Khungu la mu Mtsinje Kugonjetsa Mliri Wowopsawo
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU NIGERIA
MKHALIDWE weniweni wa malowo unalidi wa midzi yambiri ya m’mbali mwa mtsinje ku West Africa. Kagulu kena ka anthu kanakhala potero pa mabenchi pansi pa mtengo wina waukulu umene mthunzi wake unawatetezera ku dzuŵa lotentha kwambiri. Asanu a iwo—amuna anayi ndi mkazi mmodzi—anali akhungu kotheratu.
“Sanadziŵe chimene chinawachititsa kukhala akhungu m’mudzi wakalewo,” inatero mfumu ina ya m’mudzi, imene inavala mkanjo woyera wotaya thupi. “Ambiri a anthu okalamba kumeneko anamwalira ali akhungu. . . . Anaganiza kuti mzimu wina woipa unawakwiyira. Anapembedzera zithumwa zawo kuti ziwatetezere. Mizimu ya makolo awo inawauza kuti apereke chakudya ku zithumwazo. Chotero anapha nkhuku ndi nkhosa monga nsembe. Komabe anangopitiriza kuchita khungu.”
Potsirizira pake, madokotala anafika ndi kufotokoza kuti khungulo silinachititsidwe ndi mizimu. Linakhalapo chifukwa cha nthenda yotchedwa onchocerciasis, kapena kuti khungu la mu mtsinje, lopatsidwa dzinalo chifukwa chakuti tintchentche toluma timene timaiwanditsa timaikira mazira ake m’mitsinje ya madzi othamanga.
Mwaŵi wake ngwakuti, khungu la mu mtsinje silimagwira munthu mwawamba monga mmene zilili nthenda zina za m’maiko otentha. Silili lowopsa kwa anthu okhala m’mizinda kapenanso kwa awo amene amafika kudera lake. Khungulo limachitika kokha pamene munthu alumidwa kwa zaka zambiri.
Komabe, khungu la mu mtsinje lili nthenda yowopsa ya m’maiko otentha, imene imapha anthu ambirimbiri. Pamene kuli kwakuti imasakaza m’madera ena a ku Middle East ndi ku Central ndi South America, ogwidwa nayo koposa ndi aja amene amagwira ntchito ndi kukhala pafupi ndi mitsinje yodzazidwa ndi ntchentchezo mu dera la equator la Afirika. M’midzi ina pafupifupi aliyense ali ndi nthendayi. Malinga ndi kuyerekezera ziŵerengero kwa The Carter Center ku Atlanta, Georgia, U.S.A., anthu pafupifupi 126 miliyoni ali pangozi yoyambukiridwa ndi nthendayo. Anthu ena 18 miliyoni ali ndi kachilombo konga nyongolotsi m’matupi mwawo kamene kamachititsa khungu la mu mtsinje. Chiŵerengero cha anthu omwe akuona pang’ono kapena ochitiratu khungu chikuyerekezeredwa kukhala chili pa miliyoni imodzi kapena mamiliyoni aŵiri.
Tsopano, mliri wa zaka mazana ambiri umenewu ukugonjetsedwa ndi zoyesayesa zogwirizana za WHO (World Health Organization) ndi magulu ena, pamodzi ndi maboma a maiko osiyanasiyana. Mosasamala kanthu za kudana ndi kupanda chiyembekezo m’mbali yaikulu ya Afirika, programu imeneyi yochepetsera kufalikira kwa nthenda ikuyenda bwino. Programuyo ikutamandidwa kukhala “chimodzi cha zipambano ndi chitukuko chachikulu m’mankhwala m’zaka za zana lino la makumi aŵiri.”
Nthenda Yowopsa
Khungu la mu mtsinje limawanditsidwa ndi mitundu ingapo ya ntchentche zazikazi zakuda (gulu la Simulium). Pamene ntchentche ya nthendayo iluma munthu, imasiya mbozi ya kachilombo konga nyongolotsi (Onchocerca volvulus). Pang’ono ndi pang’ono, ili m’khungu la anthu olumidwawo, mboziyo imakhwima ndi kukula kukhala nyongolotsi zotalika masentimita 60.
Itakhala ndi mazira, nyongolotsi yaikazi iliyonse imayamba kubala tinyongolotsi totchedwa microfilariae; zimapitiriza kuchita zimenezi kwa zaka 8 kufikira 12, zikumabala zambirimbiri. Ma microfilariae samakula kusiyapo ngati atengedwa ndi ntchentche zakuda, ndi kukulira mu ntchentchezo, ndi kuwabwezeranso mwa munthu. Nyongolotsi zazing’onozing’ono zimenezi, kwakukulukulu zimayendayenda m’khungu monse ndipo potsirizira pake zimaloŵa m’maso. Nyongolotsi zambiri zofika 200 miliyoni zingaunjikane mwa wodwala mmodzi. Zimakhala zambiri kwakuti opima amangodula tinyama ta khungu kuti apime. Pa maikolosikopo, tinyamato timasonyeza kuti tili ndi tinyongolotsi tambirimbiri tating’ono kwambiri tochita nyakatunyakatu.
Tizilombo timeneti timasautsa odwalawo. M’kupita kwa zaka khungu la munthu wolumidwayo limatupatupa ndi kukhala ndi mamba. Kaŵirikaŵiri maŵanga otumbuluka amaonekera. Odwalawo amayamba kukhala ndi khungu limene pooneka limanga ngati la ng’ona, khungu la buluzi, kapena khungu la nyalugwe. Kuyabwa kwake nkwakukulu, kwasimbidwa kuti kumachititsa ena kudzipha. M’kupita kwa nthaŵi, ngati nyongolotsi zazing’onozo ziloŵa m’maso, kuona kumayamba kuchepa, ndipo wodwalayo amadzakhala wakhungu kotheratu.
M’madera osauka akumidzi, kumene ntchentche zakuda zili zofala, khungu lili chinthu chovuta kwambiri kupirira nacho. Chifukwa chimodzi nchakuti anthu akumidzi ambiri amakhulupirira mwamwambo kuti khungulo ndi chilango cha Mulungu ndi kuti anthu akhungu ali opanda pake m’midzi yawo. Chifukwa china nchakuti palibe thandizo la kuboma, zikumapangitsa odwalawo kudalira kotheratu pa mabanja awo. Sata, mkazi wina wodwala khungu la mu mtsinje ku Burkina Faso, anati: “Kwa munthu wakhungu, kaya akhale mwamuna kapena mkazi, kuvutika kwake nkofanana. Ngati mtsikana ali wakhungu ndi wosakwatiwa, sadzapeza mwamuna. Ndinakwatiwa ndisanakhale wakhungu, komano mwamuna wanga anamwalira. Mlongo wanga anakhala wakhungu pamene anali wamng’ono ndipo sanathe kupeza mkazi. Aŵiri tonsefe timasamaliridwa ndi achibale athu—pa chakudya, pa zonse. Nzowopsa.”
M’madera amene khungu la mu mtsinje lili lofala, anthu kaŵirikaŵiri amasiya midzi yawo, ataumirizidwa ndi ntchentche ndi nthendayo kuthaŵa. Malo achondewo okhala pafupi ndi madzi amangosiyidwa ndi kukhala osalimidwa. Zimenezi nazonso, zimakulitsa umphaŵi ndi njala.
Kulimbana ndi Ntchentche Zakuda
Zoyesayesa za padziko lonse za kuchepetsa khungu la mu mtsinje ku maiko asanu ndi aŵiri a ku West Africa zinayamba kuchiyambiyambi kwa ma 1970. Pokhala okonzekera ndi biodegradable larvicides, mankhwala ophera tizilombo amene amapha mbozi, magulu a mahelekopitala, ndege zazing’ono, ndi malole anaukira ntchentche zakuda, zonyamula matendawo. Cholinga chawo chinali cha kuukira ndi kupha ntchentche zakuda pamene zili zosatetezereka kwenikweni—pamene zili mbozi.
Kunali kosayenera kuthira poizoni m’mitsinje yonse. Akatswiri anadziŵa kuti ntchentche zakuda zazikazi zimaikira mazira ake pamadzi ndi kuti mazirawo amamatirira mu nthambi ndi m’matanthwe a m’madzi othamanga. Ndi madzi othamanga kwambiri okha amene amapereka okosijeni yambiri ku mbozi zomakulazo imene imafunikira kuti zikhale ndi moyo. Zimenezi zinatanthauza kuti malo ake oswerako m’mphepete mwa mtsinje anali ochepa ndi odziŵika.
Chifuno cha kufafaza mankhwala m’madera ake oswerana sichinali cha kuthetseratu ntchentche zakuda, ntchito imene ili yosatheka. Koma mwa kuchepetsa chiŵerengero cha ntchentchezo, akatswiri anayembekezera kuti njira ya kayendedwe ka kachilombo kake idzadulidwa. Ntchentche zochepa zidzatanthauza odwala atsopano ochepa. Malinga ndi kulingalira kwawo, ngati ntchentchezo zikanaletsedwa kuikira mazira kufikira tizilombo timene tinalipo titafa mwa anthu olumidwa, pakanafika nthaŵi imene sipakanakhalanso tizilombo totsalira. Chotero, ngati ntchentche inaluma munthu, sikanatenga tizilimbo tilitonse tokaloŵetsa kwa ena.
Pulojekitiyo inali yovuta. Ntchentchezo zimaswana zambirimbiri m’malo ovuta kufikamo. Ndiponso, popeza kuti zikhoza kuuluka makilomita mazana ambiri, anafunikira kulimbana ndi ntchentche zakuda m’dera lalikulu. Ndiponso, kusamala kwapadera kunafunikira popeza akanalekerera zimenezi ngakhale kwa mwezi umodzi ntchentche zambiri zikanabukanso, zikumalepheretsa ntchito yochitidwa zaka zambiri.
Kuyambira m’ma 1970, mosankha malo, ndege zinafafaza makilomita oposa 19,000 a malo akutali a m’mitsinje. Chotero, nthendayo anaithetsa m’madera okwanira 80 peresenti a madera oyambukiridwa nayo m’maiko amene anagwirizana nawo m’zimenezi.
Mbulu Umodzi Kapena Iŵiri Kamodzi pa Chaka
Ndiyeno, kuyambira mu 1987, chida china chinakonzedwa polimbana ndi khungu la mu mtsinje. Panthaŵiyi, chinthu chimene anafuna kugonjetsa chinali tizilombo tokhala m’thupi la munthu, m’malo mwa kulimbana ndi ntchentche zakuda. Chidacho chinali mankhwala otetezereka ndi amphamvu otchedwa Mectizan (ivermectin), opangidwa m’malaboletale a kampani ina ya mankhwala ya ku America.
Kuti aletse kukula kwa nthendayo, munthu wolumidwayo afunikira kutenga mlingo umodzi wa mankhwala—mbulu umodzi kapena iŵiri—chaka chilichonse. Mectizan samapha tizilombo tatikulu tonga nyongolotsi m’thupi, koma amapha tinyongolotsi tating’ono ndipo amaletsa zazikuluzo kubala ma microfilariae owonjezereka. Zimenezi zimaimitsa kupitiriza patsogolo kwa nthendayo mwa wodwala ndipo zimachedwetsa kupatsiridwa kwa nthendayo mwa ena. Ndiponso mankhwalawo amachiritsa kutemeka kumene kukuyamba pa khungu la m’diso ndi kutetezera kukula kwa kutemeka kwina. Komabe, iwo sangakonzenso diso lakalelo, ndipo sangabwezeretse kuona pamene khungu lachitika.
Komabe, vuto linali pa kuperekedwa kwake—kupititsa mankhwalawo kwa anthu owafuna. Unyinji wa anthu okhala kumidzi yakutali ndi yapatalipatali ungangofikiridwa ndi miyendo. Kaŵirikaŵiri kugwiritsira ntchito galimoto kumafuna kuilambulira modzera kapena ngakhale kumanga milatho. Nthaŵi zina nkhondo yachiŵeniŵeni, kusoŵa ndalama, ndi ndale za m’dzikomo zimawonjezera zovuta pa kuperekedwa kwake. Komabe, mosasamala kanthu za zopinga zimenezi, podzafika kuchiyambiyambi kwa 1995 mibulu pafupifupi 31 miliyoni ya Mectizan inali itaperekedwa, makamaka mu Afirika.
Ziyembekezo za Mtsogolo
M’zaka 20 zapitazo, Onchocerciasis Control Programme yalimbana ndi khungu la mu mtsinje m’maiko 11 a ku West Africa, dera la ukulu woŵirikiza katatu dziko la France. Kodi zotulukapo zake zakhala zotani? Malinga ndi ziŵerengero za WHO, kugwiritsira ntchito pamodzi mankhwala ophera mbozi ndi Mectizan kwachita zambiri potetezera anthu oposa 30 miliyoni amene kale anali pangozi ya mliri wakalekale woopsa umenewu. Anthu oposa 1.5 miliyoni amene anayambukiridwa kwambiri ndi kachilomboko tsopano achira kotheratu. Ndiponso, kugonjetsedwa kwa khungu la mu mtsinje kukupereka kwa anthu mahekitala pafupifupi 25 miliyoni a malo okhala ndi olimamo—malo aakulu otha kudyetsa anthu 17 miliyoni pachaka.
Nkhondoyo siinathebe. Maiko a mu Afirika mmene mwamenyedwa nkhondo ya khungu la mu mtsinje ali ndi ochepera theka la anthu okhala pangozi ya nthendayo.
M’zaka zaposachedwapa zoyesayesa za kulimbana ndi nthendayo zawonjezeredwa. M’zaka ziŵiri zokha, kuyambira mu 1992 kufikira mu 1994, chiŵerengero cha anthu amene anapatsidwa Mectizan chinaŵirikiza kuposa kaŵiri, kuyambira pa 5.4 kufikira 11 miliyoni. Podzafika kumapeto kwa 1994 pafupifupi maiko 32 mu Afirika, Latin America, ndi Middle East anali atayamba kuchiritsa ndi mankhwala a Mectizan, amene m’kupita kwa nthaŵi adzatetezera anthu ambiri ofikira 24 miliyoni pa khungu.
Pan American Health Organization ikukhulupirira kuti idzathetsa nthendayo ndi kusakhalanso chinthu chowopseza anthu m’maiko onse a America podzafika chaka cha 2002. Zoonadi, mu Afirika, thayolo nlokulirapo. Komabe, United Nations Children’s Fund ikunena kuti: “Taona kale poyera kuti ponena za mbadwo umene tsopano ukukula khungu silidzakhalanso chiwopsezo chachikulu chamtsogolo monga momwe linalili m’chigawo chimene kwa nthaŵi yaitali khungu lakhala mbali yozoloŵereka ya kukalamba.”
Kudziŵa za zoyesayesa zochitidwa kuthandiza anthu okhala pangozi ya kuchita khungu kumasangalatsa mtima. Mu utumiki wake wa pa dziko lapansi, Yesu Kristu anasonyezanso nkhaŵa yachikondi kwa anthu mwa kupenyetsanso ambiri amene anali akhungu. (Mateyu 15:30, 31; 21:14) Pa mlingo wochepa, zimenezi zinasonyeza zimene zidzachitika pa dziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu. Indedi, nthaŵi ikudza pamene palibe aliyense adzakanthidwa ndi khungu la mtundu uliwonse. Mawu a Mulungu amaneneratu kuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa.”—Yesaya 35:5.
[Mawu Otsindika patsamba 11]
“Anali kuimba mlandu mizimu wa kuchititsa khungu. Tsopano, amadziŵa kuti ndi nyongolotsi”
[Mawu Otsindika patsamba 13]
Mbulu umodzi kapena iŵiri pachaka ingatetezere khungu la mu mtsinje