Pamene Ana Abedwa ndi Anthu Osawadziŵa
“TITHANDIZENI KUMFUNAFUNA CHONDE. ANTHUNI THANDIZANI SARA CHONDE!”
Dandaulo lomvetsa chisoni limeneli la makolo aŵiri ovutika mtima kwambiri linasonyezedwa pa wailesi yakanema mu United States monse poyesayesa kupeza mwana wawo wamkazi wa zaka 12, Sara Ann Wood. Iye anali atafwambidwa milungu itatu yapitayo pamene anali kuyenda panjinga kumka kwawo mu msewu wa m’malo a ulimi amene anali kukhalamo.
GULU lalikulu la ofunafuna linafufuza m’tchire lonse, m’minda, ndi m’nyanja zapafupi likumafunafuna zizindikiro za msungwana wosoŵayo. Pafupifupi panthaŵi yofananayo, Tina Piirainen, kholo lina lovutika mtima kwambiri m’boma loyandikana nalo, anasonyezedwanso pa wailesi yakanema akumachonderera za mwana wake wamkazi wosoŵa. Atanyengereredwa kuloŵa m’kanjira ka m’tchire, Holly wa zaka khumi anazimiririka m’nyengo yosafika ola. Pambuyo pake mtembo wake unapezedwa m’munda.
Moyo wa makolo a ana osoŵa umakhala wopweteka. Iwo tsiku ndi tsiku amalimbana ndi nkhaŵa yakuti kaya mwanayo ali moyo, kapena akuvulazidwa kapena akugonedwa, kaya kapena wafa, monga mmene zinalili kwa Ashley wachichepereyo. Ashley anapita ndi makolo ake kukaonerera mlongo wake pampikisano wa maseŵero a mpira. Atatopa ndi kuonerera, anamka kubwalo la maseŵero—nangozimiririka. Pambuyo pake, mtembo wa Ashley unapezedwa m’munda wina wapafupi. Anali atanyongedwa.
Tsoka Lowopsa
Mu United States, chaka chilichonse, mabanja oyambira pa 200 kufikira pa 300 amakhala ndi tsoka lowopsa la kufwambidwa kwa mwana ndiyeno mwina mwake osadzaonanso mwanayo ali wamoyo. Pamene kuli kwakuti ziŵerengero zake zikuonekera kukhala zazing’ono poyerekezera ndi maupandu ena achiwawa amene amachitidwa, mantha ndi nthumanzi zimene zimagwira zitaganya zonse zimayambukira anthu zikwi zambiri. Motekeseka maganizo kwambiri iwo amafunsa kuti, ‘Kodi tsoka lotero lingachitike motani kuno? Kodi mwana wanga adzakhala wotsatira?’
Mu United States, chiŵerengero cha pachaka cha ana obedwa chochitiridwa lipoti chili pakati pa 3,200 ndi 4,600. Zigawo ziŵiri mwa zitatu za ameneŵa kapena kuposa pamenepo amagonedwa. Ernest E. Allen, pulezidenti wa National Center for Missing and Exploited Children, anati: “Chifukwa chachikulu chochitira zimenezi ndicho cha kuwagona, motsatiridwa ndi cholinga cha kuchita mbanda.” Ndiponso, malinga ndi kunena kwa Dipatimenti ya Chiweruzo, kubedwa kwina kwa ana koposa 110,000 kumayesedwa chaka chilichonse, makamaka ndi oyenda pa galimoto, kaŵirikaŵiri amuna, akumayesa kunyengerera mwana kuloŵa m’galimoto lawo. Maiko ena akuyang’anizananso ndi chiwawa chachikulu pa ana.
Kodi Chitaganya Chili ndi Mlandu?
Ponena za kupha ana, wofufuza wina wa ku Australia akusonyeza kuti “si chinthu chongodzichitikira.” M’buku lake Murder of the Innocents—Child-Killers and Their Victims, Paul Wilson akunena kuti “akupha ndi ophedwa omwe amagwidwa mu mkhalidwe woipitsitsa umene chitaganya chenichenicho chapanga.”
Kungaonekere kukhala kodabwitsa kuganiza kuti chitaganya cha anthu chingakhale ndi mlandu wake, kapena mwina mwake kuchirikiza tsoka limeneli, popeza kuti anthu ochuluka amaona kulimidwa pamsana ndi mbanda kwa ana kukhala machitidwe oipitsitsa. Komabe, zitaganya za anthu zotukuka, ndipo ngakhale zimene zili zosatukuka kwambiri, nzodzazidwa ndi mafilimu, akanema a pa TV, ndi zofalitsidwa zotamanda kugonana ndi chiwawa.
