Malo Okuzungulirani—Mmene Amakhudzira Thanzi Lanu
POSACHEDWAPA, Dr. Walter Reed, wa bungwe la World Resources Institute, anauza Wailesi ya bungwe la United Nations kuti tsopano, padziko lonse, zimene munthu akuchita ku malo achilengedwe omuzungulira zafika pamlingo wakuti munthuyo “akusokoneza kwambiri dongosolo la chilengedwe.” Dr. Reed akuti kusokoneza chilengedwe chomuzungulira kumeneku, m’malo mwake kukubweretsa zinthu zoopseza thanzi la munthu padziko lapansi. M’nkhani yobwereramo m’buku lakuti World Resources 1998-99, magazini ya Our Planet, yofalitsidwa ndi bungwe la United Nations, ikundandalitsa zina mwa zinthu zoopsa ku thanzi la anthu zimenezo. Zina mwa izo ndi izi:
□ Kuwononga mpweya kwa m’nyumba ndi panja kwaonedwa kuti ndi kumene kumachititsa matenda osiyanasiyana a m’chifuwa amene amapha ana pafupifupi mamiliyoni anayi chaka chilichonse.
□ Kusoŵa madzi abwino ndi kupanda ukhondo kumachititsa kufala kwa matenda a kutsegula m’mimba amene amapha ana mamiliyoni atatu chaka chilichonse. Mwachitsanzo, kolela, matenda amene anathetsedwa kalekale ku Latin America, anabukanso kumeneko ndi kupha anthu 11,000 mu 1997 mokha.
Tsiku lililonse ana oposa 30,000 okhala m’zigawo zosaukitsitsa padziko akuti amafa ndi matenda obwera chifukwa cha malo owazungulira. Tangoganizirani chiŵerengero chimenecho—anthu 30,000 tsiku lililonse pa chaka, anthu otha kudzaza mipando yonse ya ndege 75 za mtundu wa jumbo jet!
Komabe, zinthu zoipa kuthanzi lamunthu zokhudza malo omuzungulira, si zili m’mayiko osauka okha ayi. Magazini ya Our Planet ikunena kuti “anthu opitirira 100 miliyoni ku Ulaya ndi ku North America akupumabe mpweya woipa,” zimene zimachititsa kuti matenda a chifuwa cha phumi achuluke kwambiri. Panthaŵi yomweyomweyo, kuyenderana komanso malonda a padziko lonse kwachititsa kuti pabwere matenda 30 atsopano m’mayiko otukuka. Kuphatikiza apo, magaziniyo inati matenda amene anathetsedwa kale “akubwereranso ndi mphamvu.”
Pavutira nkha7ni ndi pakuti ambiri mwa matenda ameneŵa amene ali okhudza malo angathe kupewedwa mosawononga ndalama zambiri kwenikweni malingana ndi kupita patsogolo kwa zinthu kwa masiku ano. Mwachitsanzo, umoyo wa anthu ungapite patsogolo kwambiri ngati anthu atapatsidwa madzi oyera ndi kukhala aukhondo. Kodi pangafunike ndalama zingati kuti cholinga chimenechi chitheke? Wailesi ya United Nations inalengeza kuti malingana ndi lipoti la United Nations Human Development 1998, kupereka madzi oyera ndi kukhazika mwaukhondo munthu aliyense kungawononge ndalama zokwanira madola mabiliyoni 11—zimenezi sizikukwanira n’komwe pa ndalama zimene anthu a ku Ulaya amawononga pogula aizikilimu m’chaka chimodzi chokha!
[Mawu a Chithunzi patsamba 15]
Chithunzi: Casas, Godo-Foto