Ntchentche Zonyansazo—kodi Zili Ndi Ntchito Imene Simumaganizirapo?
AMBIRI a ife timaona ntchentche kukhala zovuta kapena ngozi yeniyeni kwa anthu. Koma asayansi ya zinthu zamoyo akupeza kuti ntchentche, ndi kuvutitsa kwakeko, zili ndi ntchito imene sitimaganizirapo.
Mitundu yambiri imathera nthaŵi yaikulu patsiku kupita ku maluŵa, malo opereka zakudya zamwamsanga amene amapatsa tizilombo tinzawo madzi a m’maluŵa ndi pollen. Ntchentche zina zimene zingatulutse zakudya zomanga thupi ku pollen—ntchito yaikulu ndithu—zimadalira pa chakudya chopatsa mphamvu kwambiri chimenechi kuti zikhale ndi mazira.
Pamene zikupita ku maluŵa osiyanasiyana, ntchentchezo mosapeŵeka zimanyamula timibulu ta pollen tonambuka, timene timamamatira kumatupi awo. Ntchentche imodzi imene asayansi ya zinthu zamoyo anapenda mosamala inali ndi timibulu 1,200 ta pollen pa thupi lake! Pamene kufufuza kowonjezereka kwachitidwa pa zimene ntchentche imachita pantchito yonyamula pollen, asayansi apeza kuti maluŵa ena amadalira pa izo kuti akhale ndi moyo.
Magazini a Natural History akufotokoza kufufuza kotsatizana kumene kunachitidwa ku Colorado, North America. Ntchentche wamba za muscoid, zimene zimafanana ndi ntchentche za m’nyumba, anazithira fumbi la maonekedwe oŵala kotero kuti zizioneka mosavuta. Ataona zochita zake zatsiku ndi tsiku, ofufuzawo anadabwa kuona kuti kwa maluŵa ena akuthengo ntchentche zimenezi ndizo zobweretsa pollen zofunika kwambiri kuposa njuchi ndi kuti zimafika patali kuposa njuchi.
Kodi ntchito ya ntchentche njofunika motani? Maluŵa ena anaphimbidwa ndi ukonde kotero kuti pasakhale tizilombo tilitonse. Maluŵa ameneŵa sanatulutse mbewu zilizonse—kusiyana kwambiri ndi obala oyandikana nawo amene analandira pollen kuchokera ku ntchentche. Ngakhale kuti maluŵa ena kwakukulukulu analandira pollen kuchokera ku njuchi, kwa mitundu ina monga wild flax kapena wild geranium, m’malo ena ntchentche zinachita 90 peresenti ya ntchitoyi.
Kodi nchiyani chimene Carol Kearns ndi David Inouye, aŵiri a ofufuzawo, anapeza? ‘Motero, kwa maluŵa ambiri a m’thengo mu Colorado Rockies, ntchentche zimaposa njuchi, agulugufe, ndi ma hummingbird . . . Popanda tizilombo timeneti, timene anthu ambiri amationa kukhala tonyansa, maluŵa ambiri a kuthengo amene amachititsa ulendo wa kumadambo akumapiri kukhala wosangalatsa kwambiri angalephere kutulutsa mbewu.’ Mosakayikira, ntchentche zili ndi ntchito yake!