Apambana Nkhondo Yolimbana ndi Masoka
ZOYESAYESA za United Nations ndi za boma lililonse palokha za kuchepetsa zotulukapo za masoka achilengedwe zilidi zoyamikirika. Mapulojekiti onga International Decade for Natural Disaster Reduction amasonyeza kuti anthu safunikira kukhala osoŵa chochita atakumana ndi masoka otero. Ngati munthu payekha, magulu a anthu, ndi maboma atsatira njira zoyenera, akhoza kupulumutsa miyoyo.
Zimenezi nzosangalatsa, chifukwa Baibulo limatiuza kuti posachedwapa padzakhala kusintha kwa boma loyang’anira anthu. Chiyambire masiku a Yesu, Akristu apemphera Pemphero la Ambuye (la “Atate Wathu”), limene limaphatikizapo mawu akuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Ufumu wa Mulungu uli boma lenileni. Malinga ndi kunena kwa ulosi wa Baibulo, posachedwapa “udzaphwanya ndi kutha maufumu [aumunthu] onse. Nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Talingalirani anthu onse akukhala pansi pa boma limodzi langwiro. Kumeneko kudzakhala kusintha kotani nanga!
Ngati maboma alipowa amaona kufunika kwake kwa kuchitapo kanthu kuti ngozi zachilengedwe zisakhale masoka achilengedwe, tiyenera kukhala ndi chidaliro chakuti boma la Mulungu lidzatsimikizira kuti anthu ake asavutike mwa njira imeneyi. Ufumu wa Mulungu udzadzetsa mtendere wachikhalire pa pulaneti lino kwa nthaŵi yoyamba chiyambire pamene Kaini anapha Abele. Mu Ufumu umenewo, “ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:11) Ufumuwo udzaphunzitsa anthu kwakuti m’lingaliro lenileni ‘anthu onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova, ndipo mtendere wawo udzakhala waukulu.’—Yesaya 54:13.
Lerolino, anthu ochuluka amene masoka achilengedwe amawagwera ndiwo amphaŵi. Komabe, pokhala ndi uyang’aniro wangwiro ndi maphunziro oyenera mu Ufumu wa Mulungu, anthu sadzasauka ndi umphaŵi. Poneneratu za mikhalidwe yotero mwanjira imene anthu a m’tsiku lake anakhoza kumva, mneneri Yesaya analemba kuti: “Yehova wamakamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.” (Yesaya 25:6) Inde, phwando la zinthu zabwino! Pofotokoza zowonjezereka ponena za moyo mu ulamuliro wa Ufumuwo, wamasalmo analemba kuti: “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa, ngati za ku Lebano: ndipo iwo a m’mudzi adzaphuka ngati msipu wapansi.”—Salmo 72:16.
Mwachionekere, nkhondo ya munthu ndi masoka achilengedwe idzatha. Motsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu ndiponso pokhala ndi uyang’aniro wa Ufumu wa Mulungu, anthu owopa Mulungu adzakhala atapambana nkhondoyo. Umenewo udzakhala mpumulo wotani nanga!