Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 8/15 tsamba 3-4
  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani kwa Akhungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Pali Chiyembekezo Chotani kwa Akhungu?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchiritsa Akhungu m’Tsiku la Yesu
  • Kutsegula Maso Kuti Aone Mbiri Yabwino
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Muzithandiza Anthu Osaona Kudziwa za Yehova
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2015
  • Khungu la mu Mtsinje Kugonjetsa Mliri Wowopsawo
    Galamukani!—1995
  • Yesu Anachiritsa Munthu Amene Anabadwa Wosaona
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 8/15 tsamba 3-4

Kodi Pali Chiyembekezo Chotani kwa Akhungu?

JOHN MILTON analemba mabuku ake andakatulo otchedwa Paradise Lost ndi Paradise Regained ngakhale kuti anali wakhungu kotheratu. Kukhala wakhungu ndi wogontha sikunachititse Helen Keller kuleka ntchito yake yothandiza opunduka mwakuthupi. Inde, anthu ambiri akhungu amalimbana bwino lomwe ndi vutolo. Koma kukanakhala kokondweretsa chotani nanga ngati aliyense akanakhala ndi maso oona bwino! Makamaka inu mungavomereze zimenezi ngati muli ndi wokondedwa wina kapena bwenzi amene ali wakhungu kapena wosapenya bwino.

Zoonadi, m’maiko ena maprogramu ophunzitsa opunduka amaphunzitsa anthu osapenya bwino maluso a moyo watsiku ndi tsiku. Mabuku a akhungu ndi agalu ophunzitsidwa amathandiza akhungu kusamalira zambiri za zosoŵa zawo. Chikhalirechobe, anthu ambiri amalingalira khungu kukhala kupunduka kowopsa koposa. Mlembi wina anati: “Kukhala wakhungu ndiko kusoŵa ufulu wopezera mbali yofunika koposa ya moyo wathu wa kuona zinthu.” Panthaŵi imodzimodziyo, ambiri afunikira kudalira pa ena mowonjezereka.

Kodi nchifukwa ninji, inu mungadabwe motero, khungu lili lofala chotere? Chabwino, kodi munamvapo za trachoma? Ndiyo imene imachititsa odwala khungu pafupifupi mamiliyoni asanu ndi anayi. The New Encyclopædia Britannica ponena za iyo ikuti: “Nthendayo njopatsirana ndipo imafalikira pamene anthu ambirimbiri akhala mopanikizana pamodzi m’malo opanda ukhondo. Kupereŵera kwa madzi osamba, ndi ntchentche zambirimbiri zoitanidwa ndi chimbudzi cha anthu, zimathandizira kuwanditsa nthendayo. Mwanjira ina trachoma ili vuto la chitaganya koposa kukhala vuto la zamankhwala; ngati miyezo yokhalira moyo ingawongoleredwe, kukhala mopanikizana kukumachepetsedwa, ntchentche zikumaletsedwa, ndipo madzi abwino okwanira nakhalapo, kufalikira kwa trachoma kumachepa mofulumira.” Anthu pafupifupi miliyoni imodzi amavutika ndi onchocerciasis. Kapena bwanji za xerophthalmia? Ngakhale kuti dzinalo nlovuta, choonadi nchakuti ndiyo nthenda yofala yochititsa khungu. Nthenda ya shuga, diphtheria, chikuku, scarlet fever, ndi nthenda zopatsirana mwa kugonana zingachititsenso khungu.

Pamene tikukula, maso athu angayambe kufooka chifukwa cha zovuta zonga kufooka kwa macula lutea ndi glaucoma, ndiponso sitinganyalanyaze ng’ala. The New Encyclopædia Britannica ikunena kuti: “Ng’ala idakali pamwamba pa mndandanda wa zochititsa khungu m’maiko ambiri m’dziko, ndipo zimenezi nzomvetsa chisoni popeza kuti ikhoza kuchiritsidwa mosavuta konse ndi opaleshoni.”

Mosasamala kanthu za kutulukira kwatsopano m’kuchiritsa nthenda za maso, kuthetsedwa kwa khungu kukuonekera kukhala kuli patali. Insaikulopediya imodzimodziyo ikuti: “Kupita patsogolo m’kuletsa ndi kuchiritsa khungu ndi mankhwala ndi opaleshoni kwangokhala kopindulitsa kwa anthu amene ali okhoza kupeza chisamaliro cha mankhwalacho. Kufikira miyezo ya chakudya ndi ukhondo ya chigawo chachikulu cha anthu a padziko itawongoleredwa, khungu lokhoza kuletsedwa lidzakhalabe lili pamlingo wake waukulu umene ulipowu.”

Pamene kuli kwakuti mankhwala opha tizilombo ndi opaleshoni zilidi zofunika m’kulimbana ndi khungu, chiyembekezo cha kuchiritsa kwachikhalire nchogwirizana ndi kanthu kena kamene kanachitika pafupifupi zaka zikwi ziŵiri zapitazo.

Kuchiritsa Akhungu m’Tsiku la Yesu

Tayerekezerani munthu wina wa m’zaka zake za m’ma 30 akumayenda mumsewu wa fumbi. Pomva kuti iye akudutsa, amuna aŵiri akhungu kumphepete kwa msewuwo akufuula kuti: “Mutichitire ife chifundo.” Ngakhale kuti openyerera akuwalamula kutonthola, akhunguwo akufuulitsa kuti: “Mutichitire chifundo.” Munthuyo akuwafunsa mokoma mtima kuti: “Mufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” Iwo akuyankha mwamsanga kuti: “Kuti maso athu apenye.” Tsopano tangoganizani: Munthuyo akukhudza maso awo, ndipo pomwepo iwo akupenya!​—Mateyu 20:29-34.

Zinali zosangalatsa chotani nanga kwa omwe kale anali akhungu ameneŵa! Komabe, khungu lili lofala. Chimenechi chinali chochitika chimodzi chabe. Kodi nchifukwa ninji chingafune chisamaliro chanu? Chifukwa chakuti anali Yesu wa ku Nazarete amene mokoma mtima anachititsa akhungu amenewo kuti aone. Kwenikweni, kuwonjezera pa kukhala ‘wodzozedwa kuuza anthu osauka uthenga wabwino,’ Yesu ‘anatumidwa kuti akhungu apenyenso.’​—Luka 4:18.

Anthu anadabwa ndi kuchiritsa kozizwitsa kotero kochitidwa kupyolera mwa mzimu woyera wamphamvu wa Mulungu. Timaŵerenga kuti: “Khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziŵalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israyeli.” (Mateyu 15:31) Popanda kulipiritsa kapena kudzionetsera kapena kudzifunira ulemerero wa iye mwini m’kuchiritsa kotero, Yesu anasonyeza chikondi ndi chifundo cha Yehova Mulungu. Komabe, Yesu anachitiranso chisoni anthu akhungu mwauzimu ndi opanda thandizo amene anali “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.”​—Mateyu 9:36.

Ngakhale kuti mbiriyo njokondweretsa, inu mungadabwe kuti, Bwanji nanga lerolino? Popeza kuti lerolino palibe munthu amene amachiritsa monga momwe Yesu anachitira, kodi kuchiritsa kumeneko kuli ndi tanthauzo kwa ife? Kodi pali chiyembekezo chilichonse kwa akhungu? Chonde ŵerengani nkhani yotsatira.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

“Kufikira miyezo ya chakudya ndi ukhondo ya chigawo chachikulu cha anthu a padziko itawongo- leredwa, khungu lokhoza kuletsedwa lidzakhalabe lili pamlingo wake waukulu umene ulipowu.”​—The New Encyclopædia Britannica

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena