Kuneneratu za Mapeto a Dziko
“Kwa zaka zikwi zambiri aneneri amdima akhala akunenera kuti dziko linali pafupi kutha.”—Premonitions: A Leap Into the Future.
MU 1033, patangopita zaka 1,000 kuchokera pa imfa ya Kristu, nzika za Burgundy, France, zinali ndi mantha aakulu chifukwa chakuti kunanenedwa kuti dziko lidzatha chaka chimenecho. Mantha a chiwonongeko anakula pamene kunachitika mikuntho yachilendo yambiri yowononga ndi pamene kunagwa njala yowopsa. Makamu aakulu anasonyeza poyera kulapa kwawo.
Zaka makumi angapo zimenezo zisanachitike, pamene zaka chikwi kuchokera pa kubadwa kwa Kristu zinayandikira (malinga ndi kuŵerengera zaka kovomerezedwa panthaŵiyo), ambiri anakhulupirira kuti mapeto a dziko anali pafupi. Ntchito yojambula zinthu ndi madzoma m’nyumba za agulupa ku Ulaya akuti zinatsala pang’ono kuima. Eric Russell anati m’buku lake lakuti Astrology and Prediction: “Mawu amene anafala kwambiri m’zikalata za chuma chamasiye mkati mwa theka lachiŵiri la zaka za zana la khumi anali akuti ‘Poona kuti mapeto a dziko tsopano ayandikira.’”
Martin Luther, amene anayambitsa Kukonzanso kwa Chiprotesitanti m’zaka za zana la 16, ananeneratu kuti mapeto a dziko anali pafupi m’tsiku lake. Malinga ndi kunena kwa buku lina, iye anati: “Ine ndikutsimikiza kuti tsiku la chiweruzo layandikira kwambiri.” Mlembi wina anafotokoza kuti: “Mwa kugwirizanitsa zochitika m’mbiri ndi maulosi a Baibulo Luther anakhoza kulengeza za kuyandikira kwa chiwonongeko chomaliza.”
M’zaka za zana la 19, William Miller, amene anthu amati ndiye anayambitsa Adventist Church, ananeneratu kuti Kristu adzabweranso pakati pa March 1843 ndi March 1844. Chotero, ena panthaŵiyo anayembekezera kutengedwa kumka kumwamba.
Posachedwapa, chipembedzo china cha ku Ukraine chotchedwa Great White Brotherhood chinaneneratu kuti dziko lidzatha pa November 14, 1993. Ku United States of America mlaliki wapawailesi, Harold Camping, anati mapeto a dziko azadza m’September 1994. Mwachionekere, kuneneratu madeti a mapeto a dziko kumeneku kwakhala kolakwika.
Kodi zimenezi zachititsa anthu kusakhulupiriranso kuti dziko lidzatha? Kutalitali. “Kuyandikira kwa zaka chikwi zina m’chaka cha 2000,” inatero U.S.News and World Report ya December 19, 1994, “kukuchititsa maulosi ambirimbiri a tsiku la chiwonongeko.” Magaziniwo anasimba kuti “Amereka pafupifupi 60 peresenti amaganiza kuti dziko lidzatha tsiku lina mtsogolo; mwa amenewo pafupifupi mmodzi mwa atatu alionse amaganiza kuti lidzatha patapita zaka makumi oŵerengeka.”
Kodi nchifukwa ninji pakhala kuneneratu kochuluka motere kwa mapeto a dziko? Kodi pali chifukwa chomveka chokhulupirira kuti lidzatha?