Tsopano pali mafilimu ambirimbiri osonyezedwa mopanda manyazi a zithunzithunzi zaumaliseche osonyeza ana ndipo ngakhale achikulire ovala ngati ana. Ameneŵa amasonyeza chithunzithunzi cha kugonana kwenikweni ndi chiwawa choloŵetsamo ana. Wilson akusonyezanso m’buku lakelo kuti pali maina a akanema monga yotchedwa Death of a Young One, Lingering Torture, ndi Dismembering for Beginners. Kodi oonerera chiwawa chankhanza chimenechi ndi zithunzithunzi zaumalisechewo ndi ambiri motani? Ndi indasitale ya mamiliyoni zikwizikwi a madola!
Chiwawa chosonyezedwa mosabisa ndi zithunzithunzi zaumaliseche za kugonana zili ndi chiyambukiro chachikulu kwambiri pa miyoyo ya awo amene amalima pamsana ana. Munthu wina woimbidwa mlandu amene anapha anyamata achichepere asanu amene anawagona anaulula kuti: “Ine ndine wamathanyula wa ana woimbidwa mlandu wambanda, ndipo zithunzithunzi zaumaliseche ndizo zinali choputira cha kuwonongeka kwanga.” Profesa Berit Ås, wa ku Oslo University, akufotokoza za chiyambukiro chimene zithunzithunzi zaumaliseche wa mwana zili nacho: “Tinalakwa kwambiri pamapeto a ma 1960. Tinkakhulupirira kuti zithunzithunzi zaumaliseche zingaloŵe m’malo mwa maupandu a kugonana mwa kupereka kanthu kena koziziritsa mtima kwa opalamula milandu ya kugona ena, ndipo tinachotsa ziletso zake. Tsopano tikudziŵa kuti tinalakwa: zithunzithunzi zaumaliseche zotero zimaloleza maupandu a kugona ena. Zimachititsa wopalamulayo kuganiza kuti, ‘Ngati ndingathe kuonerera zimenezi, kuzichita kuyeneranso kukhala kwabwino.’”
Chikhumbo cha munthu wachikulire cha kutenthedwa chimakula pamene akhala womwerekera m’zithunzithunzi zaumaliseche. Monga chotulukapo chake, ena amafunitsitsa kugwiritsira ntchito kaya kunyengerera kapena chiwawa kuti apeze ana owagwiritsira ntchito pa cholinga chawo choipacho, kuphatikizapo kugwirira chigololo ndi mbanda.
Pali zochititsa zina za kubedwa kwa ana. M’maiko ena zimenezi zawonjezereka chifukwa cha mikhalidwe yoipa yazachuma. Pokopeka ndi ndalama zambiri za dipo zolipiridwa ndi mabanja achuma, achifwamba amalunjika pa kuba ana. Chaka chilichonse makanda ambiri amabedwa ndi kugulitsidwa kumagulu osunga ana mobisa amene amawatulutsira kunja kwa dzikolo.
Kodi ndani amene amapanga mbali yaikulu ya ana osoŵa? Kodi nchiyani chimene chimawachitikira? Nkhani ziŵiri zotsatira zidzafotokoza nkhaniyi.
[Bokosi patsamba 6]
Mamiliyoni A Ana Ochita Uhule
Malinga ndi kunena kwa United Nations, pafupifupi ana mamiliyoni khumi, makamaka m’maiko osatukuka, aumirizidwa kuloŵa mu uhule, ambiri a iwo ali amene afwambidwa. Ntchito yoipa imeneyi yawonjezeka mu Afirika, Asia, ndi Latin America limodzi ndi kuwonjezeka kwa alendo oona malo m’maiko ena. M’madera ena, pakati pa mamiliyoni ambiri a odzaona malo m’maiko ena, makamaka ochokera ku maiko achuma, pafupifupi zigawo ziŵiri mwa zitatu ndiwo “oona malo ofunafuna ogonana nawo.” Koma pali tsiku la kuŵerengera mlandu, popeza kuti maupandu a munthu ali ‘pambalambanda ndi ovundukuka pamaso pake pa iye amene tichita naye,’ Yehova Mulungu.—Ahebri 4:13.
[Chithunzi patsamba 5]
Pamene mwana abedwa limakhala tsoka lowopsa