Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 7/8 tsamba 14-16
  • Sangalalani Ndi Matchuti Popanda Chisoni!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Sangalalani Ndi Matchuti Popanda Chisoni!
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Khalani Wosapambanitsa
  • Sungani Maunansi Abwino
  • Zimene Zikuchirikizidwa?
  • Chititsani Tchuti Kukhala Nthaŵi Yofupa
  • Kodi Muli Wokonzekera Tchuti?
    Galamukani!—1996
  • Zimene Muyenera Kusamala Nazo
    Galamukani!—1996
Galamukani!—1996
g96 7/8 tsamba 14-16

Sangalalani Ndi Matchuti Popanda Chisoni!

PAMENE munthu wina wa ku America amene tsopano akukhala ku Ulaya, anafunsidwa za mmene iyeyo anasangalalira ndi ulendo wake kumalo ena otchuka atchuti, anayankha kuti: “Malowo ayenera kukhala anali okongola anthu asanafikeko.” Kodi mwakhalapo ndi malingaliro onga ngati ake? Mdadada wa mahotela ndi madisiko, gombe loipitsidwa ndi la anthu ambirimbiri, ndi mawailesi obangula sizimasangalatsa aliyense kumalo a tchuti.

Nzomvetsa chisoni kunena kuti si nthaŵi zonse pamene matchuti amatiyendera bwino. M’malo motitsitsimula, amatithetsa mphamvu; m’malo motipatsa nyonga, nthaŵi zina amatichititsa kufuna kupuma kwambiri. Motero, funso loyenera nlakuti, Kodi tingasangalale motani ndi matchuti popanda chisoni?

Khalani Wosapambanitsa

Mofanana ndi zokoleretsa chakudya, matchuti amatulutsa zabwino koposa pamene agwiritsiridwa ntchito mwakamodzikamodzi. Ngakhale kuti moyo wa munthu wolemera wodziŵika amene nthaŵi zambiri amayenda maulendo apandege ungaoneke kukhala wokopa, uwo uli wopambanitsa ndipo sudzetsa chimwemwe chenicheni.

Kusawawanya ndalama kuli kofunika makamaka pa matchuti. Linganizani zinthu bwino musanapite, ndipo yesani kugwiritsira ntchito ndalama zolingana ndi bajeti yanu. Peŵani kunyengedwa ndi makonzedwe apadera ochitidwa ndi makampani azaulendo amene angakulimbikitseni “kusangalala tsopano lino, ndi kulipira pambuyo pake.”

Ndiponso, musawopsedwe kwambiri ndi ngozi zokhoza kuchitika kwakuti mzimu wachikondwerero ndi wosada nkhaŵa umene umachititsa tchuti kukhala chokopa nkutsekerezedwa. Ndiponso, kuchita zinthu moyenera kumaphatikizapo kudziŵa ngozi yaikulu koposa imene ingatichititse kukumbukira za tchuti chathu mwachisoni. Simakhudza za ngozi, nthenda, kapena upandu wina koma, m’malo mwake, nja maunansi a munthu.

Sungani Maunansi Abwino

Matchuti ochitidwa limodzi ndi banja ndi mabwenzi ena angalimbitse chikondi. Komanso, matchuti angachititse kusweka kwa unansi, umene ungakhale wovuta kuukonzanso. Mtolankhani Lance Morrow anati: “Ngozi ya tchuti ili pa kukhoza kwake kuchititsa mikangano yonse ya banja kukhala yoonekera kwambiri ngati zochitika m’seŵero . . . Anthu m’moyo wawo wamasiku onse ali ndi ntchito, mathayo, mabwenzi ndi njira zamasiku onse zochitira ndi kupsinjika mtima. M’nyumba zokhalamo m’chilimwe, nkhani za m’banja zimene zinachitika zaka 20 zapita zikhoza kuvumbuluka ngati nkhanu.”

Chotero musanapite ku tchuti, tsimikizirani ndi mtima wonse kuchipangitsa kukhala chochitika chosangalala. Kumbukirani kuti munthu aliyense ali ndi zimene amakonda. Ana angafune kudziŵa zinthu zatsopano, mwina makolo angafune kupuma. Khalani wokonzekera kulepa kwa ena zimene mungakonde kuchita ndi kumene mungakonde kupita. Ngati kuli kwanzeru ndi kothandiza, vomerani kulola aliyense nthaŵi ndi nthaŵi kuchita zimene zimamkondweretsa. Phunzirani kusonyeza mikhalidwe ya mzimu wa Mulungu masiku onse chaka chonse, ndipo kupitiriza kuchita motero sikungakhale kovuta mkati mwa tchuti chanu.—Agalatiya 5:22, 23.

Pamene kuli kwakuti kusunga unansi wabwino ndi banja ndi mabwenzi kuli kofunika, unansi wathu ndi Mulungu ngwofunika koposadi. Pamatchuti kaŵirikaŵiri timakumana ndi anthu amene ali ndi lingaliro losiyana ndi lathu lachikristu ponena za Mulungu ndi zofunika zake. Kuyanjana nawo kwambiri—mwinamwake ngakhale kukhala ndi chizoloŵezi cha kupita kumalo osangulutsa okayikitsa—kungachititse zomvetsa chisoni. Kumbukirani kuti Baibulo limachenjeza kuti: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.”—1 Akorinto 15:33.

Pamene muli patchuti, ngati muzindikira za chikhumbo china cha kufuna kusiya miyezo ndi zizoloŵezi zachikristu ndi machitidwe, limbanani ndi chofooka chimenecho mwanzeru ndi kupempha thandizo la Mulungu la kulimbana ndi chikhumbo chimenecho!

Zimene Zikuchirikizidwa?

Anthu amene samaumba moyo wawo mogwirizana ndi mapulinsipulo achikristu angalingalire kuti pamene ali patchuti zilizonse nzololeka. M’maiko ena a azungu, kuona malo kofuna ogonana nawo ndiko malonda aakulu, ndipo makampani ena a zamaulendo amakuchirikiza. The European ikulemba kuti ‘zinthu zonyansa zimene amuna achizungu amachita m’malo atchuti a mizinda ina ya ku Asia zadziŵika ndi anthu ambiri kwa nthaŵi yaitali.’ Potchula za dziko lina la ku Asia, magazini achijeremani Der Spiegel anayerekezera kuti pafupifupi 70 peresenti ya alendo onse achimuna ali “oona malo ofuna ogonana nawo.”

Akazi oona malo tsopano akutsatira zochita za anzawo achimuna. Kampani ina ya ndege zahayala ya ku Germany imene imachita maulendo a ku Caribbean ikuyerekezera kuti 30 peresenti ya mapasinjala ake achikazi amamka kumeneko patchuti kokha ndi chifuno cha kukagonana ndi ena. The European inagwira mawu mtolankhani wachijeremani kukhala akunena kuti: “Amaona zimenezi kukhala njira yofeŵa ndi yosavuta yopezera chikondwerero—seŵero la ku malo achilendo.”

Komabe, Akristu oona samaona chiŵereŵere monga njira yosangulukira yololeka. Chimaswa mapulinsipulo achikristu ndipo nchodzala ndi ngozi. Ngakhale kuti amadziŵa za ngoziyo, anthu ambiri amangoyesa kupeŵa zotulukapo zake m’malo mwa kuleka mchitidwewo. Chitsanzo chimodzi ndi chija chopezeka m’manyuzipepala a ku Germany osonyeza sumbulele ndi mipando iŵiri ya kugombe yopanda anthu. Mawu ake amati: “Yendani bwino, ndipo mukabwereko wopanda AIDS.”

Chipatso chonyansa cha oona malo ofuna ogonana nawo ndicho kugona ana. Makamaka, mu 1993 boma la Germany linakhazikitsa lamulo lopangitsa Ajeremani kulangidwa ngati atapezedwa ndi mlandu wa kugona ana—ngakhale pamene ali patchuti kumaiko akunja. Komabe, kufikira pano, pakhala zotulukapo zabwino zochepa. Kuchititsa ana uhule kwakhala—ndipo kudzakhalabe—mkhalidwe wonyansa ndi wosautsa m’chitaganya cha anthu.

Chititsani Tchuti Kukhala Nthaŵi Yofupa

Kuŵerenga, kuphunzira Baibulo, ndi kuloŵa mu utumiki wachikristu ndiko zochita za Akristu oona zokondweretsa ndi zofupa. Koma ambiri amavutika kupeza nthaŵi yokwanira kuti achite zinthu zimenezi kufikira pamlingo umene angakonde. Kodi pangakhalenso nthaŵi ina yabwino koposa imeneyo yochitira zimenezo pamene muli womasuka patchuti?

Zoonadi, tchuti chotangwanitsa ndi chokhutiritsa sichingakuloleni kuchita zinthu zachikristu kufikira pamlingo umene mumafikako nthaŵi zonse. Komano bwanji osapatula nthaŵi ina yake ya kuchita ntchito yauzimu yolimbikitsa? Zimenezi zidzasiyabe nthaŵi ya kusangulutsa. Ndithudi, ena amagwiritsiradi ntchito nthaŵi yowonjezereka imene amakhala nayo pamatchuti kufutukula utumiki wawo. Monga momwe Yesu ananenera, “achimwemwe ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.”—Mateyu 5:3, NW.

Nanunso mwina mudzakhala mukupita kutchuti posachedwapa. Ngati zili choncho, tsimikizirani kukasangalala nacho bwino! Musawope mopambanitsa ngozi zimene zingachitike, komano khalani osamala moyenerera. Kumbukirani malingaliro onga awo opezeka m’bokosi patsamba lino. Pambuyo pake, bweraniko muli wotsitsimulidwa, mutapuma, ndi wofunitsitsa kupitiriza zochita zanu m’moyo zimene zili zofunika koposa. Tchuti sichichedwa kutha, komano mudzakumbukira zinthu zake zina zapadera kosatha. Ha, nchamtengo wapatali chotani nanga—tchuti chochitidwa popanda chisoni!

[Bokosi patsamba 16]

Malangizo Angapo a Patchuti

Chenjerani ndi Akuba

1. Linganizani kuti winawake aziyang’anira zinthu kunyumba kwanu.

2. Peŵani madera amene ali odziŵika kwambiri kukhala angozi.

3. Chenjerani ndi opisa m’matumba, ikani ndalama pamalo abwino pathupi panu, ndipo siyani ndalama zambiri kumalo otetezereka kumene mukukhala.

4. Samalani ndi anthu achilendo ofuna kukuthandizani.

Peŵani Ngozi

1. Ngati mukuyendetsa galimoto, khalani watcheru, ndipo pumani kaŵirikaŵiri.

2. Pamene mukukhala m’mahotela kapena pamene mukuyenda pandege, dziŵani bwino zochita pangozi.

3. Lolani nthaŵi yakuti thupi lizoloŵere musanayambe zochitika zina zofuna nyonga.

4. Khalani ndi zovala zoyenera, nsapato, ndi zipangizo za zochita zanu.

Sungani Thanzi Labwino

1. Pemphani dokotala wanu kuti akulangizeni pa akatemera kapena mankhwala ofunikira.

2. Tengani thumba la mankhwala la paulendo lokhala ndi mankhwala ofunika.

3. Pumani mokwanira, ndipo samalani zimene mukudya ndi kumwa.

4. Nthaŵi zonse sungani ziphaso zofunika pathupi panu za mankhwala anu ofunika kapena za zofuna zanu.

Sungani Maunansi Achimwemwe

1. Sonyezani chikondi ndi kulingalira awo amene muli nawo.

2. Sungani miyezo yapamwamba ponena za mayanjano anu.

3. Musalole apatchuti ena kukutsogolerani kuchita zimene mukukayikira.

4. Patulani nthaŵi ya kukhutiritsa njala yauzimu.

[Zithunzi patsamba 15]

Sankhani zochita zabwino pamene muli patchuti

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena