Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 11/8 tsamba 26-28
  • Mmene Tingaonere Kukongola Kotizinga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Tingaonere Kukongola Kotizinga
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kudziŵa Zinthu Zimene Zimachititsa Kukongola
  • Kuona Zazing’ono ndi Zazikulu
  • Amuna Amene Anaphunzira Kuyang’anitsitsa
  • Waluso wonyalanyazidwa koposa m’Nthaŵi Yathu
    Galamukani!—1995
  • Kodi Kaonekedwe ka Zinthu Kamakukhudzani Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Kodi Luso Nchiyani?
    Galamukani!—1995
  • Kukongola Kungakhale Kokha kwa pa Khungu
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 11/8 tsamba 26-28

Mmene Tingaonere Kukongola Kotizinga

“M’zinenero zonse, amodzi a mawu oyambirira ndiwo akuti ‘taimani kaye ndione!’”—William White, Jr.

KAMWANA kamene kakuyang’anitsitsa gulugufe amene akupeyukapeyuka, mwamuna ndi mkazi wake okalamba amene akuyang’anitsitsa kuloŵa kwa dzuŵa kwaulemerero, mkazi wa panyumba akuchita chidwi ndi ma rose ake olinganizidwa—onsewo atembenukira kwakanthaŵi pa kukongola.

Popeza kuti kukongola kwa chilengedwe cha Mulungu kuli ponseponse, sikuli kofunika kuti tiyende ulendo wautali kuti tikakuone. Malo ochititsa chidwi angakhale kutali nafe, koma kanthu kena kopangidwa mwaluso lokondweretsa kangapezeke pamene mumakhala ngati mukafunafuna ndipo—makamaka—ngati mudziŵa mmene mungakapezere.

Kaŵirikaŵiri kwanenedwa kuti “kukongola kuli m’maso mwa munthu.” Komabe, ngakhale ngati kukongolako kulipo, si onse amene angakuone. Mwinamwake pangafunikire chithunzithunzi kuti tikhale pansi ndi kuyang’anitsitsa kukongola kwake. Kwenikweni, ojambula ambiri amakhulupirira kuti ukatswiri wawo umadalira kwambiri pa luso lawo la kuyang’anitsitsa kuposa pa kujambula ndi manja. Buku lakuti The Painter’s Eye, lolembedwa ndi Maurice Grosser, likulongosola kuti “wojambula ndi manja amajambula ndi maso ake, osati ndi manja ake. Chilichonse chimene amaona, ngati achiona bwino, angathe kuchijambula. . . . Kuona bwino ndiko chinthu chofunika.”

Kaya ndife ojambula kapena ayi, tingaphunzire kuona bwino kwambiri, kuona kukongola kotizinga. M’mawu ena, tifunikira kupita ndi kukayang’anitsitsa zinthu ndi lingaliro lina latsopano.

Ponena za nkhaniyi John Barrett, mlembi wa mbiri ya zinthu zachibadwa, akugogomezera za kufunika kwa munthu kudziloŵetsa m’nkhaniyi. “Palibe chimene chimaloŵa m’malo mwa kudzionera, kukhudza, kununkhiza ndi kumva nokha nyama zamoyo ndi zomera ndi mphamvu zonse za chilengedwe zimene zimagwira ntchito pa zinthuzo,” iye akutero. “Lolani kukongolako kukhomerezeka m’maganizo . . . Kuli konse kumene mungakhale, choyamba yang’anitsitsani, sangalalani ndi kuyang’anitsitsanso.”

Koma kodi tiyenera kuyang’anitsitsa chiyani? Tiyenera kuyamba kuphunzira kudziŵa zinthu zazikulu zinayi za kukongola. Zinthu zimenezi zingadziŵidwe pafupifupi m’mbali iliyonse ya chilengedwe cha Yehova. Pamene kaŵirikaŵiri tiima ndi kuyang’anitsitsa, mpamenenso timasangalala kwambiri ndi luso lake.

Kudziŵa Zinthu Zimene Zimachititsa Kukongola

Maumbidwe ndi Mitundu. Tikukhala m’dziko la zinthu za maumbidwe osiyanasiyana. Zina nzowongoka ngati maphata a nsungwi kapena zopingasana mozungulira ngati nyumba ya kangaude, pamene kuli kwakuti zina nzopanda maumbidwe enieni monga ngati mtambo umene umasintha nthaŵi zonse. Maumbidwe a zinthu ambiri ngokongola, kaya akhale a zomera za kumaiko ena, mopoteka mwa nkhono za kunyanja, kapena ngakhale nthambi za mtengo umene masamba ake ayoyoka.

Pamene maumbidwe amodzimodziwo abwezeredwanso, amapanga mtundu umene umakhalanso wokongola m’maso. Mwachitsanzo, tayerekezerani za mitengo yothithikana mu nkhalango. Maumbidwe ake—alionse osiyana ndi ena, komabe ofanana—amapanga mtundu wokondweretsa. Koma kuti munthu aone bwino maumbidwe ndi mtundu umene zimapereka, payenera kukhala kuunika.

Kuunika. Kukhalapo kwa kuunika kumapereka mkhalidwe wina wapadera pa maumbidwe amene timaona kukhala okongola. Dongosolo lake limaoneka, maonekedwe ake amakhalapo, ndipo malingaliro a chinthucho amapangika. Kuunika kumasiyanasiyana malingana ndi nthaŵi ya tsiku, nyengo ya chaka, kachedwe kakunja, ndipo ngakhale chifukwa cha malo amene timakhala. Tsiku la mitambo la kuunika kochepa nlabwino pofuna kudziŵa za maonekedwe obisika a maluŵa a kuthengo kapena za maonekedwe a masamba a nyengo ya mphakasa, pamene kuli kwakuti mong’ambika ndi nsonga za mtandaza wa mapiri zimaonetsa maumbidwe awo ochititsa chidwi pamene kutuluka kapena kuloŵa kwa dzuŵa kuziunikira. Kuŵala kwa dzuŵa kofunda kwa kamphepo kwa ku Northern Hemisphere kumachirikiza malingaliro a malo okongola odyerako ziŵeto. Komanso, dzuŵa loŵala la malo a Tropic limachititsa nyanja yosaya kukhala malo ochititsa chidwi a osambira m’madzi ndi ma snorkel.

Komabe pakali chinthu chinanso chofunika.

Maonekedwe. Amachititsa zinthu zosiyanasiyana zimene timaona motizinga kukhala zenizeni. Pamene kuli kwakuti maumbidwe ake angazisiyanitse, maonekedwe ake amasonyeza mkhalidwe wake wapadera. Ndiponso, kuoneka kwa maonekedwewo mogwirizana ndi mtundu wake zimapanga mkhalidwe wakewake wokongola. Angakhale maonekedwe oŵala kwambiri monga ngati ofiira kapena ofiirira amene amafunikira chisamaliro chathu kuti tiwazindikire, kapena maonekedwe otsitsimula mtima onga bluu kapena obiriŵira.

Tangoyerekezerani kagulu ka maluŵa achikasu kokhala pakati pa mitengo. Kuunika kumaŵalira maluŵa achikasuwo, amene amaŵala m’mphepo ya mmaŵa, pamene kuli kwakuti mitengo yakuda yokongola chifukwa cha dzuŵa la mmaŵa imapanga maonekedwe osiyana abwino kwambiri. Tsopano takhala ndi chithunzithunzi. Chimene tingofunikira kuchita ndicho ‘kuchiika m’feremu,’ apa mpamene kulinganiza kumafunika.

Kulinganiza. Njira imene zinthu zitatu zazikuluzo—maumbidwe, kuunika, ndi maonekedwe—zimagwirizanira ndiyo imene imatsimikiziritsa kulinganiza kwake. Ndipo pamenepa, ife monga openyerera, tili ndi mbali yofunika koposa yoti tichite. Mwa kungosunthira pang’ono cha kutsogolo, kumbuyo, cha m’mbali, cha mu mtunda, kapena cha mmunsi, tingasinthe kaonekedwe ka zinthu kapena kuunika pa chithunzithunzi chathucho. Motero tingathe kutulutsa chithunzithunzi cha zinthu zimene tikufuna zokha.

Kaŵirikaŵiri, timatha kulinganiza chithunzithunzi pamene tifika pa malo ena okongola amene azingidwa ndi mitengo ya pafupi kapena zomera. Koma zithunzithunzi zambiri zabwino kwambiri, zazing’onopo, zingakhale zili pamene taponda.

Kuona Zazing’ono ndi Zazikulu

M’ntchito ya manja a Mulungu, zinthu zazikulu ndi zazing’ono zomwe nzokongola, ndipo chisangalalo chathu chidzawonjezereka ngati tiphunzira kuona dongosolo lake, limenenso lili logwirizana mokondweretsa. Zimaumba zithunzithunzi zazing’ono zimene zili zopezeka ponseponse m’chithunzithunzi chachikulu cha chilengedwe. Kuti tizizindikire, timangofunikira kuŵerama ndi kuyang’anitsitsa.

Zithunzithunzi za mkati mwa chithunzithunzi zimenezi zafotokozedwa ndi wojambula ndi kamera wina John Shaw m’buku lake lakuti Closeups in Nature kuti: “Ndimadabwa nthaŵi zonse kuti pamene ndiyang’anitsitsa dongosolo la chilengedwe ndimafuna kuonetsetsa kwambirinso nthaŵi zonse. . . . Choyamba timaona chithunzithunzi chachikulu, ndiyeno banga lina la maonekedwe ena penapake m’chithunzithunzimo. Pamene tiyang’anitsitsa timaona maluŵa ndipo, paduŵa lina, gulugufe. Mapiko ake amasonyeza mtundu wina wapadera, mtunduwo ngopangidwa mwadongosolo lenileni la mamba a pamapiko, ndipo alionse a mambawo ngokonzedwa bwino kwambiri pa iwo okha. Ngati tizindikiradi kukonzedwa bwino kumene kuli pa mamba a pa phiko la gulugufe, tingayambe kumvetsa mokhulupirira kukonzedwa bwino kwa mmene chilengedwe chilili.”

Kuwonjezera pa chikondwerero chimene kukongola kumatipatsa, luso la chilengedwe—chachikulu ndi chaching’ono chomwe—lingatikokere pafupi ndi Mlengi wathu. “Kwezani maso anu kumwamba, muone,” analimbikitsa motero Yehova. Mwa kuima kaye ndi kuona, kuyang’anitsitsa, ndi kusinkhasinkha, kaya tiyang’anitsitse thambo la nyenyezi kapena chilengedwe china chilichonse cha Mulungu, timakumbutsidwa za Uyo “amene analenga izo.”—Yesaya 40:26.

Amuna Amene Anaphunzira Kuyang’anitsitsa

M’nthaŵi za Baibulo atumiki a Mulungu anali ndi chidwi chapadera pa chilengedwe. Malinga ndi kunena kwa 1 Mafumu 4:30, 33, “nzeru ya Solomo inaposa nzeru za anthu onse a Kummaŵa,  . . . nakamba za mitengo, kuyambira mkungudza uli ku Lebano kufikira hisopi wophuka pakhoma; anakambanso za nyama ndi mbalame ndi zinthu zokwaŵa pansi ndi za nsomba.”

Mwinamwake chidwi cha Solomo pa ulemerero wa chilengedwe mwapang’ono chinali chifukwa cha chitsanzo cha atate wake. Davide, amene anathera zaka zake zambiri zaunyamata monga mbusa, kaŵirikaŵiri anasinkhasinkha pa ntchito ya manja a Mulungu. Makamaka kukongola kwa thambo kunamchititsa chidwi. Pa Salmo 19:1, analemba kuti: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.” (Yerekezerani ndi Salmo 139:14) Mwachionekere, kuona kwake chilengedwe kunamkokera pafupi ndi Mulungu wake. Kungachitenso chimodzimodzi kwa ife.a

Monga momwe anthu owopa Mulungu ameneŵa anadziŵira, kuzindikira ndi kuyamikira ntchito ya manja a Mulungu kumatitsitsimula ndi kukhutiritsa moyo wathu. M’dziko lathu lamakonoli lodzazidwa ndi zosangulutsa zokonzedweratu zimene kaŵirikaŵiri zili zoluluza makhalidwe, kuyang’anitsitsa chilengedwe cha Yehova kungakhale chochita chabwino kwa ife ndi mabanja athu. Kwa awo amene akulakalaka dziko latsopano la Mulungu lolonjezedwa, zimenezo ndizo chinthu chotherapo nthaŵi chimene adzasangalala nachonso mtsogolo.—Yesaya 35:1, 2.

Pamene tiona zinthu zopangidwa mwaluso zotizinga ndi kuzindikiranso makhalidwe a Waluso Wamkuluyo amene anazipanga, mosakayikira tidzasonkhezereka kuvomereza mawu a Davide akuti: “Palibe wina wonga inu, [Yehova, NW]; ndipo palibe ntchito zonga zanu.”—Salmo 86:8.

[Mawu a M’munsi]

a Olemba Baibulo ena, onga ngati Aguri ndi Yeremiya, analinso anthu achidwi kwambiri ndi mbiri ya chilengedwe.—Miyambo 30:24-28; Yeremiya 8:7.

[Zithunzi patsamba 26]

Zitsanzo za mtundu ndi maumbidwe, kuunika, maonekedwe, ndi kulinganiza

[Mawu a Chithunzi]

Godo-Foto

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena