Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 12/8 tsamba 28-29
  • Pamene Chithandizo Chowonjezereka Chimafunika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Chithandizo Chowonjezereka Chimafunika
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mtsogolo
  • Kugonjetsa Vutolo
    Galamukani!—1997
  • Kulera Mwana Wovuta Monga Kholo
    Galamukani!—1994
  • “Khazikika Numvetsere!”
    Galamukani!—1997
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 12/8 tsamba 28-29

Pamene Chithandizo Chowonjezereka Chimafunika

NGAKHALE kuti malingaliro ambiri operekedwa m’nkhani zapitazo angakhale othandiza kwambiri, nthaŵi zina chithandizo chowonjezereka chimafunika m’mikhalidwe ina. Mwachitsanzo, kufufuza zochitika kwaphatikizapo malipoti a ana amene sali chabe onyanyuka komanso owopsa kwambiri. Ana ameneŵa, ngakhale kuti amaleredwa ndi mabanja achikondi, amasonyeza khalidwe lawo lowononga mwa kuphwanya zinthu, kuzazira anthu, kukoleza moto, kuwombera mfuti, kubaya ndi mpeni (ngati wapezeka), ndi kuvulaza zinyama, anthu ena kapena iwo eni, atangoganiza kuchita zimenezo. Amasonyeza mkhalidwe wa chipwirikiti weniweni.

Kaya afunikira kapena safunikira kupeza chithandizo cha mankhwala kuti alere bwino lomwe mwana wawo, ili nkhani ya chosankha chaumwini. Banja lililonse liyenera kusankha mmene lingakwaniritsire zosoŵa zapadera za mwana wawo, akumakumbukira chitonthozo chotsimikizirika choperekedwa kwa makolo pa Miyambo 22:6.

Imodzi ya njira zochiritsira zamkangano koposa ndiyo kupereka mankhwala. Mankhwala operekedwa kaŵirikaŵiri, Ritalin, ali ndi zotulukapo zabwino ndi zoipa. Mabanja ambiri akondwera ndi kupita patsogolo kwa mwana wawo pamene akulandira Ritalin kapena mankhwala ena owongolera machitidwe. Komabe, mkangano umene ulipo tsopano ukupitirizabe, osati kokha ponena za thandizo la mankhwala ameneŵa komanso ponena za kuwalemba ochulukitsitsa ndi mwakaŵirikaŵiri kwambiri. Kwenikweni, madokotala ena akukayikiriratu phindu lake, mwachitsanzo akumati, kugwiritsira ntchito Ritalin nthaŵi yaitali kungakhale ndi ziyambukiro zambiri zovulaza. Komabe, kuyenera kugogomezeredwanso kuti mabanja ambiri ndi madokotala atchula ziyambukiro zoipa zoŵerengeka chabe ndi kuti aona khalidwe lowongokera ndi kupita patsogolo m’maphunziro. Mokondweretsa, achikulire ambiri omwe apimidwa ndi kupezedwa ndi ADD amenenso pakali pano akulandira mankhwala alinso okondwa ndi zotulukapo zake. Chotero, kugwiritsira ntchito mankhwala kuli chosankha chaumwini chozikidwa pa kufufuza ndi kulingalira kosamalitsa.

Kwa amene ayesa mankhwala nakhala ndi zotulukapo zoipa, palinso njira zina zochiritsira. Mabanja ambiri aŵerenga ndi kupeza zotulukapo zabwino za machiritsidwe a vitamini ndi zitsamba kapena kugwiritsira ntchito zonse ziŵiri. Monga momwe taonera poyamba, ADD/ADHD nthaŵi zina ingachititsidwe ndi kusokonekera kwa makemikolo a thupi mu ubongo kumene kumakhulupiriridwa kuti kumawongoleredwa ndi machiritsidwe ameneŵa.

Ndiponso, palinso zinthu zina zimene ena amakhulupirira kuti zimayambitsa mavuto ena ambiri okhudza ADD/ADHD. Dr. Doris Rapp, m’buku lake lakuti Is This Your Child?, akunena kuti “ana ena ali ndi matenda akuthupi ndi/kapena amalingaliro, akhalidwe, ndi mavuto akuphunzira omwe mwapang’ono kapena kwakukulukulu amachititsidwa ndi zoyambukira thupi kapena choyambukira china cha m’malo okhala.” Ndiponso, kuyambukiridwa ndi utoto, shuga, ndi zokoleretsa kungabutse mavuto ameneŵa mwa kukhala ndi mtima wonyamuka mwachiwawa, kusinthasintha khalidwe, ndi kusaona tulo.

Mabanja ambiri aphunzira mmene angasinthire khalidwe la ana awo, komabe nzeru ya maphunziro ya ana awo ingachititse mavuto enanso. Kwa ena, mautumiki apadera onga kuphunzitsidwa, kupatsidwa uphungu, magulu olimbikitsana, ndi aphunzitsi apadera angathandize. Chifukwa chakuti ana ameneŵa amaoneka kukhala akuchita bwinopo pamkhalidwe wa anthu aŵiri, mabanja ena, mopatsidwa malingaliro ndi dokotala wawo, asimba za chipambano cha sukulu ya panyumba.

Chofunikanso kuzindikira ndicho maprojekiti ambiri a kuphunzitsa, onga ya Dr. Mel Levine yakuti Schools Attuned, imene imasonyeza kusiyana kwa munthu payekha ndi kusiyanasiyana kwakukulu kwa ana. Programu ya Dr. Levine imachirikiza kusintha maphunziro kuti akwaniritse zosoŵa za mwana aliyense. Kulikonse kumene njira yofutukulidwa ya kaphunzitsidwe imeneyi yagwiritsiridwa ntchito mu United States, zotulukapo zikuoneka kukhala zabwino.

Mtsogolo

Kulera ana kungafaniziridwe ndi kugula nyumba yatsopano. Zonse ziŵirizo zimafuna kuwononga ndalama kwa moyo wonse; komabe, chifukwa cha mikhalidwe, oyembekezeredwa kugula angakakamizike kukhutira ndi yosakhala bwino koposa. Mofananamo, makolo opanda ungwiro olera ana opandanso ungwiro m’dziko la Satana amakakamizika kukhutira ndi zosakhala bwino koposa. Nyumba yogulidwa chatsopano ingakhale ndi mbali zosaoneka bwino kapena zosakondweretsa, koma mwa kugwirirapo ntchito ndi luso pang’ono, mbali zambiri zosaoneka bwino zingawongoleredwe. Ngakhale mbali yake yocholoŵana m’kamangidwe mwamsanga ingakhale mbali yochititsa chidwi ya panyumbapo.

Mofananamo, ngati makolo asinthira ku zosoŵa zapadera za mwana wawoyo, iye angakhale mbali yokongola ya miyoyo yawo. Mwana aliyense ayenera kuzindikiridwa ndi mikhalidwe yakeyake. Motero, sumikani maganizo pa mbali zabwino. M’malo mwa kutsendereza ana, limbikitsani luso la mmodzi ndi mmodzi, ndipo zindikirani kuti iye ali munthu wofunikira ulemu ndi chikondi—mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova Mulungu.—Salmo 127:3-5.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena