Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 7/8 tsamba 9-10
  • Kodi Muli Wokonzekera Tchuti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Muli Wokonzekera Tchuti?
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Matchuti Ali ndi Malo Awo
  • Kuyenda Ulendo, Maphunziro Paokha
  • Kukonzekera Bwino
  • Sangalalani Ndi Matchuti Popanda Chisoni!
    Galamukani!—1996
  • Zimene Muyenera Kusamala Nazo
    Galamukani!—1996
Galamukani!—1996
g96 7/8 tsamba 9-10

Kodi Muli Wokonzekera Tchuti?

CHILIMWE ku Northern Hemisphere chayandikira. Posapita nthaŵi mamiliyoni ambiri adzakhala akupita kutchuti. Koma matchuti samangokhala m’chilimwe chokha. Kuona malo kwafikira kukhala malonda aakulu a chaka chonse, obweretsa ndalama zochuluka koposa pachaka. Ngakhale kuti opita kutchuti ambiri amamka kumalo a m’dziko lawo, kumka kumaiko akunja, kumene panthaŵi ina kunali kwa olemera okha, tsopano kwafala.

Nthaŵi ya tchuti yoperekedwa ndi olemba ntchito imasiyanasiyana m’maiko. Mu 1979, 2 peresenti yokha ya antchito a ku Germany anapatsidwa tchuti cha milungu isanu ndi umodzi, koma tsopano unyinji wawo umapatsidwa. Avareji ya tchuti ya antchito a m’maindasitale ku Western Europe imapitirira pa milungu isanu.

Matchuti Ali ndi Malo Awo

Ajeremani amakonda kutcha matchuti kuti “milungu yabwino koposa ya chaka.” Komanso, omwerekera ndi ntchito angaone masiku a tchuti amakono kukhala opanda kanthu, opanda zochita zaphindu. Komano limeneli lingakhale lingaliro lomkitsa. Munthu wolingalira moyenera amavomereza nzeru ya kupuma kwa nthaŵi ndi nthaŵi pa mchitidwe wamasiku onse, akumachita zinthu zina, ndi kukhala womasuka.

Mbali zabwino za matchuti zinatsimikiziridwa pakufufuza kwa 1991 kwa akuluakulu azamalonda a ku Ulaya, amene 78 mwa 100 alionse ananena kuti matchuti “ngofunika kwambiri kuti mkulu wapantchito asatheretu.” Anthu atatu mwa anayi alionse analingalira kuti matchuti anawongolera kagwiridwe ka ntchito, ndipo oposa anthu aŵiri mwa atatu alionse anati matchuti anawongolera luso. Mokondweretsa, 64 peresenti ya akazi ndi 41 peresenti ya amuna anagwirizana pa mawu awa: “Popanda kupita patchuti nthaŵi ndi nthaŵi ndikhoza kusokonezeka maganizo.”

Kuyenda Ulendo, Maphunziro Paokha

M’zaka za zana la 17, dokotala wachingelezi ndi mlembi Thomas Fuller analemba kuti: “Munthu amene amayenda kwambiri amadziŵa zambiri.” Kuyenda kumatipatsa mwaŵi wa kudziŵana ndi anthu a kumalo ena, kuphunzira za miyambo yawo ndi moyo wawo. Kuyenda m’maiko amene ali osaukirapo kuposa kwathu kungatiphunzitse kukhala oyamikira zimene tili nazo ndipo kungadzutse mwa ife malingaliro a kuchitira chifundo anthu osoŵa kuposa ife.

Ngati tikulola, kuyenda kungawongolere malingaliro olakwa ndi kuchepetsa tsankhu. Kumapereka mpata wa kuphunzira, mwinamwake pang’ono pokha, chinenero chatsopano, kulaŵa chakudya chosiyanasiyana chimene chingatikomere, kapena kukulitsa alabamu ya banja lathu ya zithunzi, masilaidi, kapena laibulale ya mavidiyo ya zithunzithunzi za chilengedwe chokongola cha Mulungu.

Zoonadi, kuti tipindule koposa, tiyenera kuchita zochuluka kuposa kungoyenda. Oona malo amene amayenda theka la dziko ndi kukabindikira m’hotela pakati pa oona malo anzawo—ochuluka a iwo ali akumudzi kwawo—kukasambira m’dziŵe la pa hotela kapena kugombe, ndi kudya chakudya chimene amadya nthaŵi zonse kwawo sangaphunzire zambiri. Nzachisoni chotani nanga! Malinga ndi malipoti, zikuchita ngati unyinji wa oyenda maulendo amalephera kukhala ndi chidwi chachikulu m’maiko amene amayendamo kapena mwa anthu a kumeneko.

Kukonzekera Bwino

Samuel Johnson, wolemba nkhani ndi ndakatulo wachingelezi wa m’zaka za zana la 18, ananena kuti munthu amene amayenda ulendo “ayenera kukhala ndi chidziŵitso, ngati akufuna kumka ndi chidziŵitso kwawo.” Chotero ngati muli ndi nthaŵi ya kudzayenda, konzekerani ulendo wanu. Ŵerengani za kumene mukupita musanapiteko. Konzani zimene mukufuna kukaona, ndi kusankha zimene mukufuna kuchita. Ndiyeno linganizani zinthu malinga ndi zimenezo. Mwachitsanzo, ngati mukufuna kukayenda kugombe kapena kukakwera mapiri, tengani nsapato ndi zovala zoyenera.

Musayese kupanikizira zinthu zambiri pa mndandanda wanu ndipo mwa kutero mukumasenza zopsinja za moyo watsiku ndi tsiku kumka nazo kutchuti chanu. Sungani nthaŵi yambiri yopanda zochita kaamba ka zinthu zamwadzidzidzi. Limodzi la mapindu enieni a kukhala pa tchuti ndilo kukhala ndi nthaŵi ya kuganiza ndi kusinkhasinkha popanda kupanikizika ndi mndandanda wosasinthika, kumva kukhala womasuka pa kupsinjika ndi kusunga nthaŵi kopanikiza kumeneko.

Tchuti chofupa kwambiri chingaphatikizepo kugwira ntchito zolimba. Kuchita kanthu kena kaŵirikaŵiri ndiko mfungulo ya tchuti chabwino. Mwachitsanzo, gulu lina losachita malonda ku United States lotchedwa Volunteer Vacations limalinganiza kuti antchito odzifunira azitha matchuti awo akumasamalira nkhalango zosungirako nyama kapena nkhalango wamba. Wantchito wina wodzifunira ananena kuti anagwira ntchito zolimba, koma anasangalala nayo kwambiri kwakuti anasankha za kubwerezanso zimenezo chaka chotsatira.

Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri zimagwiritsira ntchito matchutiwo kumka ku misonkhano yachikristu kapena kupititsa patsogolo utumiki wawo wapoyera. Ena amagwiritsira ntchito matchuti awo kugwira ntchito pa malikulu kapena pamaofesi anthambi za Mboni za Yehova m’maiko akwawo, ndipo amasangalala ndi ntchitoyo. Pambuyo pake ambiri a ameneŵa amalemba makalata oyamikira mwaŵiwo.

Inde, matchuti angakhale osangalatsa koposa, ngakhale kukhala milungu yabwino koposadi ya chaka. Nchifukwa chake ana amayembekezera masikuwo kufikira atadza! Komabe, pali zinthu zimene mufunikira kusamala nazo. Nkhani yotsatira idzafotokoza zimenezi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena