Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 7/8 tsamba 11-13
  • Zimene Muyenera Kusamala Nazo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zimene Muyenera Kusamala Nazo
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Tetezerani Zinthu Zanu Zamtengo Wapatali
  • Peŵani Ngozi
  • Sungani Thanzi Labwino
  • Sangalalani Ndi Matchuti Popanda Chisoni!
    Galamukani!—1996
  • Kodi Muli Wokonzekera Tchuti?
    Galamukani!—1996
Galamukani!—1996
g96 7/8 tsamba 11-13

Zimene Muyenera Kusamala Nazo

“CHIFUNO chodziŵika cha matchuti ndicho kuchita zinthu zina, kusanguluka kwa kanthaŵi, kusintha zochita zamasiku onse,” analemba motero mtolankhani Lance Morrow. Komabe, iye anati ena amafika kwawo kuchokera ku tchuti ali otheratu kwakuti amalumbira “kusadzapitanso.”

Komabe, m’malo mwa kungoiŵala lingaliro la kupita kumatchuti, kungakhale kwanzeru kupenda pasadakhale mbuna zimene zingakhalepo ndi kutsatira njira zozipeŵera.

Tetezerani Zinthu Zanu Zamtengo Wapatali

Ambiri abwera ku tchuti ndi kupeza kuti nyumba yawo inathyoledwa pamene anachokapo. Chotero musanachoke kumka kutchuti, pemphani mabwenzi kapena anansi anu kuti azizonda nyumba yanu nthaŵi zonse. Nthaŵi zina akhozadi kukhala pamenepo kuti apachititse kuoneka ngati mulipo. Apempheni kutenga manyuzipepala anu ndi kuchotsa makalata m’bokosi lanu la makalata tsiku lililonse, pakuti palibe chinthu chimene chimadziŵitsa za kuchokapo kwanu koposa mulu wa manyuzipepala kapena bokosi lanu la makalata lodzala ndi makalata osachotsedwamo.

Mufunikiranso kutetezera zinthu zanu zamtengo wapatali pamalo anu atchuti. M’maiko ena anthu akumaiko ena amaonedwa kukhala olemera, ndipo wodzaona malo aliyense akhoza kuberedwa. Chotero, chizoloŵezi chabwino ndicho kusiya ndalama zina ndi ziphaso zina ku hotela zili pabwino kapena pamalo ena osungika. Khalani wochenjera ndi anthu achilendo, komano wokoma mtima.

Chaka chilichonse Miami, Florida, ku U.S.A., amalandira alendo ndi anthu akomweko mamiliyoni ambiri apatchuti. Apandu amakhaladi ali yakaliyakali m’madera atchuti otero. Magazini a Time anasimba kuti mkati mwa 1992, “ku Florida kokha, odzaona malo, alendo ndi anthu akomweko 36,766 anaphedwa, kugwiriridwa chigololo, kuberedwa kapena kuwachitira zoipa zina.”

Pamene muli patchuti, samalani makamaka ndi opisa m’matumba. Amuna ayenera kusunga chikwama chawo cha ndalama pamalo obisika ndi otetezereka, monga ngati m’thumba lawo lamkati kapena m’thumba lawo lakutsogolo la buluku. Oyenda ulendo odziŵa bwino kaŵirikaŵiri amabisa ndalama mwanjira zaluso. Mwachitsanzo, ena amatenga ndalama zawo, mapasipoti, ndi mavisa m’kachikwama kaphanthiphanthi komangiriridwa m’khosi mwawo ndi kukaphimba ndi zovala zawo. Akazi ayenera kusamala kuti mwina okwera njinga zopalasa kapena njinga zamoto angafikire ndi kutsomphola zikwama zimene amakoloweka papheŵa.

Apandu akupezabe njira zatsopano zolalira oona malo. Mapasinjala omagona m’sitima zomka kumitunda yakutali m’maiko a Azungu, aberedwa usiku. Mankhwala ogonetsa angapoperedwe m’chipinda cha sitima kuti achititse omwe alimo kusagalamuka pamene katundu wawo akufunkhidwa. Panthaŵi ina, malinga ndi kunena kwa The European, “kukulingaliridwa kuti mbala zinatsika bwinobwino m’sitima zili ndi ndalama zoposa $845,000 ndi katundu wakuba.”

Peŵani Ngozi

“Mankhwala okha amene ndili nawo pa vuto la ngozi zachizoloŵezi,” anatero wanthabwala Robert Benchley, “ndiwo kugona pa bedi tsiku lonse.” Komano iye anawonjezera kuti: “Ngakhale uli pamenepo, nkotheka kuti mukhoza kugwapo.” Mfundo yake njakuti, ngozi zimachitika kulikonse! Chotero kuwopa ngozi pamene muli patchuti sikuyenera kukuchititsani kukhala kunyumba. Koma pali chifukwa china chapadera chofuna kuti musamale pamene muli patchuti.

Mayendedwe a galimoto angakhale onyenga mkati mwa nyengo za tchuti. Ajeremani afikira pa kuzoloŵera mzera wa makilomita 80 kutalika wa galimoto mkati mwa nthaŵi zimenezo. Magazini a Time a August 14, 1989, anati: “Sabata latha mu Ulaya yense, miyandamiyanda ya mabanja inayamba holide yawo yamwambo ya August—ndipo munthu aliyense anavutika. . . . Misewu yonse yaikulu ya Paris inadzazidwa mosatheka kuyenda. . . . Pakati pa July 28 ndi Aug. 1, anthu 102 anafa pa kugundana kwa galimoto.” Chotero, mwanzeru imani pang’ono kuti mumasuke thupi louma chifukwa cha kuimaima kwa galimoto.

The European inasimba za malangizo akuti oyendetsa galimoto “asamayambe maulendo awo kufikira pa Sande—kapena kuyenda usiku.” Koma inavomereza kuti opita kutchuti ochuluka “amaumirirabe kuyamba kuyenda panthaŵi yofanana.” Chotulukapo chake? Ulaya wa galimoto zotsekerezana. Ngakhale kuti kuli kwanzeru kuyenda ulendo pamene misewu ili ndi galimoto zochepa, musanyalanyaze kuti kuyenda usiku kungakhale kwangozi. Munthu samaona bwino usiku, nchifukwa chake pamakhala ngozi zowonjezereka. Mmamaŵa kwambiri ingakhale nthaŵi yabwino kwambiri ya kuyenda ulendo.

Musanyalanyaze zinthu zina zimene zingachititse ngozi mutafika kumalo anu atchuti. Ngati simunachite mwankhongono mbali yokulira ya chakacho, mungadzivulaze m’thupi ngati muchita mosayenera. Chotero ikani malire a maseŵero pamasiku oyamba oŵerengeka, pamene thupi lanu likhoza kuvulala.

Sungani Thanzi Labwino

Malinga nkunena kwa buku lakuti 2,000 Everyday Health Tips for Better Health and Happiness, “matenda odziŵika koposa amene anthu oyenda amadwala pa maulendo akutsidya lanyanja amawatenga m’chakudya, madzi ndi nthenda zingapo zopatsirana.” Makampani othandiza apaulendo angapereke malangizo onena za mmene angapeŵere mavuto amenewo, ndipo kutsatira malingaliro awo kumathandiza.

M’mbali zambiri nkofunika kupeŵa kumwa madzi apampope. Ndipo kumbukirani kuti ma ice cube mwina amapangidwa ndi madzi amenewo. Kungakhalenso kwanzeru kupeŵa kudya masamba, mayonnaise, chakudya chokhala ndi cream, nyama yaiŵisi kapena yofutsa, nkhono, ndi zipatso zaziŵisi, pokhapo ngati mwazisenda inu mwini. M’Madera Otentha, muyenera kuŵiritsa mkaka wamadzi musanaumwe.

Ngozi yaikulu kwa apatchuti osavala zochuluka ndiyo dzuŵa, ndipo m’zaka zaposachedwapa ngoziyo yawonjezereka mofulumira chifukwa cha kuchepa kwa ozoni kuthambo. Chiŵerengero cha odwala nthenda yatsopano ya melanoma yoipa, kansa ya pakhungu yowopsa kwambiri, chinaŵirikiza kaŵiri ku United States pakati pa 1980 ndi 1993. Anthu aona masikipa ku Australia okhala ndi mawu akuti “SLIP! SLOP! SLAP!” (Valani shati, dzolani mafuta otetezera dzuŵa, ndipo valani chipeŵa.) Komatu musakopeke ndi lingaliro lonyenga. Mafuta otetezera dzuŵa ali osadalirika.

Ulendo wapandege wodutsa madera angapo a nthaŵi zosiyana ungachititse munthu kutopa. Ngakhale kuti kumeneku sikuli nthenda, kutopa kumeneku kumasokoneza kugwira ntchito bwino kwa thupi la munthu, makamaka ngati munthuyo ali wodwaladwala. Kufufuza kumene kunachitidwa pa oyenda ulendo wapandege pakati pa London ndi San Francisco, madera amene ali osiyana ndi maola asanu ndi atatu, kunavumbula kuti “kuti maganizo a munthu azoloŵere . . . panafunikira masiku osachepera asanu ndi aŵiri kufikira khumi.” Buku lakuti The Body Machine linasimbanso kuti oyenda ulendo ena amene anadutsa mofulumira madera angapo a nthaŵi zosiyana anali ndi “chikhoterero cha kukhala osalankhula, ozengereza ndi okhoza kuphophonya kuŵirikiza kaŵiri. Kusumika maganizo ndi kukumbukira zinthu nakonso kunasokonezeka.”a

Ndiponso, ulendo wapandege umawanditsa nthenda kuchokera ku kontinenti imodzi kumka ku ina m’maola oŵerengeka chabe. Nyuzipepala ya ku Germany Nassauische Neue Presse inati: “Madokotala akuvutika maganizo kwambiri chifukwa cha nthenda ‘zachilendo’ monga ngati malungo kapena hepatitis zimene apatchuti amabweretsa kuchokera ku Afirika, Asia, kapena ku South America. Chaka chilichonse Ajeremani 2,000 amabwerera kwawo ndi malungo.” Chaola chitapha anthu mu India mu 1994, njira zamphamvu zochiletsa kuwanda m’maiko ena zinatengedwa.

Anthu odwaladwala, ndiponso akazi okhala ndi pakati, ayenera kusamala kwambiri poyenda ulendo. Ngakhale kuti nthaŵi zambiri pamakhala palibe chifukwa chowakakamiza kusayenda, iwo ayenera kufunsa dokotala wawo pasadakhale. Kuli kwanzeru kwa aliyense amene akuyenda ulendo kukhala ndi dzina, keyala ndi nambala za telefoni za bwenzi kapena wachibale wina amene angadziŵitsidwe patachitika ngozi.

Munthu amene amafunikira kumabayidwa majekeseni a insulin kuchititsa shuga ya m’mwazi wake kukhala pamlingo woyenera ayenera kukumbukira kuti kudutsa madera anthaŵi angapo kudzasokoneza programu yake yofunikira kusamala ya kadyedwe ndi majekeseni. Adzafunikira kulinganiza zinthu malinga ndi zimenezo. Kapena woyenda ulendo wokhala ndi chiŵiya chothandiza mtima kugunda ayenera kutsimikizira kuti watenga nambala ya telefoni ya dokotala wake wa mtima.

Ndiponso, aliyense wodalira pa mankhwala ena akutiakuti afunikira kukhala nawo m’katundu wake wapamanja chifukwa chakuti ngati katundu atayika kapena asokera zingakhale zachisoni. Kusasintha zovala kwa masiku angapo kungakhale kosakondweretsa; kusagwiritsira ntchito mankhwala kwa maola oŵerengeka okha kungaike moyo pangozi.

Ngozi za patchuti siziyenera kupeputsidwa. Komabe, si nthaŵi zonse pamene kumakhala chokuwopsezani kuti musachoke panyumba. Ingokhalani wosamala. Kumbukirani: Kukonzekera bwino kumathandiza pa kuletsa ngozi. Tsatirani uphungu wanzeru wakuti: “Munthu wochenjera amaona zovuta zikubwera nabisala; wopusa amangopitirira nalipitsidwa.”—Miyambo 22:3, The New English Bible.

[Mawu a M’munsi]

a Kuti mupeze mfundo zina ponena za kutopa paulendo wapandege, onani Galamukani!, wachingelezi wa June 8, 1986, masamba 19-21.

[Chithunzi patsamba 13]

Pamene muli patchuti, samalani ndi zimene mukudya

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena