Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/15 tsamba 2-4
  • Muzithandiza Anthu Osaona Kudziwa za Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzithandiza Anthu Osaona Kudziwa za Yehova
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzilalikira Anthu Osaona
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Amachita Zinthu Bwinobwino Ngakhale Kuti Ndi Osaona
    Galamukani!—2015
  • Kutsegula Maso Kuti Aone Mbiri Yabwino
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani kwa Akhungu?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
km 5/15 tsamba 2-4

Muzithandiza Anthu Osaona Kudziwa za Yehova

1. Kodi Yesu anasonyeza bwanji chifundo kwa anthu osaona?

1 Tsiku lina Yesu anali pa ulendo ndipo ankachokera ku Yeriko. Pa nthawiyi n’kuti patatsala masiku ochepa kuti Yesu aphedwe. Ali pa ulendowu anakumana ndi opemphapempha awiri omwe anali osaona ndipo anayamba kumupempha mofuula kuti: “Ambuye . . . tichitireni chifundo!” N’kutheka kuti pa nthawiyi n’kuti Yesu akuganizira mayesero omwe ankayembekezera kukumana nawo. Komabe anaima n’kuitana anthu osaona aja ndipo anawachiritsa. (Mat. 20:29-34) Kodi tingatengere bwanji chitsanzo cha Yesu pa nkhani yochitira chifundo anthu osaona?

2. Kodi tingalalikire bwanji munthu wosaona yemwe takumana naye mu utumiki?

2 Muziwathandiza: Mukakumana ndi munthu wosaona muzimuuza dzina lanu n’kumupempha ngati angakonde kuti mumuthandize. Popeza nthawi zambiri anthu osaona amachitidwa chipongwe, mwina angayambe ndi kukukayikirani. Komabe ngati mutasonyeza kuti mukufuna kumuthandizadi akhoza kuyamba kumasuka n’kuvomera kuti mumuthandize. Komatu ndi bwino kukumbukira kuti matenda a khungu amakhala osiyanasiyana ndipo zimenezi zingakhudzenso thandizo lomwe angafunikire. Mukamuthandiza, mungamuuze kuti ndinu wa Mboni za Yehova ndipo mumaphunzira Baibulo ndi anthu. Mungamupemphe ngati angakonde kuti mumuwerengere lemba la Salimo 146:8 kapena la Yesaya 35:5, 6. Ngati amatha kuwerenga zilembo za anthu osaona, mungamufunse ngati angakonde kuti mudzamubweretsere buku, kabuku kapena magazini yomwe ingamuthandize kudziwa zambiri zokhudza Baibulo. Mungamupangire dawunilodi mabuku omvetsera pa webusaiti yathu ya jw.org. Ngati ali ndi kompyuta yokhala ndi pulogalamu yomwe imatha kuwerenga mawu amene akuoneka pa sikirini, mungamuuze kuti pa webusaiti yathu pali mabuku omwe angapange dawunilodi n’kumamvetsera.—Onani bokosi lakuti, “Zimene Mungachite Mukamathandiza Munthu Wosaona.”

3. Kodi tingafufuze bwanji anthu osaona m’gawo lathu?

3 Muzifufuza Anthu Osaona: Nthawi zambiri tikamalalikira kunyumba ndi nyumba, sitikumana ndi anthu osaona. Zili choncho chifukwa anthu osaona ambiri samasuka kukambirana ndi anthu osawadziwa omwe abwera kunyumba kwawo. Choncho, pamafunika khama kuti ‘tifufuze’ anthu oterewa n’cholinga choti tiwalalikire. (Mat. 10:11) Kodi pali munthu yemwe mumagwira naye ntchito kapena yemwe mumaphunzira naye amene ndi wosaona? Mungachite bwino kuyamba inuyo kuyankhula naye. Ngati m’dera lanu muli sukulu ya anthu osaona, mungapemphe akuluakulu a pasukulupo kuti muike mabuku athu a zilembo za anthu osaona mulaibulale ya pasukulupo. Kodi mukudziwa winawake yemwe ali ndi wachibale wosaona? Kapena kodi m’dera lanu muli mabungwe omwe amathandiza anthu osaona? Ngati zili choncho, mungafotokozere yemwe amayendetsa ntchito za bungwelo kapena wolandira alendo wa pamalopo kapenanso achibale a munthu wosaonayo kuti a Mboni za Yehova amathandiza anthu osaona. Mungawauzenso kuti mungathe kuwabweretsera mabuku a zilembo za anthu osaona komanso mabuku ongomvetsera. Mungawasonyezenso zimene Baibulo limanena zakuti Mulungu adzathetseratu vuto la kusaona. Ndi bwinonso kuwaonetsa vidiyo yachingelezi yomwe imapezeka pa webusaiti yathu ya jw.org yamutu wakuti, “Without It, I Would Feel Lost,” Vidiyoyi imanena za munthu wina wosaona yemwe amasangalala chifukwa choti ali ndi Baibulo la zilembo za anthu osaona. Ngati mutawafotokozera bwinobwino, zingathandize kuti akuuzeni kumene mungapeze anthu osaonawo komanso angakuloleni kuti muzicheza nawo.

4. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Janet anachita?

4 Mlongo wina wosaona, dzina lake Janet, anapita kumalo ena kumene kumakhala anthu osaona. Kumeneko anayamba kucheza ndi mayi wina wosaonanso. Janet anamuuza kuti, “Yesu anachiritsa anthu osaona pofuna kusonyeza zomwe adzachitire anthu onse osaona m’tsogolo.” Anakambirana ndi mayiyo lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 ndipo Janet anafotokoza mmene Ufumu wa Mulungu udzachitire zimenezi. Mayiyo atamva zimenezi, anadabwa kwambiri n’kunena kuti: “Sindinamvepo munthu wosaona akunena zimenezi. Anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu amakhala wosaona chifukwa cha zoipa zimene iyeyo kapena makolo ake anachita.” Patapita nthawi, Janet anatumizira mayiyu meseji yokhala ndi linki yotsegula buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Panopa amaphunzira ndi mayiyu kawiri pa mlungu.

5. Tikamasonyeza chidwi anthu osaona, kodi zotsatira zake zingakhale zotani?

5 Ifeyo sitingathe kuchiritsa anthu osaona ngati mmene Yesu ankachitira. Komabe anthu amene mulungu wa nthawi ino wachititsa khungu maganizo awo, tingawathandize kuti adziwe choonadi cha m’Mawu a Mulungu. (2 Akor. 4:4) Anthu amenewa akuphatikizapo osaona. Yesu anachiritsa anthu awiri osaona a ku Yeriko aja chifukwa choti ‘anagwidwa ndi chifundo.’ (Mat. 20:34) Ifenso tikamachitira chifundo anthu osaona, tingathe kuwathandiza kuti adziwe Yehova, yemwe m’tsogolomu adzachiritsa anthu onse osaona.

Zimene Mungachite Mukamathandiza Munthu Wosaona

  • Muziyankhula mutayang’anizana naye, koma musamakweze mawu kwambiri. Kumbukirani kuti vuto la munthuyo ndi loti saona koma amamva bwinobwino.

  • Ngati akufuna kuti mumutsogolere, pindani mkono wanu kuti akolowekepo dzanja lake. Kenako muziyenda naye pang’onopang’ono muli patsogolo pake. Mukaona chinachake chomwe chingamupunthwitse monga chitsa kapena mwala, mungachite bwino kumuuziratu.

  • Musamaope kugwiritsa ntchito mawu ngati “tionana mawa,” chifukwa nawonso amagwiritsa ntchito mawuwa. Munthu akamafotokoza za chinthu chinachake, anthu osaona amaona chinthucho m’maganizo mwawo.

  • Mungachite bwino kumacheza ndi munthu wosaona pamalo opanda phokoso. Anthu osaona samasuka kwenikweni ngati mukuyankhula nawo pamalo pomwe pakumveka phokoso losiyanasiyana chifukwa sadziwa zimene zikuchitika pamalopo.

  • Ngati mukuchoka, mungachite bwino kumuuza. Zimenezi zingathandize kuti asamapitirizebe kuyankhula poganiza kuti inuyo muli pompo.

  • Ngati munthu wosaonayo sakhala m’gawo la mpingo wanu koma akufuna kudziwa zambiri, lembani fomu ya Kaonaneni ndi Wachidwi Uyu (S-43) n’kukaipereka kwa mlembi wa mpingo wanu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena