mantha?

Chifukwa Baibulo limanena momvekera bwino kuti padzakhala opulumuka “chisautso chachikulu” chonse chimenechi. (Chivumbulutso 7:14) Cholembedwa chimene chikulonjeza zimenezi chimanena kuti ngati tidzakhala pakati pa opulumuka, tidzasangalala ndi madalitso osayerekezeka ochokera m’dzanja la Mulungu. Chimamaliza ndi chitsimikiziro chakuti Yesu “adzawaŵeta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi a moyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pawo.”​—Chivumbulutso 7:16, 17.

Awo​—ndipo ife tingaphatikizidwepo​—amene adzasangalala ndi madalitso sadzakhala ndi mantha amene akugwira anthu lerolino. Komabe, zimenezo sizimatanthauza kuti iwo adzakhala alibiretu mantha, pakuti Baibulo limasonyeza kuti pali mantha ena abwino. Nkhani yotsatira idzafotokoza chimene mantha ameneŵa ali ndi mmene ayenera kutikhudzira.

[Chithunzi patsamba 8]

Alambiri a Yehova mokondwa amayembekeza dziko latsopano loyandikalo

[Mawu a Chithunzi patsamba 7]

Kuipitsa: Chithunzi: Godo-Foto; roketi: Chithunzi cha U.S. Army; mitengo kupsa: Richard Bierregaard, Smithsonian Institution

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena