Kodi Nchifukwa Ninji Pali Machenjezo Abodza Ambiri?
Mapeto a Dziko—Kodi Ali Pafupi Motani?
NTHANO ya mnyamata yemwe ankaŵeta nkhosa za anthu a m’mudzi imasimbidwa kaŵirikaŵiri. Pofuna kudzutsa nthumanzi, tsiku lina iye anafuula kuti, “Mmbulu! Mmbulu!” pamene kunalibe mmbulu. Anthu a m’mudzimo anathamangirako zibonga zili m’manja kuti akapitikitse mmbuluwo, koma anapeza kulibe. Zidamsangalatsa kwambiri kwakuti pambuyo pake mnyamatayo anabwereza mfuu yake. Kachiŵirinso anthu a m’mudziwo anathamangirako ndi zibonga zawo, nangopeza kuti linali chenjezo lina labodza. Pambuyo pake mmbulu unafikadi, ndipo mnyamatayo anafuula, “Mmbulu! Mmbulu!” koma anthu a m’mudziwo ananyalanyaza mfuu yake kukhala chenjezo lina labodza. Iwo ananyengedwa kunakwanira.
Ndimo mmene zakhalira ndi anthu amene amalengeza za mapeto a dziko. Kwa zaka mazana ambiri kuyambira m’tsiku la Yesu, maulosi ambiri osakwaniritsidwa aperekedwa kotero kuti ambiri samawakhulupiriranso.
Gregory I, yemwe anali papa kuyambira 590 mpaka 604 C.E., m’kalata yopita kwa wolamulira wa ku Ulaya, anati: “Tifuna kuti Inu Wolemekezeka mudziŵe, monga momwe taphunzirira m’mawu a Mulungu Wamphamvuyonse m’Malemba Opatulika, kuti mapeto a dziko lilipoli ali pafupi ndi kuti Ufumu wosatha wa Oyera Mtima ukuyandikira.”
M’zaka za zana la 16, Martin Luther, myambitsi wa Tchalitchi cha Lutheran, analosera kuti mapeto anali pafupi. Malinga ndi kunena kwa buku lina, iye anati: “Pa ine ndekha, ndine wotsimikizira kuti tsiku la chiweruzo lili pafupi kwenikweni.”
Ponena za limodzi la magulu oyambirira a Baptist, kwasimbidwa kuti: “Anabaptist a m’Zaka za Zana Lakhumi ndi Chisanu ndi Chimodzi anakhulupirira kuti Kulamulira kwa Zaka Chikwi kukafika mu 1533.”
“Edwin Sandys (1519-1588), Akibishopu wa ku York ndi Bishopu Wamkulu wa Mangalande . . . anati, . . . ‘Tiyeni tikhale otsimikizira kuti kudza kwa Ambuye kuli pafupi.’”
William Miller, yemwe amalingaliridwa kukhala woyambitsa wa Tchalitchi cha Adventist, anagwidwa mawu kukhala akunena kuti: “Ndine wotsimikizira kotheratu kuti malinga ndi dongosolo loŵerengera nthaŵi Lachiyuda, Kristu adzafika nthaŵi iliyonse pakati pa March 21, 1843, ndi March 21, 1844.”
Molingana ndi tanthauzo la Deuteronomo 18:20-22, kodi kusakwaniritsidwa kwa maulosi amenewo kumasonyeza amene analoserawo kukhala aneneri onyenga? Lemba limenelo limati: “Mneneri wakuchita modzikuza ndi kunena mawu m’dzina langa, amene sindinamlamulira anene, kapena kunena m’dzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe. Ndipo mukati m’mtima mwanu, Tidzazindikira bwanji mawu amene Yehova sananena? Mneneri akanena m’dzina la Yehova, koma mawu adanenawa sachitika, nisafika, ndiwo mawu Yehova sanawanena.”
Pali ena amene amapereka maulosi odziwonetsera a mapeto a dziko kuti akope chidwi ndi kupeza otsatira, koma ena amakhulupiriradi kuti zilengezo zawo nzowona. Iwo akulankhula za ziyembekezo zozikidwa pa kumasulira kwawo kwa malemba ena kapena zochitika zakuthupi. Iwo samanena kuti maulosi awo ali zivumbulutso zachindunji zochokera kwa Yehova ndi kuti mwanjira imeneyi akulosera m’dzina la Yehova. Chifukwa chake, m’zochitika zoterozo, pamene mawu awo sachitika, iwo sayenera kuwonedwa monga aneneri onyenga monga awo amene tachenjezedwa za iwo pa Deuteronomo 18:20-22. M’kulakwa kwawo kwaumunthu, iwo anamasulira molakwa zinthu zina.a
Mosalefulidwa ndi zolephera zakale, anthu ena akopeka mtima ndi kuyandikira kwa chaka cha 2000 ndipo apereka maulosi ena a mapeto a dziko. The Wall Street Journal ya pa December 5, 1989, inafalitsa nkhani yokhala ndi mutu wakuti “Millennium Fever: Prophets Proliferate, the End Is Near.” (Nthumanzi ya Zaka Chikwi: Aneneri Akuwonjezereka, Mapeto Ali Pafupi.) Ndi kuyandikira kwa chaka cha 2000, alengezi ambiri akulosera kuti Yesu akubwera ndi kuti ma 1990 adzakhala “nthaŵi ya mavuto omwe sanawonedwepo.” Panthaŵi imene nkhaniyi inkalembedwa, zochitika zatsopano zinali ku Lipabuliki la Korea, kumene Mission for the Coming Days inalosera kuti pa October 28, 1992, pakati pausiku, Kristu adzafika ndi kutengera okhulupirira kumwamba. Magulu ena angapo olalikira tsiku lachiweruzo apereka maulosi ofananawo.
Unyinji wa machenjezo abodza ngwomvetsa chisoni. Ngwofanana ndi mfuu yakuti mmbulu, mmbulu ya mbusa uja—anthu amawanyalanyaza mwamsanga, ndipo pamene chenjezo lowona lifikadi, nalonso limanyalanyazidwa.
Koma kodi nchifukwa ninji pakhala chikhoterero choterocho chopereka machenjezo abodza kwa zaka mazana onsewa kufikira tsiku lathu, monga momwe Yesu ananenera kuti zikakhala tero? (Mateyu 24:23-26) Pambuyo pouza otsatira ake za zinthu zosiyanasiyana zimene zikazindikiritsa kubweranso kwake, Yesu anawauza zimene timaŵerenga pa Mateyu 24:36-42 kuti: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha. Ndipo monga masiku a Nowa, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa munthu. . . . Chifukwa chake dikirani, pakuti simudziŵa tsiku lake lakufika Ambuye wanu.”
Iwo anauzidwa osati kungodikira kokha ndi kukonzekera komanso kudikira mwachidwi. Aroma 8:19 amati: “Pakuti chiyembekezetso cha cholengedwa chilindira vumbulutso la ana a Mulungu.” Chibadwa cha anthu nchakuti ngati tikuyembekezera mwakhama ndi kulakalaka chinachake, timakhala ndi chisonkhezero champhamvu chofuna kuchiwona chili pakhomo ngakhale ngati umboniwo ngwosakwanira. M’kulakalaka kwathuko, machenjezo abodza angaperekedwe.
Pamenepo, kodi nchiyani chimene chidzasiyanitsa machenjezo owona ndi abodza? Kuti mupeze yankho, chonde onani nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a M’kulakalaka kwawo kubweranso kwa Yesu, Mboni za Yehova zinapereka madeti amene sanali olondola. Chifukwa cha zimenezi, ena amawatcha aneneri onyenga. Komabe, palibe mpamodzi pomwe m’zochitika zimenezi pamene ananena kuti maulosi amenewo anawanena ‘m’dzina la Yehova.’ Iwo sananene konse kuti, ‘Awa ndimawu a Yehova.’ Nsanja ya Olonda, magazini alamulo a Mboni za Yehova, inanena kuti: “Tilibe mphatso ya kunenera.” (January 1883, tsamba 425) “Ndiponso sitidzalola kuti zolembedwa zathu zilambiridwe kapena kulingaliridwa kukhala zosalakwa.” (December 15, 1896, tsamba 306) Nsanja ya Olonda inanenanso kuti chenicheni chakuti ena ali ndi mzimu wa Yehova “sichimatanthauza kuti amene akutumikira tsopano monga mboni za Yehova ali ouziridwa. Sizimatanthauza kuti zolembedwa m’magazini ano a Nsanja ya Olonda nzouziridwa ndi zosalakwa ndi zopanda zophophonya.” (May 15, 1947, tsamba 157) “Nsanja ya Olonda simanena kuti ndimawu ouziridwa, ndiponso siili yaukumu.” (August 15, 1950, tsamba 263) “Abale amene amakonza mabuku ameneŵa sali osakhoza kulakwa. Zolemba zawo sizili zouziridwa mofanana ndi zija za Paulo ndi olemba Baibulo ena. (2 Tim. 3:16) Ndipo chotero, nthaŵi zina, kwakhala kofunika kuwongolera malingaliro ena, pamene chowonadi chinamvekera. (Miy. 4:18)”—February 15, 1981, tsamba 19.