Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 12/8 tsamba 23-26
  • Woyenera Kusunga Anah—Chipembedzo ndi Lamulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Woyenera Kusunga Anah—Chipembedzo ndi Lamulo
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ufulu Wofunika Kwambiri wa Makolo ndi Ana
  • Ufulu wa Makolo Amene Ali Osayenera Kusunga Ana
  • Kukambirana Loya Alipo Kunja kwa Bwalo la Milandu
  • Woyenera Kusunga Ana—Kuiona Bwino Nkhaniyo
    Galamukani!—1997
  • Kodi Chingamkhalire Bwino Mwana Nchiyani?
    Galamukani!—1997
  • Makolo Olera Ana Ali Okha Amakhala ndi Mavuto Ambiri
    Galamukani!—2002
  • Pamene Makolo Achita Kufwambako
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 12/8 tsamba 23-26

Woyenera Kusunga Anah—Chipembedzo ndi Lamulo

PAMILANDU ya chisudzulo ndi yokhudza woyenera kusunga ana, chipembedzo chingakhale chofunika—ndiponso chovuta zedi. Mwachitsanzo, pangabuke mafunso onga otsatirawa.

Kodi woweruza ayenera kulingalirapo pa umboni wonena kuti kholo linalo siliyenera kusunga ana chifukwa chakuti khololo lili la chipembedzo china, makamaka chipembedzo chimene chili ndi anthu ochepa? Kodi woweruza ayenera kupenda umboni wonena za zikhulupiriro ndi miyambo ya chipembedzo cha makolo kuti adziŵe chipembedzo chimene, malinga ndi kuganiza kwake, chingamyenerere mwanayo? Ndiyeno kodi iye angagamule kuti mwanayo akulire m’chipembedzocho ndi kuletsa kuti mwanayo asaphunzitsidwe za chipembedzo chinacho?

Lerolino, anthu ambiri amakwatirana osakhala a chipembedzo chimodzimodzi kapena a fuko limodzimodzi. Chotero mabanja ameneŵa atasudzulana, ana angakhale atazoloŵera kale zipembedzo ziŵiri. Nthaŵi zina, kholo lina pamlandu wa osudzulanawo lingakhale litayamba chipembedzo china posachedwa chosiyana ndi chimene khololo linalimo kale. Mwina chipembedzo chake chatsopanocho chingakhale chothandiza pa moyo wa khololo ndiponso chofunika kwambiri kwa ilo koma chosadziŵika kwa anawo. Choncho, pakubukanso funso lina, Kodi khoti lingaletse khololo kuti lisamapite ndi ana kumapemphero a chipembedzocho chabe chifukwa chakuti chili chosiyana ndi chipembedzo chimene makolowo analimo poyamba?

Mafunso ameneŵa ngovuta kwambiri. Amafuna kuti woweruzayo asamangolingalira za zofunika kwa mwanayo komanso zimene zingawakhalire bwino makolowo ndi ufulu wawo.

Ufulu Wofunika Kwambiri wa Makolo ndi Ana

Nzoona kuti oweruza angalole malingaliro awoawo pa chipembedzo kuwalamulira. Koma m’maiko ambiri sikuti ufulu wa chipembedzo wa makolo kapena wa mwana unganyalanyazidwe ayi. Maiko ameneŵa angakhale ndi malamulo amene samalola woweruza kulanda makolo ufulu wofunika kwambiri wosamalira kakulidwe ka mwana wawo, kuphatikizapo maphunziro akusukulu ndi achipembedzo a mwanayo.

Mwananso ali ndi ufulu wolandira maphunziro oterowo kwa makolo ake. Woweruza asanachite kalikonse mwalamulo ponena za malangizo achipembedzo a mwana, khoti liyenera kumva umboni wokhutiritsa wakuti “mapembedzedwe a chipembedzo china angavulaze mwanayo mwamsanga ndiponso koopsa.” (Kanyenye ngwathu.) Kungosiyana zipembedzo kapena kukangana kwa makolo pa za chipembedzo sizokwanira kuti Boma liloŵerepo.

Ku Nebraska, U.S.A., nzeru imene mayi wina amene ali mmodzi wa Mboni za Yehova anasonyeza pamlandu wa amene ayenera kusunga ana imasonyeza mmene malamulo ameneŵa amatetezera onse makolo ndi ana omwe. Tate wosakhala Mboniyo sanafune kuti mwana wawo wamkazi azipita kumapemphero a Mboni za Yehova ku Nyumba ya Ufumu. Khoti laling’ono linavomerezana ndi tateyo.

Kenako mayiyo anachita apilo ku Bwalo Lapamwamba la Nebraska. Mayiyo anatsutsa kuti panalibe umboni wakuti zochita za Mboni za Yehova zingawononge ubwino wa mwana mwamsanga ndiponso koopsa. Mayiyo ananena “kuti kupezeka pa zochitika za chipembedzo cha makolo ndi kutengamo mbali . . . kudzapatsa mwana maziko osankhira chipembedzo chimene angakonde atafika pamsinkhu woti nkumvetsetsa zinthu.”

Bwalo lalikululo linasintha chigamulo cha bwalo laling’ono niligamula kuti “bwalo [laling’ono] linalakwa kuika ziletso pa ufulu wa mayiyo wolera mwanayo m’maleredwe a chipembedzo chake.” Panalibiretu umboni wakuti kupezeka pa mapemphero pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kunasokoneza mwanayo.

Ufulu wa Makolo Amene Ali Osayenera Kusunga Ana

Nthaŵi zina, makolo osudzulana amayesa kugwiritsira ntchito mikangano yokhudza maleredwe a m’chipembedzo ncholinga choti atenge ana aziwalera ndiwo. Mwachitsanzo, pamlandu wa Khalsa v. Khalsa m’boma la New Mexico, U.S.A., makolowo anali m’chipembedzo cha Asiki adakali okwatirana. Koma sipanapite nthaŵi atasudzulana pamene mayiyo anakhala Mkatolika nayamba kuletsa ana kutsata Chisiki.

Tateyo anakwiya ndipo anapereka nkhaniyo kubwalo la milandu pofuna kuti akhale ndi ulamuliro waukulu wolera ana m’maleredwe a chipembedzo chake cha Asiki. Kodi bwalo lozenga mlanduwo linatani nalo pempholo? Linamkanira. Bwalo lozenga mlandulo linatero kuti “pamene ana anali kwa [iye], iwo mwaufulu kapena mokakamiza sanali kutengamo mbali m’zochita zilizonse za Asiki, kuphatikizapo zochita zilizonse za tchalitchi, kupita nawo kukampu ya Asiki kapena kusukulu za mkaka za Asiki.”

Tateyo anachita apilo ku New Mexico Court of Appeals. Bwalo lalikulu limeneli linavomerezana ndi tateyo nilisintha chigamulo choperekedwa ndi bwalo lozenga mlandu. Bwalo la apilo linati: “Mabwalo ayenera kutsatira lamulo la kusakondera zipembedzo, ndipo ayenera kuloŵapo pankhani zimenezi zovuta ndipo zotetezereka ndi lamulo kokha pamene pali umboni womveka ndi wosatsutsika wosonyeza kuti zingasokoneze ana. Ziletso pankhani ngati zimenezi zimabweretsa ngozi yoti ziletso za bwalozo mosayenera nkupondereza ufulu wa kulambira wa makolo kapena zingaoneke kuti zikutero.”

Chigamulo chimenecho chikugwirizana ndi malamulo ambiri amene ali odziŵika m’maiko ambiri. Kholo lanzeru lidzalingalira malamulo ameneŵa. Ndiponso, kholo lachikristu lidzalingalira bwinobwino zakuti mwana afunikira kuchita zinthu limodzi ndi makolo aŵiriwo, limodzinso ndi kuti ayenera kulemekeza makolo aŵiriwo.—Aefeso 6:1-3.

Kukambirana Loya Alipo Kunja kwa Bwalo la Milandu

Ngakhale kuti kukambirana loya alipo kunja kwa bwalo kungakhale kosaloŵetsamo zambiri mosiyana ndi kukambirana pamaso pa woweruza, kholo lisakuone ngati nkhani wamba. Mapangano alionse ochitika iwo atamvana kapena zinthu zimene agamula pankhani ya woyenera kusunga mwana imeneyo zingakhale ndi mphamvu patakhala zikalata za kubwalo la milandu. Choncho, kungakhale bwino kuti kholo lifunse loya wa zabanja wodziŵa zambiri kuti litsimikize kuti nkhani zonse zokhudzana ndi woyenera kusunga ana zikusamalidwa bwino ndipo mosakondera.

Kholo lililonse liyenera kukhala ndi nthaŵi yokonzekera kukambirana. Khalidwe la kholo pakukambiranako lingakhudze kwambiri zotsatira zake. Kaŵirikaŵiri, makolo osudzulana amasokonezeka nzeru ndi chisudzulo koti amaiŵala zinthu zofunika kwambiri: Kodi chingamkomere mwana nchiyani? Kodi mwana akufunikiranji kuti akule bwino m’nzeru, m’mtima, ndi kuthupi?

Kumbukirani kuti m’zamalamulo, chofunika kwambiri pokambirana loya alipo, si kusiyana zipembedzo kapena maganizo pa zinthu zina, koma mmene makolo angapezere maziko ogwirizaniranapo ndi kuchitirana pangano kuti ana ziwakhalire bwino. Mwina kholo lidzaona kuti padzakhalabe kukondera chipembedzo kapena zina zilizonse, adzalifunsa mafunso osayembekezera, kapena zochitika zina zimene cholinga chake ndicho kuliputa kapena kulisokoneza. Zolakwa za kholo lililonse zingavumbulidwe ngakhale kukokomezedwa. Komabe, pamene okhudzidwawo akhala ololerana, angafikire pa kumvana.

Nthaŵi zina, kukambirana loya alipo kungaoneke ngati kukutenga nthaŵi ndipo kotopetsa. Njira ina ndiyo bwalo kuloŵapo limodzinso ndi mbiri yake yonyazitsa, vuto la ndalama, ndi kuvutitsa mwana. Kulibe amene angafune zimenezo. Monga mavuto ena onse aakulu m’moyo, kholo lachikristu liyenera kuona kukambiranako mwapemphero, likumakumbukira chiitano chouziridwa cha ‘kupereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso Iye, adzachichita.’—Salmo 37:5.

Nanga bwanji ngati njira yothetsera vutolo siikupezeka ndipo woweruza wagamula kuti kholo linalo liyenera kusunga mwana? Kapena bwanji ngati mmodzi pa makolo osudzulanawo ali wochotsedwa mumpingo wachikristu? Ndiponso, kodi aliyense wa iwo ayenera kuganiza bwanji ngati onse aŵiri kapena mmodzi ali woyenera kusunga ana? Kuti tithandize makolo kuchita monga mwa nzeru yaumulungu pamene zinthu zikuvuta kwambiri, mafunso ameneŵa ndi mapulinsipulo a Baibulo okhudzana nawo adzafotokozedwa m’nkhani yotsatira.

[Bokosi patsamba 24]

Mikhalidwe Itatu Yofunika Kwambiri

Woweruza m’khoti pankhani za banja amene anafunsidwa ndi Galamukani! anatero kuti mikhalidwe ina yofunika kwambiri imene amafuna kuona mwa kholo imaphatikizapo itatu yotsatirayi:

Kulolera—kukhala wofunitsitsa kulola kholo linalo kuti lizionana naye mwana (ngati silingavulaze mwanayo kapena kuwononga khalidwe lake)

Kuzindikira—kudziŵa zimene mtima wa mwana ufuna

Kudziletsa—moyo wabwino panyumba umene ungalimbikitse mkhalidwe wabata umene mwana angakuliremo bwino

[Bokosi patsamba 24]

Malangizo kwa Oweruza

Mwa kukhala ndi malangizo, oweruza ena atha kupewa mikangano yosayenera yokhudza zikhulupiriro za chipembedzo cha kholo. Mwachitsanzo:

1. Unansi wabwino uyenera kukhalapo pakati pa mwana ndi makolo onse aŵiri. Woweruza John Sopinka wa Bwalo Lapamwamba la Canada anatero kuti kholo lililonse liyenera kuloledwa “kuchita zinthu zimene zimalithandiza kusonyeza khalidwe lake lenileni [kuphatikizapo mapembedzedwe ake]. Kholo limene lili ndi ufulu wocheza ndi mwana siliyenera kunamizira kuti lili ndi khalidwe limene lilibe pamene likucheza ndi mwanayo.”

2. Kuletsa kholo lokhala ndi ufulu wocheza ndi mwana kuti lisamamphunzitse za chipembedzo chake ndiko kupondereza ufulu wa kupembedza wa khololo, kusiyapo ngati pali umboni wosatsutsika wakuti zimenezo zingawononge koopsa mwanayo.

[Chithunzi patsamba 25]

Oweruza amakhala ndi ntchito yaikulu pamilandu ya woyenera kusunga ana

[Chithunzi patsamba 26]

Loya angathandize makolo kuthetsa mikangano popanda kuzenga mlandu m’bwalo kumene kumataya nthaŵi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena