Lingaliro la Baibulo
Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani?
“OTSATIRA DARWIN AMANENETSA KUTI KUSANKHA KWA CHIBADWA NDIKO NJIRA YOKHA YOKWANIRA YOFOTOKOZERA CHIYAMBI CHA ZAMOYO. KOMA KUMAONEKA KWANZERU KUNENA KUTI, NGATI CHAMOYO CHIKULA KUKHALA CHOCHOLOŴANA KWAMBIRI, CHODZIDZIŴA BWINO KWAMBIRI NDI CHANZERU KWAMBIRI, NCHIFUKWA CHAKUTI CHIMAFUNA MIKHALIDWE IMENEYO.”—DYLAN THOMAS (1914-53, WANDAKATULO NDI MLEMBI WACHIWELSHI).
KUFUNAFUNA chifuno cha moyo si kwachilendo. Kwakhalako zaka mazana ambiri m’maganizo mwa anthu ofuna kudziŵa chifunocho. Kufufuza kwaposachedwapa kukusonyeza kuti lerolino nkhaniyo ili m’maganizo mwa anthu ambirimbiri a ku New Zealand kuposa ndi zaka khumi zapitazo. Anthu okwanira 49 peresenti, azaka 15 ndi kuposapo, ikutero nkhani yofalitsidwa mu Listener, “anaganiza za chifuno cha moyo kaŵirikaŵiri,” kumene kuli kuwonjezeka kuchoka pa 32 peresenti amene anapezeka pamene kufufuza kwina kofanana ndi kumeneku kunachitidwa mu 1985.
Anthu a ku New Zealand akuchita ngati kuti akusonyeza malingaliro amene anthu akumaiko ena ali nawo. Listener ikupitiriza: “Kuwonjezeka kwa anthu okayikira tanthauzo la kukhalapo kwathu kungakhale kukusonyeza kuti tsopano tili ndi nkhaŵa yaikulu kuposa imene tinali nayo m’ma [19]80, osadziŵa kumene tikupita.”
Mwachionekere, mayankho operekedwa ndi akatswiri a chisinthiko pa funso la onse limenelo lakuti, Kodi nchifukwa ninji tili ndi moyo? samakhutiritsa anthu ambirimbiri. Kodi Baibulo lingapereke kampasi ya makhalidwe yofunikira kupezera chifuno cha moyo wa munthu?
“Mphamvu Yaikulu Yosonkhezera”
Pa zolengedwa zonse za pa dziko lapansi, munthu yekha ndiye amene amasinkhasinkha za chifuno cha moyo. Kodi mukudziŵa chifukwa chake? Baibulo limapereka chifukwa china pa Mlaliki 3:11. Ponena za Mlengi, limati: “Iye wapatsa anthu chikumbumtima cha nthaŵi yakale ndi yamtsogolo.” (The New English Bible) Ngakhale kuti zamoyo zonse zimakonda moyo, munthu ali wosiyana chifukwa chakuti amalingalira za nthaŵi—yakale, yalero, ndi yamtsogolo. Munthu amasinkhasinkha zakale ndi kuyembekezera za mtsogolo, kuzikonzekera, inde, ngakhale kufunitsitsa kudzapezekako. Ndipo amagwiritsidwa mwala pamene walephera kupeza zonulirapo zake za mtsogolo chifukwa cha kufupika kwa moyo wake.
Nchifukwa chake, munthu yekha ndiye amafunsa mafunso akuti, Kodi nchifukwa ninji ndili ndi moyo? Kodi ndikupita kuti? Katswiri wa nthenda za maganizo Viktor Frankl analemba kuti: “Kuyesayesa kupeza chifuno cha moyo wa munthu ndiko mphamvu yaikulu yosonkhezera munthu. . . . Palibe nchimodzi chomwe m’dziko, ndikunenetsa, chimene chingathandize kwambiri munthu kupulumuka ngakhale pa mikhalidwe yoipitsitsa, mofanana ndi kudziŵa kuti moyo wa munthu uli ndi chifuno.”
