Woyenera Kusunga Ana—Kuiona Bwino Nkhaniyo
NTHAŴI zambiri, pamakhala vuto lalikulu anthu atasudzulana, polimbirana kuti mwana aziwakonda ndi kumsunga. Nthaŵi zina mwambi wakuti, “Ndewu imafuna anthu aŵiri” sumakhala woona. Ingakhalepo ngati kholo limodzi lokha nlovuta ndipo limaumirira zofuna zake. Loya wa zabanja wa ku Toronto, Canada, anati: “Pamilandu ya banja, pamakhala kukwiya ndipo zonse zimakhudza mtima.”
M’malo moganiza za zimene zingamkhalire bwino mwana, makolo ena amapitiriza mkanganowo mwa kumadula zisamani. Mwachitsanzo, ena ayesa kunena kuti asinthe kholo limene likusunga mwana chifukwa khololo lili mmodzi wa Mboni za Yehova ndipo mwanayo sadzapeza mpata wokhala ndi ‘moyo wabwino.’
Kholo losakhala Mboni linganene nkhani ya kukondwerera masiku a kubadwa, Krisimasi, kapena ngakhale Halloween. Ena angadandaule kuti mwana sadzakhala ndi mayanjano abwino ndi kuti sadzagwirizana ndi anzake ngati asankha kusachitira suluti mbendera. Kapenanso ena anganene kuti mwanayo adzasokonezeka mwa kutsagana ndi kholo pokalankhula ndi ena za Baibulo. Makolo ena osakhala Mboni afika ngakhale ponena kuti moyo wa mwanayo udzakhala pangozi chifukwa kholo limene lili Mboni silingalole mwanayo kuikidwa mwazi.
Kodi Mkristu angatani nalo vuto lokhudza mtima kwambiri limenelo lamkangano? Kuchita zinthu mokwiya—“kuthira mchere pachilonda”—sikudzathandiza. Ngati nkhaniyo yapita kwa woweruza, kholo lililonse lidzakhala ndi mpata woti amve zonena zake. Nkofunika kwambiri kukumbukira uphungu wa Baibulo wakuti: “Umsenze Yehova nkhaŵa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza: nthaŵi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Mwa kusinkhasinkha zimenezi ndi mwa kutsatira mapulinsipulo a Baibulo, makolo angathe mothandizidwa ndi Yehova, kulimbana ndi zotsatira zilizonse zokhudza amene ayenera kusunga ana.—Miyambo 15:28.
Kulolera
Nkhani yofunika kwambiri ndiyo zimene zingamkhalire bwino mwana. Ngati kholo likufuna zopambanitsa, mwina sangalilole kusunga mwana ndipo angachepetse ufulu wake woona ana. Kholo lanzeru limachita mwamtendere, pokumbukira uphungu wa Baibulo wakuti: “Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. . . . Patukani pamkwiyo . . . Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.” (Aroma 12:17-21) Kaya akhale m’khoti, mu ofesi ya loya, kapena pamaso pa wopenda amene ayenera kusunga mwana, makolo afunikira kutsimikiza kuti ‘kufatsa [“kulolera,” NW] kwawo kukuzindikirika ndi anthu onse.’—Afilipi 4:5.
Nthaŵi zina wosudzulana naye angayese kunyenga ena mwa kupereka zifukwa zosokeretsa ndi zopeka. Kuli kwanzeru kuletsa chibadwa chaumunthu chokwiya kwambiri ndi mawu okhumudwitsa ameneŵa. Aja osudzulana nawo amakonda kugwiritsira ntchito nkhani za umoyo, chipembedzo, ndi maphunziro pofuna kupeka bodza pamlandu wa woyenera kusunga ana.—Miyambo 14:22.
Kulolera kumaphatikizapo nzeru yoona maumboni ndi yomvana bwinobwino. Kholo lililonse siliyenera kuiŵala kuti ngakhale anasudzulana, mwanayo akali ndi makolo aŵiri. Makolowo anasudzulana inde, koma sanasudzulane ndi mwana ayi. Chifukwa chake, pokhapo zitanyanya kwambiri, kholo lililonse liyenera kukhala ndi ufulu wochita ukholo pamene lili ndi mwanayo. Liyenera kukhala ndi ufulu wofotokoza maganizo ake ndi zokonda zake ndi woti mwana azichitako ntchito zololeka za makolo, zachipembedzo kapena zina zilizonse.
Tiyeni tipende zimene zingakhale zigamulo pamlandu: (1) kusunga mwana makolo aŵiri, (2) kusunga mwana kholo limodzi, ndi (3) malire a ufulu woona mwana. Kodi kusunga mwana makolo aŵiri kumasiyana bwanji ndi kusunga mwana kholo limodzi? Kodi mungatani ngati akulandani ufulu wosunga mwana? Nanga bwanji ngati kholo linalo nlochotsedwa?
Kusunga Mwana Makolo Aŵiri
Oweruza ena amakhulupirira kuti mwana afunikiradi kumaonana ndi makolo onse aŵiri. Amaganiza zimenezo chifukwa cha zofufuza zimene zimasonyeza kuti ana samapsinjika maganizo kwambiri kapena kupwetekeka mtima makolowo atasudzulana ngati iwowo athandizana kusunga mwana. M’malo moganiza kuti kholo linalo lamnyanyala, mwanayo adzaona kuti makolo aŵiriwo amamkonda ndipo adzagwirizana ndi mabanja aŵiriwo. “Kusunga mwana makolo aŵiri ndiyo njira yoti makolo aŵiriwo azithandizana,” akutero loya wa milandu ya banja.
Komabe, Dr. Judith Wallerstein, mkulu wa bungwe la Center for the Family in Transition, ku Corte Madera, California, akuchenjeza kuti makolo afunikira kukhala ogwirizana ndipo mwanayo ayenera kukhala wosavuta kuzoloŵera ndi kumvana ndi anthu kuti makonzedwe a kusunga mwana makolo aŵiri atheke. Mikhalidwe imeneyi njofunika chifukwa makolo aŵiri osunga mwanawo amakhalabe ndi ufulu walamulo wosankha zochita pankhani zokhudza umoyo, maphunziro, maleredwe a m’chipembedzo, ndi moyo wa mwanayo pa mayanjano ake ndi anthu ena. Koma zimenezo zimatheka kokha ngati makolo aŵiriwo ali ololerabe polingalira zimene zingamkhalire bwino mwana wawo osati zimene zingawakhalire bwino iwo paokha.
Kusunga Mwana Kholo Limodzi
Khoti lingagamule kuti kholo limodzi limene, malinga ndi kuganiza kwawo, lili lokonzeka bwino kusamalira zosoŵa za mwana, ndilo lizisunga mwana. Woweruza angagamule kuti kholo losunga mwanalo ndilo lokha limene lizisankha zochita pankhani zofunika zokhudza ubwino wa mwana. Nthaŵi zambiri, khoti limagamula zimenezo litamvetsera zimene ofufuza apeza—nthaŵi zambiri ameneŵa ndi akatswiri a zamaganizo, madokotala a nthenda zamaganizo, kapena antchito yothandiza anthu.
Ochirikiza mfundo yakuti kholo limodzi liyenera kusunga mwana amakhulupirira kuti makonzedwewo amathandiza mwanayo kukhazikika kwambiri. Pamene makolo alephera, kapena sangathe kulankhulana bwino, oweruza ambiri amasankha makonzedwe ameneŵa osungira mwana. Inde, kholo losayenera kusunga mwanayo silimaiŵalikiratu pamoyo wa mwanayo ayi. Kaŵirikaŵiri kholo losayenera kusunga mwana amalipatsa ufulu woona mwanayo, ndipo makolo aŵiriwo angapitirize kumpatsa malangizo ofunikira mwanayo ndi kumkonda.
Ufulu Woona Mwana
Ngati makolo aganiza kuti pankhani ya woyenera kusunga ana payenera kukhala “wopambana” ndi “wolephera” ndiye kuti sakulingalira bwino. Makolo amaukhoza ukholo wawo “napambana” pamene aona ana awo akukula kukhala anthu achikulire okhwima, okhoza, ndi olemekezeka. Kukhoza polera mwana sikumatheka chifukwa choti khoti lapatsa munthu mphamvu yosunga mwana. Mwa kulabadira zofunika za khoti pankhani za woyenera kusunga ana, ngakhale pamene zimenezo zikuoneka ngati zokondera, Mkristu amasonyeza kuti ‘akumvera maulamuliro aakulu.’ (Aroma 13:1) Ndi bwinonso kukumbukira kuti imeneyo si nthaŵi yolimbirana chikondi kapena kukhulupirika kwa ana mwa kuchepsa kholo linalo pofuna kuwononga unansi wake ndi iwo.
Pali zitsanzo za m’Baibulo za makolo oopa Mulungu amene pazifukwa zosiyanasiyana, anasiyana ndi ana awo. Mwachitsanzo, Amramu ndi Yokobedi, makolo a Mose, pochita zokomera mwana wawo, anamuika m’kabokosi koyandama “pakati pa mabango m’mbali mwa nyanja.” Pamene khandalo analivuula m’madzi mwana wamkazi wa Farao, iwo anakhulupirirabe Yehova. Makolo anzeru ameneŵa okhulupirika anafupidwa ndi ufulu wochuluka “woona mwana” umene anaugwiritsira ntchito bwino lomwe kuphunzitsa mnyamatayo njira ya Yehova. Mose anakula nakhala mtumiki wamphamvu wa Mulungu woona.—Eksodo 2:1-10; 6:20.
Nanga bwanji ngati kholo lina nlochotsedwa? Kodi kholo lachikristu liyenera kulola kuti kholo linalo lizidzaona mwana? Kuchotsa kumene mpingo umachita kumangosintha unansi wauzimu wa munthuyo ndi mpingo wachikristu. Kwenikweni, kumadula mgwirizano wauzimu. Koma unansi wa kholo ndi mwana umakhalapobe. Kholo losunga mwanalo liyenera kulemekeza ufulu wa kholo lochotsedwa wodzaona mwana. Komabe, ngati kholo losayenera kusunga mwanalo likhoza kumvulaza kapena kumsokoneza maganizo, ndiye kuti khoti (osati kholo losunga mwanalo) lingalinganize kuti pazikhala munthu wina woyang’anira pamene khololo libwera kudzaona mwanayo.
Simuli Nokha
Milandu ya chisudzulo ndi mikangano yotsatirapo yokhudza woyenera kusunga ana imatha munthu mphamvu. Ukwati umene unayamba bwinobwino wasweka limodzi ndi zolinga za banjalo, mapulani, ndi zimene anali kuyembekeza. Mwachitsanzo, kusakhulupirika kapena nkhanza yonyanya zingakakamize mkazi wokhulupirika kufuna kuti boma limteteze iye ndi mwana wake. Komabe, angadzimvebe wamlandu ndi wopereŵera poyesa kupeza chimene chinalakwika kapena njira yabwino imene nkhaniyo akanaisamalira. Mabanja ambiri amada nkhaŵa ndi mmene kusweka kwa banja kumakhudzira ana awo. Nkhondo ya m’khoti yokhudza woyenera kusunga ana ingakhale nkhani yosautsa mtima imene siimangoyesa chabe kukhulupirika kwa munthu monga kholo lachikondi komanso imayesa chikhulupiriro chake ndi chidaliro mwa Yehova.—Yerekezerani ndi Salmo 34:15, 18, 19, 22.
Pamene wosalakwayo achitapo kanthu chifukwa cha nkhanza pa ana kapena kuchitidwa nkhanza konyanya ndi mnzake kapena kuteteza thanzi lake kuti asatenge matenda opatsana mwa kugonana kwa mnzake wolakwayo, palibe chifukwa choti wosachimwayo adzimve wamlandu kapena kuti Yehova wamnyanyala. (Salmo 37:28) Wolakwayo kapena wankhanza kwa mnzakeyo ndiye waswa pangano lopatulika la ukwati ndi ‘kumchitira chosakhulupirika’ mnzake.—Malaki 2:14.
