Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 11/8 tsamba 10-11
  • Mmene Mungakhalire ndi Moyo Kosatha

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungakhalire ndi Moyo Kosatha
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chifuno cha Mulungu
  • Mmene Mungakhalire ndi Moyo Kosatha
  • Kodi Moyo Wosatha Ndi Wothekadi?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kukhala ndi Moyo Kosatha Siloto Chabe
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Chifuno cha Mulungu cha Dziko Lapansi N’chiyani?
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Kodi Tingakhale kwa Utali Wotani?
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 11/8 tsamba 10-11

Mmene Mungakhalire ndi Moyo Kosatha

POPEZA kuti thupi la munthu mwachionekere lili ndi mphamvu ya moyo wotalikirapo kuposa umene anthu amakhala nawo lerolino, ena amakhulupirira kuti sayansi idzapeza njira imene tingakhalire ndi moyo kosatha. “Pamene tipeza chidziŵitso chokwana cha makhemikolo a thupi ndi mmene amachirikizirana,” analemba motero Dr. Alvin Silverstein, “tidzamvetsa mkhalidwe wa moyo. Tidzazindikira . . . mmene munthu amakalambira.”

Padzakhala zotulukapo zotani? Zidzatifikitsa ku “nyengo yatsopano m’mbiri ya munthu,” anatero Silverstein. “Sipadzakhalanso anthu ‘okalamba,’ pakuti chidziŵitso chimene chidzachititsa imfa kugonjetsedwa chidzadzetsanso unyamata wamuyaya.”

Kodi anthu adzachita zimenezi? “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye,” Baibulo limalangiza motero. “Mpweya wake uchoka, abwerera kumka ku nthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.” (Salmo 146:3, 4) Anthu alephera kupeza, ngakhale kuwongolera, tchimo lacholoŵa limene limachititsa ukalamba ndi imfa, monga momwedi taonera. Mlengi wathu yekha ndiye angachite zimenezo.

Koma kodi chilidi chifuno cha Mulungu kuti anthu akhale ndi moyo kosatha pa dziko lapansi?

Chifuno cha Mulungu

Kodi Yehova Mulungu anawaika kuti anthu aŵiri oyamba kuti akhale ndi moyo? M’paradaiso wa pa dziko lapansi. Ndipo iwo analangizidwa kuti ‘abalane, achuluke, nalidzaze dziko lapansi, kuligonjetsa.’ (Genesis 1:28) Inde, chifuno cha Mulungu chinali chakuti, m’kupita kwa nthaŵi, banja la anthu olungama likakhale pamodzi pa dziko lonse lapansi mumtendere ndi chimwemwe.—Yesaya 45:18.

Ngakhale kuti chiweruzo cha imfa chinaperekedwa pa Adamu chifukwa cha kusamvera kwake, chifuno choyambirira cha Mulungu chakuti anthu akhale ndi moyo kosatha m’Paradaiso pa dziko lapansi sichinasinthe ayi. (Genesis 3:17-19) “Inde, ndanena,” Mulungu akutero, “ndidzachionetsa.” (Yesaya 46:11; 55:11) Mulungu anasonyeza kuti chifuno chake ponena za dziko lapansi sichinasinthe pamene anati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.

Pokhala Mlengi wathu, Mulungu ali ndi mphamvu ya kuwongolera chilema chimene chimachititsa anthu kukalamba ndi kufa. Adzachita zimenezi pamaziko otani? Popeza kuti chilema chimenecho ndi choloŵa cha kwa Adamu, munthu woyamba, Mulungu wapereka nsembe ya dipo ya moyo wangwiro wa Mwana wake, Yesu Kristu, “kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16; Mateyu 20:28.

Kwenikweni, Yesu Kristu akutenga malo a Adamu woyambirira monga atate wathu, kapena wotipatsa moyo. Nchifukwa chake m’Baibulo Yesu akutchedwa “Adamu wotsiriza.” (1 Akorinto 15:45) Chotero m’malo moweruzidwa kuti afe monga ana a Adamu wochimwa, anthu omvera amaonedwa kukhala oyenera kulandira moyo wosatha monga ana a “Atate [wawo] Wosatha,” Yesu Kristu.—Yesaya 9:6.

Ndithudi, “Mfumu yosatha” ndi “Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu” ali Yehova Mulungu. (1 Timoteo 1:17; Chivumbulutso 15:3; Akolose 1:3) Komabe, Yesu Kristu, kuwonjezera pa kukhala kwake “Atate [wathu] Wosatha” ndi “Mpulumutsi,” alinso “Kalonga wa Mtendere.” (Luka 2:11) Pokhala woimira Atate wake, Kristu adzagwiritsira ntchito ulamuliro waukalonga kudzetsera mtendere pa dziko lapansi.—Salmo 72:1-8; 110:1, 2; Ahebri 1:3, 4.

Pansi pa ulamuliro wa Yesu Kristu, Paradaiso wa pa dziko lapansi amene anatayika adzapezeka. Yesu anati zimenezi zidzachitika “[m’kulenganso, NW], pamene Mwana wa munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake.” (Mateyu 19:28) Otsatira a Kristu okhulupirika—onse pamodzi 144,000—adzalamulira dziko lapansi la Paradaiso limodzi naye. (2 Timoteo 2:11, 12; Chivumbulutso 5:10; 14:1, 3) Anthu mamiliyoni ambiri adzapindula ndi ulamuliro wolungama umenewo mwa kukhala ndi moyo pa dziko lapansi m’Paradaiso. Pakati pawo padzakhala mpandu uja amene anafera pambali pa Yesu amenenso Yesu analonjeza kuti: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.”—Luka 23:43.

Chotero, ngakhale akufa osalungama adzaukitsidwa ndipo adzapatsidwa mwaŵi wakuti ayenerere moyo wosatha pa dziko lapansi. (Machitidwe 24:15) Baibulo limafotokoza bwino kwambiri za kuchotsedwa kwa nthenda, ukalamba, ndi imfa, likumati: “Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Mmene Mungakhalire ndi Moyo Kosatha

Mosakayika mukufuna kudzapezeka pakati pa awo amene adzalandira dziko lapansi ndi kukhalamo kosatha. Ngati zili choncho, muyenera kufitsa zofunika za moyo wosatha m’Paradaiso. Popemphera kwa Atate wake wakumwamba, Yesu Kristu anatchula chofunika chachikulu, akumati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—Yohane 17:3.

Mboni za Yehova zili zokonzeka kukuthandizani kupeza chidziŵitso chopatsa moyo chimenechi. Ingowapemphani ndipo, kwaulere, adzakuchezerani panthaŵi yoyenera ndi kukambitsirana nanu za chifuno cha Mulungu cha kupatsa anthu ungwiro wauzimu ndi wakuthupi. Khalani ndi chidaliro chakuti Mlengi wathu wamphamvuyonse akhozadi kuwongolera tchimo la choloŵa limene limachititsa ukalamba ndi imfa. Ikudza nthaŵi, ndipo yayandikira, pamene moyo sudzakhalanso waufupi. Yehova adzadalitsa anthu ake ndi “moyo womka muyaya.”—Salmo 133:3.

[Chithunzi patsamba 10]

Pansi pa ulamuliro waukalonga wa Kristu, ukalamba ndi imfa zidzagonjetsedwa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena