Pamene Makolo Achita Kufwambako
PAMBUYO pa kuvutika ndi kumenyedwa kwakukulu ndi kuchitiridwa nkhanza mwamalingaliro kwa zaka zambiri ndi mwamuna wake, ndiyeno potsirizira pake kusiyidwa chifukwa cha mkazi wina, Cheryl anakapempha chisudzulo.a Atapatsidwa chilolezo chonse cha kuyang’anira ana ake ndi bwalo lamilandu, bata linayamba kubwerera pang’onopang’ono pamene anayamba kukonzanso moyo wake—kufikira tsiku lina pamene telefoni inalira. Anali yemwe kale anali mwamuna wake. Iye anati: “Ngati ukufuna kuonanso ana ako, uyenera kuvomereza zokwatirananso nane”! Pokhala oletsedwa kubwerera kwa amawo pambuyo pa kucheza kwa mwezi umodzi ndi atate wawo m’dziko lakwawo, ana a Cheryl anafwambidwa.
Atathedwa mphamvu, Cheryl anapempha thandizo ku U.S. State Department koma sanapeze njira ya lamulo yopezeranso ana ake okhala m’dziko lina. Mkhalidwe wa kusoŵa chochita kotheratu umene anali nawo m’zaka zambiri za kumenyedwa unabwereranso. “Zimangokhala chimodzimodzi,” iye akufotokoza motero. “Sudziŵa mmene ungaziletsere.”
“Nkhanza ya Maganizo”
Kufwamba kochitidwa ndi kholo kwatchedwa kuti “mchitidwe waukulu koposa wa nkhanza ya maganizo” wochitidwira kholo lina ndi mwana. Carolyn Zogg, mkulu wa Child Find of America, Inc., anati ponena za ofwambawo: “Makolo ambiri amene amachita zimenezi amalipsira, ndipo amalipsira m’njira yoipa kwenikweni yothekera ndiponso pambali imene ili yangozi kwambiri. Mbali imeneyo ndiyo yapamtima koposa kwa [makolo amene ali ndi lamulo la uyang’anirowo]—chuma chawo chamtengo wapatalicho, ana awo. . . . Samaganiza za mwanayo, koma za iwo eni chabe ndi kubwezera—kulipsira.”
Kufwambidwa kwa mwana sikumangochititsa kholo kukhala lokwiya, lotayikiridwa, losoŵa chochita, ndi nkhaŵa koma pafupifupi nthaŵi zonse kumavulaza ubwino wa malingaliro a mwana kumlingo winawake. M’zochitika zina mwana angaumirizike kukhala wothaŵathaŵa, akumapeŵa kuyanjana kwapafupi ndi kumva zinthu zopotozedwa ndi mabodza ponena za kholo lina. Chochitikacho chingatulutse kusokonezeka kwa m’thupi, monga ngati kukodzera pabedi, kusoŵa tulo, kukakamira kwa womsamalira, kuwopa mazenera ndi zitseko, ndi kukhala ndi mantha aakulu. Ngakhale mwa ana osinkhukirapo, chingatulutse chisoni ndi mkwiyo.
Mu United States, muli zochitika zoposa 350,000 chaka chilichonse zimene kholo lina limatenga mwana moswa lamulo la kuyang’aniridwa kwa mwana kapena kulephera kubweza mwanayo panthaŵi yololedwa. M’zochitika zoposa 100,000 za zimenezi, mwana amabisidwa ndi chiŵalo cha banja ndi cholinga cha kumletseratu kukakhala ndi kholo linalo. Ena amatulutsidwa m’malowo kapena ngakhale m’dzikolo.
Zifukwa Zina
Kodi chimene chimasonkhezera makolo kuba ana awo ndi chikhumbo cha kuyanjananso kapena mzimu wa kulipsira? Michael Knipfing wa Child Find akufotokoza kuti makolo ena amawopa kugonjetsedwa mu nkhondo ya uyang’aniro ndi yemwe kale anali mnzawo wa muukwati ndi kuti “chifukwa cha mantha iwo amangodzichitira zinthu.” Kapena pamene uyang’anirowo waperekedwa kwa wina ndipo kholo lina lipitiriza kukaniza winayo kuyenera kwake kwa kuona ana, pamakhala kugwiritsidwa mwala. Knipfing akufotokoza kuti: “Ngati mumakonda mwana wanu ndipo mukukanizidwa kuona mwana wanuyo, mumayamba kulingalira kuti palibenso njira ina yoposa kulanda mwanayo ndi kuthaŵa naye.”
Iye akunenanso kuti ‘anthu ochuluka samazindikira za zotulukapo za kufwamba mwana. Samazindikira kuti adzavutika kuti apeze ntchito. Lamulo la kugwidwa kwawo limaperekedwa. Amaganiza kuti vutolo langokhala la pakati pawo ndi kholo linalo. Samazindikira kuti apolisi amaloŵetsedwamo. Amafunikira maloya aŵiri m’malo mwa mmodzi chifukwa chakuti tsopano iwo ali ndi mlandu wa upandu woti ayang’anizane nawo ndiponso mlandu wamba, umene uli wonena za amene ayenera kuyang’anira mwana.’
Makolo ena angalingalire kuti mwana wawo akuvulazidwa ndi kholo linalo. Ngati bwalo lamilandu lichedwa kuchitapo kanthu, pamenepo kholo lothedwa nzerulo lingachitepo kanthu kena mosasamala kanthu za zotulukapo zake. Zimenezi zinaonedwa m’nkhani ya Hilary Morgan wa zaka zisanu. Dokotala wina wamalingaliro a ana analangiza kuti kuonana kwa Hilary ndi atate wake kulekeke, akumasonyeza umboni wa kusokoneza mwanayo kukhala “womvekera bwino ndi wokhutiritsa.” Komabe, bwalo lamilandu linati kusokoneza mwanako kunali kosatsimikizirika bwino ndipo linapereka chilolezo cha kuona mwanayo popanda kuyang’aniridwa. Dr. Elizabeth Morgan, amake a Hilary, moswa lamulo la bwalo lamilandu, anabisa mwana wawo wamkaziyo. Anthu ambiri amasonkhezeredwa kuchitira chisoni kholo limene limafwamba mwana ndi kuthaŵa kukabisalalo.
Ponena za Elizabeth Morgan, anatayikiridwa ntchito yake yaudokotala wa opaleshoni, anathera zaka zoposa ziŵiri m’ndende, ndi kukhala ndi ngongole za kuchipatala ndi za milandu zoposa madola 1.5 miliyoni. Iye anafotokoza mu U.S.News & World Report kuti: “Akatswiri amandiuza kuti mwana wanga akanakhala wosokonezeka maganizo kwachikhalire tsopano ngati ndikanaleka kuletsa kumsokonezako. . . . Ndinafunikira kuchita ntchito imene bwalo lamilandu linakana kuchita: Kupulumutsa mwana wanga.”
Mawu onenedwa ndi ofufuzawo Greif ndi Hegar ponena za kuba ana kochitidwa ndi makolo alidi oona: “Zimenezi nzochitika zocholoŵana kwambiri kwakuti, monga momwe dziŵe la madzi lakuya, limaoneka mosiyana pang’ono zikumadalira ndi mbali yake; nthaŵi iliyonse pamene munthu uyang’ana m’madzimo umaona kanthu kena katsopano.”—When Parents Kidnap—The Families Behind the Headlines.
Kuwonjezera pa ana ofwambidwa ndi kholo kapena ndi munthu wosamdziŵa, pali mamiliyoni a ana ena osoŵa padziko lonse—otayidwa ndi othaŵa kwawo. Kodi iwo ndi ayani, ndipo kodi nchiyani chimene chimawachitikira?
[Mawu a M’munsi]
a Dzina lasinthidwa.