Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g95 12/8 tsamba 27-28
  • Njira ya Mwana Yoyendera—ya mu Afirika ndi ya ku North America

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira ya Mwana Yoyendera—ya mu Afirika ndi ya ku North America
  • Galamukani!—1995
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njira ya ku North America
  • Njira ya mu Afirika
  • Zimene Makanda Amafunikira Ndiponso Zimene Amafuna
    Galamukani!—2004
  • Zimene Mungachite Mwana Akabadwa
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Malangizo Ofunika a Kuyamwitsa Bere
    Galamukani!—1994
  • Kupatsa Ana Zimene Amafunikira
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Galamukani!—1995
g95 12/8 tsamba 27-28

Njira ya Mwana Yoyendera—ya mu Afirika ndi ya ku North America

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU NIGERIA

PALI njira zosiyanasiyana zimene anthu padziko lonse amanyamulira ana paulendo. Njira ya ku North America njosiyana kwambiri ndi ya ku Afirika.

Pa makontinenti osiyana ameneŵa, mikhalidwe ya chuma imasiyana kwambiri. Chotero tiyenera kuyembekezera kuti njira zonyamulira ana paulendo zingasiyane kwambirinso. Choyamba, tiyeni tione mmene kaŵirikaŵiri anthu a ku North America amachitira pankhaniyi.

Njira ya ku North America

Ku United States ndi mbali zina zambiri za dziko, chikuku cha mwana cha magudumu anayi, chili njira yozoloŵereka. Ndipo m’zaka zaposachedwapa pakhala maluso a kuzipanga kukhala zosavuta kugwiritsira ntchito, zokometseredwa kwambiri, ndi zabwino kwambiri kwa mwana. Zambiri nzamkati mwawofuwofu, zokhalira zokhoza kuchapidwa, ndi mipando yotukulidwira pamwamba.

Zikukuzo zimakhala mopumuliramo ana, ndizo kusintha m’kayendedwe, kupumitsa mapazi opweteka. Kwa mwana amene ali m’tulo, chikuku chimakhala mbedi wa pamagudumu. Kaŵirikaŵiri kuyenda kwa chikukuko kumatonthoza mwana wotopa ndi woliralira.

Zikuku zimapangitsa moyo kukhala wofeŵeraponso kwa makolo. Kholo lina linati: “Zimakhala zofeŵerapo kuposa kunyamula mwanayo kulikonse.” Mwana amakhala wosavuta kumnyamula pamene ali wamng’ono, komano zinthu zimasintha pamene iye ayamba kulemera mowirikiza kaŵiri kapena katatu. Ndiponso, makolo amakonda kudziŵa kuti mwana wawo ali wotetezereka m’chikuku chimene akhoza kuchiyendetsa.

Ku United States, zikuku zimapangidwa mosamala kuti zikhale zotetezereka. Zimapangidwa zazikulu bwino ndi zolemera bwino kotero kuti zisagudubuke wamba. Mabuleki ake amakhala amphamvu ndi oikidwa pamalo pamene sangamasulidwe ndi mwana wa m’chikukumo. Akapichi ake amaikidwa mwa njira yotetezera chikukucho kuti chisapindike mwangozi. “Malo otsina” amatetezeredwa—malo amene angapane tizala tamwana. Malamba a pampando amatetezeranso ana.

Zikuku zimasiyana mitengo kuyambira pa $20 kufikira ku mtengo woŵirikiza kasanu ndi katatu kapena khumi. Mtundu wina wapamwamba umene umafikira pafupifupi $300 uli ndi malo aakulu oikamo zinthu, mkati mwawofuwofu, kunja kosayambukiridwa ndi kusintha kwa nyengo, magudumu okhoza kutembenukira kulikonse, ndi feremu yopepuka yosavuta kupinda. “Chikuku cha othamanga” cholinganizidwa mwapadera chokhoza kuyendetsedwa ndi amayi kapena atate pamene akuthamanga, chimagulitsidwa pafupifupi $380.

Njira ya mu Afirika

Mu Afirika, ndi kumaiko ambiri a ku Asia, anakubala ochuluka amabereka ana awo kumsana, monga momwe amawo ndi agogo awo aakazi anachitira kale. “Kubereka mwana kumsana,” monga momwe anthu ambiri a mu Afirika amakutchera, nkosakwera mtengo ndiponso ndiko njira yabwino kwambiri. Chinthu chokha chimene chimafunika ndicho nsalu yolimba yotchedwa mberekero. Mu mchitidwe wosavuta ndi wotetezereka, nakubala amaŵerama, ndi kuika mwana wake kumsana, ndiyeno amaika nsaluyo kumbuyo ndi kuimanga.

Kodi anawo amagwa pamene akuwabereka kumsana? Zimenezi sizimachitika kaŵirikaŵiri. Pobereka khanda kumsana ndi nsalu, nakubala amagwirizira mwanayo ndi dzanja limodzi pamene akukokera nsaluyo kutsogolo ndi dzanja lina. Ponena za makanda okulirapo, mkazi wina wa ku Nigeria wotchedwa Blessing anati: “Ana samakana; amagwiririra mwamphamvu. Amakonda kuberekedwa kumsana kwa amawo. Nthaŵi zina amalilira kuberekedwa kumsanako. Koma ngati mwana akana kumsana, nakubala amatha kupana ndi m’makwapa dzanja kapena manja onse a mwanayo kufikira atamanga nsaluyo.”

Kuti ana aang’ono kwambiri asamve khosi kupweteka, anakubala amaikanso nsalu ina, imene amamanga mofanana ndi yoyamba. Kuchirikiza ana amene ali m’tulo kwina kumachitidwa mwa kufunditsa manja a mwanayo ndi mberekero. Ana okulirapo amakonda kuti manja awo akhale omasuka.

Kodi anakubala a mu Afirika amabereka ana awo kumsana kwautali wotani? Kale mitundu ina, monga ngati Ayoruba a ku Nigeria, anali kubereka kumsana ana awo kwa zaka zofikira zitatu. Masiku ano mwana amaberekedwa kumsana kwa zaka pafupifupi ziŵiri, ngati panthaŵiyo nakubala sanabale mwana wina wotenga malo a mnzakeyo.

Mwanayo ataberekedwa bwino kumsana kwa amake, amamka kulikonse kumene amake amuka—m’malo okwera ndi otsika, m’malo ovuta, kuloŵa ndi kutuluka m’galimoto. Koma kuwonjezera pa kukhala njira yoyendera yabwino ndi yosakwera mtengo, kubereka mwana kumsana kumakwaniritsa zikhumbo za mtima zofunika, monga ngati chitonthozo. Mwana amene akulira amaberekedwa kumsana kwa amake; mwanayo amagona, ndipo amake amapitiriza kuchita ntchito yawo.

Kugoneka mwana amene ali m’tulo kuchokera kumsana kumafuna kufatsirira, popeza kuti ana ambiri samafuna kudodometsedwa. Kuti achite zimenezi, nakubala amagona cha m’mbali mosamala ndi kumasula bwinobwino mberekero, imene tsopano imakhala yomfunditsira. Nthaŵi zina, kuti achite ngati akali kumsanabe, nakubalayo amaika mtsamiro kutsogolo kwa mwanayo.

Kubereka mwana kumsana kuli ndi mapindu ena. Kumakhozetsa nakubala kudziŵa zofunikira za mwana wake. Ngati mwanayo ali wofooka, akufulukutafulukuta, akutentha thupi, kapena wanyoŵetsa matewera, nakubalayo amadziŵa. Kubereka mwana kumsana kumapindulitsanso kwa nthaŵi yaitali. Buku lakuti Growth and Development limati: “Kuyandikirana kwambiri kwa mwana ndi amake kumaumba chikondi ndi chisungiko pakati pawo, kukumapanga unansi waukulu wa m’zaka zamtsogolo. Kukukhulupiriridwa kuti chochititsa chachikulu cha chikondi chimenechi ndicho mfundo yakuti mwana woyandikana kwambiri ndi amake angathe kudziŵa mosavuta kugunda kwa mtima wawo, monga momwedi anadziŵira pamene anali m’mimba mwa amake.”

Ana amakonda kuyandikana ndi amawo kumene kumakhalapo pamene aberekedwa kumsana. Mu Afirika mukhoza kuona ana ambiri osangalala ataberekedwa kumsana kwa amawo. Ena amaodzera ndi kugona bwinobwino. Ena amaseŵeretsa tsitsi la amawo, makutu awo, kapena mkanda wa m’khosi. Ndiponso ena amagwirizana ndi amawo m’nyimbo yokongola imene amaimba mogwirizana ndi mmene akuyendera.

Inde, njira yoyendera ya mwana ya mu Afirika kaŵirikaŵiri njosiyana kwambiri ndi njira ya ku North America. Koma iliyonse njoyenerera mwambo wake ndipo imakwaniritsa zifuno zake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena