MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kuwonjezera Luso Lathu Mu Utumiki—Muzilalikira Anthu Osaona
KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI?: Anthu ambiri osaona samasuka kulankhula ndi anthu osawadziwa. Choncho kuti tilalikire anthu amenewa timafunika kuchita zinthu mwaluso. Yehova amakonda komanso kuganizira anthu osaona. (Le 19:14) Tingatengere chitsanzo chake ngati nafenso timayesetsa kuthandiza anthu osaona kuti akhale pa ubwenzi ndi Mulungu.
KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?
“Muzifufuza anthu osaona.” (Mt 10:11) Kodi mukudziwa wina aliyense yemwe ali ndi wachibale wosaona? Kodi m’gawo lanu muli sukulu kapena bungwe limene limasunga anthu osaona omwe angakonde kumalandira mabuku athu?
Muzisonyeza kuti mumawaganizira. Anthu osaona amamasuka mukakhala aubwenzi komanso mukamasonyeza kuti mumawaganizira. Mungachite bwino kukambirana nawo nkhani zimene zingawachititse chidwi
Muziwapatsa mabuku athu. Pofuna kuthandiza anthu osaona komanso amene amavutika kuona, gulu la Yehova limatulutsa mabuku a zilembo za anthu osaona komanso zinthu zina zongomvetsera. Mungawafunse kuti angakonde kumaphunzira pogwiritsa ntchito njira iti? Woyang’anira utumiki ayenera kuonetsetsa kuti mtumiki wa mabuku akuitanitsa mabuku amene munthu wosaona akufuna.