Pitirizani “kukhala nacho chikumbumtima chabwino” pamaso pa anthu ndi pa Yehova mwa kutsatira mapulinsipulo a Baibulo, kuchita naye moona mtima mnzanu amene munasudzulana naye, ndi kukhala wololera pamakonzedwe anu a kusunga mwana. ‘Nkwabwino kumva zoŵaŵa chifukwa cha kuchita zabwino, ngati chitero chifuniro cha Mulungu, kuposa kumva zoŵaŵa chifukwa cha kuchita zoipa.’—1 Petro 3:16, 17.
Ponena za ana, amafunika kuwatonthoza kuti kusweka kwa banja si mlandu wawo. Nthaŵi zina zinthu sizimakhala monga momwe zinalinganizidwira. Koma kutsatira mapulinsipulo a Baibulo kungafeŵetse zinthu pambuyo pa chisudzulo mwa kulimbikitsa kukambirana komasuka ndi kumvana pakati pa makolo ndi ana. Mwachitsanzo, zimenezi zingachitidwe mwa kulola ana kutengamo mbali polinganiza moyo wa banja pambuyo posudzulana. Mwa kuleza mtima ndi kukoma mtima ndiponso mwa kulingalira za zimene ana akuganiza ndi kumvetsera zonena zawo, mudzawathandiza kwambiri kuzoloŵera njira yatsopano yochitira zinthu ndiponso moyo watsopano.
Enanso Angathandize
Makolo sindiwo okha amene angathandize mwana wawo pamene banja lawo lasweka. Achibale, aphunzitsi, ndi mabwenzi angathandize kwambiri mwana wa m’chisudzulo ndi kumlimbikitsa. Makamaka, agogo angathandize kwambiri kuti anawo akhazikike nalimbike mtima.
Agogo achikristu angapatse anawo malangizo auzimu ndi zochita zoyenera, koma ayenera kulemekeza zimene makolo anasankha zokhudza maleredwe a m’chipembedzo, pakuti malinga ndi chikhalidwe ndi lamulo, makolo, osati agogo, ndiwo ali ndi udindo wosankha zimenezo.—Aefeso 6:2-4.
Pokhala ndi chichirikizo chotero, ana a m’chisudzulo angapirire kusweka kwa ukwati wa makolo awo. Ndipo angapitirize kuyembekeza mwachidwi madalitso a m’dziko latsopano la Mulungu, mmene mabanja onse adzamasuka ku “ukapolo wa chivundi, ndi kuloŵa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21; 2 Petro 3:13.
[Bokosi patsamba 29]
Kuwongolera Maganizo Olakwika
“Lilime la anzeru linena bwino zomwe adziŵa,” ndipo kholo lachikristu lili ndi mpata wabwino wowongolera maganizo olakwika kapena zokayikitsa. (Miyambo 15:2) Mwachitsanzo, ponena za umoyo wa ana awo, “Mboni za Yehova zimalandira mankhwala ndi kuvomera opaleshoni,” koma ataisankha kukhala kholo loyenera kusunga mwana, Mboni imakhala ndi ufulu wovomereza modziŵa machiritso alionse.a—The Journal of the American Medical Association.
Mboni za Yehova zimaona kuti chipembedzo chawo, chozikidwa pa Mawu a Mulungu, Baibulo, nchofunika kwambiri. Chimenechi chimachititsa anthu kukhala atate abwino, amayi abwino, ana abwino, mabwenzi abwino, anansi abwino, ndi nzika zabwino. Makolo achikristu amapereka chilango mwachikondi, kuwathandiza kulemekeza ulamuliro ndi kuwakonzekeretsa ana awo kukhala ndi kakhalidwe kabwino m’moyo.b—Miyambo 13:18.
Maphunziro akusukulu amafunika kwambiri pa kukula kwa mwana, ndipo Mboni za Yehova zimafuna kuti ana awo apeze maphunziro abwino koposa.c—Miyambo 13:20.
[Mawu a M’munsi]
a Onani brosha lakuti Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu?, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
b Onani buku lakuti Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja, mitu 5-7, 9, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
c Onani brosha lakuti Mboni za Yehova ndi Maphunziro, lofalitsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania.
[Chithunzi patsamba 28]
Kholo losunga mwana liyenera kumvetsera moleza mtima pamene mwanayo akufotokoza za kucheza kwake ndi kholo limene silikumsunga