Zimene Solomo Anapeza Yesu Anazitsimikiza
Chikhumbo cha kupeza chifuno cha moyo chinakopa anthu akale. Tiyeni tipende zochitika m’mbiri kalelo zaka zikwi zitatu zapitazo mu ufumu wa Israyeli wolamuliridwa ndi Solomo. Za iye, Mfumukazi ya Seba inati: “Idali yoonadi mbiri ija ndinaimva ine kudziko langa ya machitidwe anu ndi nzeru zanu. Koma sindinakhulupira mawu amenewo mpaka ndafika ine kuno, ndaona ndi maso anga; ndipo taonani, anangondiuza dera lina lokha; nzeru zanu ndi zokoma zanu zakula pa mbiri ndinaimvayo.”—1 Mafumu 10:6, 7.
Polemba buku la Baibulo la Mlaliki, Mfumu Solomo anauza oŵerenga ake zotulukapo za kuyesayesa kwake kumene anachita kuti asonyeze chifuno cha moyo. Anayesa kupeza nthaŵi ya kusangalala ndi moyo imene inayenerera mfumu ya Kummaŵa m’nthaŵi yamakedzana. M’chaputala 2, mavesi 1-10, anaufotokoza bwino moyo wokondweretsa umene munthu sangauganizire nkomwe lerolino. Iye anayesa kuchita zonse zimene moyo unamlola pankhani ya chuma ndi zokondweretsa thupi. Kodi ndi phindu lotani limene anapeza m’zinthu zimenezo? Odzitama ayenera kudabwa nalo yankho lake.
Pamene anayang’ana pa zinthu zonsezo, iye kaŵirikaŵiri sanakondwere nazo. Zinali zopanda pake, zotayitsa nthaŵi. Analemba kuti: “Pamenepo ndinayang’ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasauka pozigwira; ndipo taona, zonse zinali zachabechabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno.”—Mlaliki 2:11.
Iye, makamaka, anati zokondweretsa za pa dziko lapansi zimangodzetsa chikondwerero cha kanthaŵi. Ngakhale nzeru yaumunthu yomwe singamlanditse munthu ku zopweteka ndi nsautso ya moyo.
Nayenso Yesu Kristu ananena zofanana pamene, poyankha munthu wina woda nkhaŵa ya choloŵa cha chuma, anati kwa khamu lomwe linali kumvetsera: “Yang’anirani, mudzisungire kupeŵa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.”—Luka 12:15.
Yehova Mulungu yekha ndiye angathetse kuphophonya kwa anthu m’moyo wa tsiku ndi tsiku ndi kuchititsa zochita za munthu kukhala ndi chifuno chanzeru. Motero, moyo wopanda Mulungu ngwopanda pake. Monga momwe kwalembedwera pa Mlaliki 12:13, Solomo anafotokoza kuti: “Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”
Kupeza Chifuno cha Moyo
Lingaliro la Solomo lakuti chifuno cha moyo sichingalekanitsidwe ndi kuwopa Mulungu koyenera linatsimikizidwa mobwerezabwereza ndi Yesu Kristu. “Kwalembedwa,” Yesu anatero, akumagwira Mawu a Mulungu, “Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4; Deuteronomo 8:3) Inde, kuti moyo wa munthu ukhale wokhutiritsa, zinthu zauzimu siziyenera kunyalanyazidwa. Yesu ananenanso za iye mwini: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha iye amene anandituma ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yohane 4:34) Kutumikira Atate wake wakumwamba momvera kunampatsa chimwemwe ndi chikhutiro. Kunamlimbitsa. Kunachititsa moyo wake kukhala ndi chifuno.
Chotero, kodi chifuno chenicheni cha moyo chingakhalepo popanda Mulungu? Iyayi! Nzokondweretsa kuti wolemba mbiri Arnold Toynbee panthaŵi ina analemba kuti: “Chifuno chenicheni cha chipembedzo chapamwamba ndicho kufalitsa uphungu wauzimu ndi choonadi zimene zili mikhalidwe yake kwa miyoyo yambiri imene chingapeze, kuti uliwonse wa miyoyo imeneyi ungathe kupeza chifukwa chenicheni cha kukhalapo kwa Munthu. Chifukwa chenicheni cha kukhalapo kwa Munthu ndicho kulemekeza Mulungu ndi kukhala Naye kosatha.” Mneneri Malaki anatchula lingaliro la Mulungu: “Mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.”—Malaki 3:18.
[Chithunzi patsamba 29]
“The Thinker,” wojambulidwa ndi Rodinr
[Mawu a Chithunzi]
Scala/Art Resource, N.Y.