Thanzi ndi Malo Okhala
Yolembedwa ndi mtolankhani wa Galamukani! ku Nigeria
CHAKA chilichonse, anthu 49 miliyoni amafa padziko lonse. Pafupifupi 75 peresenti ya imfazi zimakhala zamsanga, chochititsa chake chikumakhala kuipa kwa malo okhala ndi njira ya moyo, malinga ndi lipoti la World Health Organization (WHO). Talingalirani zitsanzo zinazi:
◼ Kansa imapha anthu mamiliyoni asanu chaka chilichonse. Mbali yaikulu, WHO ikutero, “imachititsidwa kwenikweni ndi kuwonjezeka kwakukulu kwa osuta fodya m’zaka 30 zapitazi.”
◼ Matenda a kutseguka m’mimba, akumapha ana oposa mamiliyoni atatu chaka chilichonse, kaŵirikaŵiri amachititsidwa ndi zakudya ndi madzi zoipitsidwa, limodzinso ndi kusakhala ndi zimbudzi zabwino.
◼ TB, imene imapha anthu mamiliyoni atatu chaka chilichonse, imakula kumene kuli umphaŵi ndi anthu ochulukitsa, makamaka kumene kulibe ukhondo.
◼ Matenda a m’chifuŵa, makamaka chibayo, amapha mamiliyoni atatu ndi theka a ana osakwanitsa zaka zisanu chaka chilichonse. Ambiri ndi a m’tauni amene amapuma mpweya woipitsidwa kwambiri.
Pambali pa imfa zimenezi, chaka chilichonse anthu pafupifupi mabiliyoni aŵiri ndi theka—pafupifupi theka la chiŵerengero cha anthu padziko lonse—amadwala matenda amene amachititsidwa ndi madzi osakwanira kapena oipitsidwa ndi kusoŵeka kwa ukhondo. Ndiponso, WHO ikuti zodetsa nkhaŵa zotero zimene zilipo monga mvula ya asidi, muyalo wa ozoni wofoketsedwa, ndi kutentha kwa dziko lapansi zikuwononga thanzi la anthu ambiri. Onse pamodzi, lipoti la WHO linatero, anthu oposa mabiliyoni aŵiri akukhala m’malo oika moyo ndi thanzi pangozi.
Dr. Hiroshi Nakajima, woyang’anira wamkulu wa WHO, akuchenjeza kuti: “Ngati sitichitapo kanthu tsopano, vuto la Dziko Lapansi ndi okhalamo ake lidzakhala lalikulu kowopsa, ndipo malo adzakhala osakonzekanso.”
Baibulo likulonjeza kuti padzakhala nthaŵi pamene “wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) Zimenezi zidzachititsidwa, osati ndi zoyesayesa za munthu, koma ndi Ufumu wa Mulungu, umene udzachotsapo matenda ndi zochititsa zake.—Chivumbulutso 21:3, 4.
[Mawu a Chithunzi patsamba 18]
Godo-Foto