Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 11/15 tsamba 7-9
  • Amachita Zinthu Bwinobwino Ngakhale Kuti Ndi Osaona

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Amachita Zinthu Bwinobwino Ngakhale Kuti Ndi Osaona
  • Galamukani!—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Muzithandiza Anthu Osaona Kudziwa za Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Mabuku a Zilembo za Anthu Osaona Akuthandiza Kwambiri
    Kodi Zopereka Zanu Zimagwiritsidwa Ntchito Bwanji?
  • Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzilalikira Anthu Osaona
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Kutsegula Maso Kuti Aone Mbiri Yabwino
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 11/15 tsamba 7-9
A Paqui ali ndi amuna awo

Amachita Zinthu Bwinobwino Ngakhale Kuti Ndi Osaona

Mayi wina wosaona dzina lake Paqui, yemwe mwamuna wakenso ndi wosaona, anati: “Vuto langali linayamba nditangobadwa kumene. Madokotala anandithira mankhwala amphamvu kwambiri m’maso moti kungoyambira nthawi imeneyo mpaka ndili wachinyamata, ndinkaona movutikira kwambiri. Kenako ndinasiyiratu kuona. Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe kuvutika maganizo.”

PALI zifukwa zambiri zimene zimachititsa kuti anthu aziona movutikira komanso kuti akhale osaona. Nthawi zina vutoli limayamba chifukwa cha matenda kapena chifukwa chovulala. Munthu amasiya kuona, mitsempha yotumiza zithunzi ku ubongo kapena mbali ya ubongo yomwe imathandiza kuti munthu aziona ikawonongeka. Anthu ambiri amene amavutika kuona komanso amene saoneratu, safuna kuvomereza kuti sangathe kuchita zinthu zina ndipo nthawi zambiri sasangalala komanso amakhala amantha. Komatu pali anthu ambiri amene amachitabe zinthu bwinobwino ngakhale kuti ndi osaona.

Zinthu zambiri zimene timadziwa, timakhala kuti tinachita kuziona. Ndiye munthu akasiya kuona, amadalira kumva mawu, phokoso komanso fungo. Amadaliranso manja ndi zala zake kuti adziwe zinthu.

Magazini ina inanena kuti asayansi atulukira kuti zinthu zikasintha, “ubongo wathunso umasintha.” (Scientific American) Magaziniyi inanenanso kuti: “Munthu akasiya kuona, ubongo wake umasintha moti amatha kugwiritsa ntchito ziwalo zina kuti achite zomwe maso akanachita.” Kodi zimenezi zimachitika bwanji?

Amamva mawu kapena phokoso: Osaona amatha kuona zinthu m’maganizo mwawo akamva mawu a munthu kapena phokoso linalake. Mwachitsanzo bambo wina wosaona, dzina lake Fernando, anati: “Ndimatha kuzindikira munthu, pongomva mawu ake kapena mtswatswa.” Nawonso a Juan, omwe ndi osaona, anati: “Anthu osaonafe timazindikira munthu tikangomva mawu ake.” Kuwonjezera pamenepa, osaona amadziwa mmene munthu akumvera akamva mmene munthuyo akulankhulira. Mwachitsanzo amatha kuzindikira ngati munthuyo wakwiya, akudandaula kapena ngati akusangalala.

Wosaona amathanso kugwiritsa ntchito zimene wamva kuti adziwe malo amene ali, kumene zinthu zikulowera, kukula kwa chipinda komanso ngati patsogolo pake pali chinthu chomwe chingamugwetse.

Amamva fungo: Wosaona akhoza kudziwa zimene zikuchitika komanso malo amene ali, akangomva fungo linalake. Mwachitsanzo, akamayenda n’kumva kafungo kabwino ka chakudya, amadziwa kuti pamene akudutsapo pakuphikidwa chakudya. Kenako amagwirizanitsa kafungoko ndi zimene akumva n’kudziwa kuti mwina pamalopo pali lesitilanti, moti akamadzadutsanso malo omwewo, amatha kukumbukira mmene angayendere.

Amagwiritsa ntchito manja komanso zala: Bambo wina wosaona, dzina lake Francisco, anati: “Manja angawa ndiye maso anga.” Nthawi zambiri anthu osaona amagwiritsa ntchito manja awo kuti adziwe kumene akupita ndipo akamayenda amagwiritsa ntchito ndodo. A Manasés omwe anabadwa osaona anayamba kugwiritsa ntchito ndodo ali mwana. Iwo anati: “Ndodoyi imandithandiza kudziwa malo amene ndili. Ndimatha kukumbukira kuti njira imene ndikuyendayo ndinaidutsapo pongoyendetsa ndodoyi.”

Munthu akuwerenga Nsanja ya Olonda ya zilembo za anthu osaona

Akuwerenga Nsanja ya Olonda ya zilembo za anthu osaona

Anthu ambiri osaona amagwiritsa ntchito zala zawo powerenga mabuku a zilembo za anthu osaona. Masiku ano pali mabuku ambiri othandiza anthu osaona kuti adziwe zambiri za Baibulo komanso kuti azikhala ndi moyo wabwino. N’zosangalatsanso kuti pali mabuku, magazini komanso timapepala tomwe tinajambulidwa n’cholinga choti anthu osaona azimvetsera. Palinso makompyuta omwe anakonzedwa kuti azithandiza osaona kuwerenga. Zinthu zimenezi zikuthandiza kwambiri osaona kuti azitha kuwerenga Baibulo komanso mabuku ena ofotokoza Baibulo.a

Mabuku amenewa anathandiza kwambiri a Paqui komanso amuna awo, omwe tawatchula kale aja. Iwo amasangalala kwambiri komanso sakhala ndi nkhawa chifukwa amadziwa kuti mavuto amene akukumana nawo ndi osakhalitsa. Anthu a mumpingo wawo wa Mboni za Yehova, amawathandizanso kwambiri. A Paqui anati: “Panopa zinthu zimatiyendera kwabasi ndipo timaona kuti tili ndi moyo wabwino kwambiri kuposa poyamba.”

N’zoona kuti anthu osaona amakumana ndi mavuto ambiri. Koma m’nkhaniyi taona kuti akhoza kumachita zinthu bwinobwino komanso kumakhala mosangalala.

a A Mboni za Yehova amapanga mabuku a zilembo za anthu osaona m’zinenero zoposa 25.

Kukhala Wosaona Sikunandimange Manja

A Marco Antonio ali ndi galu wawo, dzina lake Dante

A Marco Antonio a ku Spain anabadwa osaona chifukwa cha matenda enaake amene amawononga mitsempha yothandiza kuona (optic nerve atrophy). Komabe, amakhala moyo ngati ena onse moti ali ndi mkazi, mwana komanso amachita bizinezi. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza nawo kuti adziwe za moyo wawo.

Ndinamva zoti ndinu munthu wa bizinezi. Ndiye tandifotokozerani, mumachita zotani?

Ndinedi munthu wa bizinezi. Ineyo ndi mnzanga winawake tili ndi kampani yokonza zinthu. Koma sikuti ndimangokhala ayi. Ndimathandiza makasitomala komanso ndimalankhulana ndi anthu amene amatibweretsera katundu. Ndimaikanso ndalama za kampani yathu kubanki.

Mumatani mukakhala kuti simukugwira ntchito?

Ndimakonda nyimbo kwambiri moti ndikamamvetsera nyimbo, kumtimaku kumangoti myaa. Nthawi zina ndimakondanso kuimba piyano, kungoti pena zimandivuta kuti ndiziwerenga manotsi a nyimbo kwinaku ndikuimba piyano. Kuti ndithane ndi vutoli, ndimawerenga manotsi ndi dzanja lamanja n’kumaimba piyano ndi dzanja lamanzere. Kenako ndimaimbanso nyimboyo, koma ulendo wachiwiriwo ndimasintha dzanja. Ndikaizolowera ndimayamba kuimba ndi manja onse.

Ndikukhulupirira kuti nanunso mumakumana ndi mavuto, nanga tinganene kuti mwangodutsa moyera ngati?

Zoona, mavuto saona nkhope. Koma ndimathokoza kuti ndili mwana, makolo anga komanso azichimwene anga ankandikonda komanso kundisamalira bwino kwambiri. Komabe nthawi zambiri ndinkapunthwa komanso kugwa. Kenako patapita nthawi, ndinayamba kuchita zinthu bwinobwino ndipo ndinkatha kuchita zinthu zambiri zimene anthu ena amachita. Ndiyeno nditakula zinkandiwawa kwambiri ndikaganizira kuti sindingathe kuchita zinthu zina monga kuyendetsa galimoto.

Panopa ndili pabanja komanso ndili ndi mwana. Ndimayesetsa kuchita zonse zomwe ndingathe kuti banja langa lizisangalala ndipo mkazi komanso mwana wanga David, amandithandiza kwambiri. Mwanayu anatengera matenda angawa, moti nayenso ndi wosaona. Ndimayesetsa kumuthandiza kuti akhale ndi moyo wabwino. Ndikufuna nditamuthandiza kudziwa kuti akhoza kuchita zambiri ngati atakhala wakhama komanso wodekha.

N’chifukwa chiyani munasankha kuti mukhale ndi galu wokutsogolerani?

Galu wangayu, yemwe dzina lake ndi Dante, amanditeteza komanso amandithandiza kuti ndiziyenda mwachangu. Galuyu anaphunzitsidwa kuti azinditsogolera. Koma ndikamapita kudera lachilendo, mkazi wanga yemwe amaona bwinobwino, amandiperekeza. Amachita zimenezi kuti galuyu aidziwe bwino njirayo. Kunena zoona, poyamba zinkandivuta kukhulupirira kuti galuyu angandithandizedi, koma panopa ndimamudalira kwambiri. Galuyu ndi wodziwa bwino ntchito yake moti akamanditsogolera, satengeka ndi zinthu zina n’kundisiya. Koma ndikangomumasula lamba wam’khosi, amachita zinthu ngati galu wamba.

Popeza ndinu wa Mboni za Yehova, mumatani kuti muzitha kuphunzira Baibulo?

M’mbuyomu kulibe zipangizo zothandiza anthu osaona, mkazi wanga Loli ankandiwerengera Baibulo komanso mabuku ofotokoza Baibulo. Mkazi wangayu anandithandiza kwambiri moti patapita nthawi ndinayamba kukamba nkhani pa misonkhano yathu ya mpingo. Koma masiku ano ndimatha kuwerenga ndekha chifukwa ndili ndi Baibulo komanso mabuku ena a zilembo za anthu osaona. Ndimapitanso pa webusaiti ya Mboni za Yehova ya jw.org n’kupanga dawunilodi mabuku omvetsera. Ndilinso ndi chipangizo china chomwe chimandithandiza kuwerenga mawu amene ali pasikilini ya kompyuta yanga. Chipangizochi chimasintha mawu omwe ali pasikilini kuti akhale m’zilembo za anthu osaona.

Nthawi zina anthu a ku maofesi a Mboni za Yehova mumzinda wa Madrid, amandiitana kuti ndikawerenge mabuku a zilembo za anthu osaona. Anthu amene amagwira ntchito yopanga mabukuwa amafuna kumva maganizo a anthu osaona n’cholinga choti mabukuwa akhale abwino kwambiri. Choncho amandiitana kuti ndikaone ngati mabukuwo akumveka bwino. Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kuthandiza nawo ntchitoyi.

Kodi mumakonda kucheza ndi ndani?

Ndimakonda kucheza ndi banja komanso achibale anga. Ndimakondanso kucheza ndi a Mboni anzanga ndipo nthawi zambiri ndimayenda nawo limodzi tikamapita kukalalikira kunyumba ndi nyumba. A Mboni anzangawa amachita zinthu mondiganizira kwambiri. Ndikamacheza nawo zimangokhala ngati aiwala kuti ndine wosaona.

Ntchito yolalikirayi imandipatsa mwayi wouza ena zimene Baibulo limalonjeza. Mwachitsanzo, lemba la Yesaya 35:5 limanena kuti Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira, “maso a anthu akhungu adzatsegulidwa.” Yesu Khristu ali padziko lapansi, anachiritsa anthu osaona. Anachita zimenezi pofuna kuthandiza anthu kudziwa kuti adzachitanso zomwezo mtsogolomu. (Mateyu 15:30, 31) Choncho, vuto la kusaona komanso mavuto ena onse sadzakhalapo mpaka kalekale ndipo palibe amene azidzanena kuti “Ndikudwala.”—Yesaya 33:24; Luka 23:43.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena