Kugwetsa Makoma ndi Kumanga Maulalo
SITINACHITE kusankha banja kapena mtundu umene tinabadwiramo, ndipo sitinachite kusankha chikhalidwe chimene tinafuna kuti chiumbe kaganizidwe kathu. Tinalibe mphamvu pa zinthuzo. Tonsefe timalamuliridwa ndi nthaŵi ndi zochitika. Koma tingalamulire njira imene timaonera ena ndi mmene timachitira nawo.
Baibulo limafotokoza mmene tingachitire zimenezo. Talingalirani mapulinsipulo angapo amene adzatithandiza kumanga maulalo a kulankhulana ndi aja amene angakhale atakulira ku malo a chikhalidwe chosiyana ndi chathu.
“Mulungu amene analenga dziko lapansi ndi zonse zili momwemo, . . . ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.” (Machitidwe 17:24, 26) Ife tonse tili a banja limodzi laumunthu chotero tili ofanana kwambiri. Kufunafuna zinthu zimene timafananapo kumapeputsa kwambiri kulankhulana. Ife tonse timafuna mabwenzi abwino ndipo timafuna kuona kuti tikukondedwa ndi kulemekezedwa. Aliyense amafuna kupeŵa kupweteka kwa thupi ndi mtima. Anthu a chikhalidwe chilichonse amakonda nyimbo ndi umisiri, amasimba nthabwala, amakhulupirira kuti anthu ayenera kumalemekezana, ndipo amafunafuna njira yokhalira achimwemwe.
“Musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini.” (Afilipi 2:3) Zimenezi sizikutanthauza kuti tiyenera kulingalira kuti anzathu amatiposa m’zonse. M’malo mwake, tiyenera kuzindikira kuti m’mbali zina za moyo, ena amatiposa. Sitiyenera kuganiza kuti ifeyo kapena chikhalidwe chathu chili ndi zabwino zonse.
“Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma.” (Agalatiya 6:10) Kungoyamba kukhala waubwenzi ndi wothandiza kwa ena, ngakhale kuti ali ndi chikhalidwe chawo, kungathandize kwambiri kuthetsa kusalankhulana.
“Mudziŵa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.” (Yakobo 1:19) Anthu odziŵa kulankhulana samangokambitsirana chabe; amamvetsetsana.
“Uphungu wa m’mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo.” (Miyambo 20:5) Khalani atcheru kuzindikira malingaliro ndi zinthu zina zobisika zimene zimachititsa khalidwe la munthu. Adziŵeni bwino anthu.
“Munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.” (Afilipi 2:4) Khalani wachifundo mwa kuona zinthu malinga ndi mmene munthu winayo akuzionera. Musakhale wadyera.
Kusiyanasiyana Chikhalidwe Pakati pa Mboni za Yehova
Umboni wakuti mapulinsipulo ameneŵa amagwiradi ntchito ukusonyezedwa ndi umodzi wodabwitsa wa Mboni za Yehova, zokangalika m’maiko 232 padziko lonse. Iwo ndi anthu ochokera mwa “mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe,” amene ali otsimikiza kutsatira chitsogozo chachikondi cha Yehova m’zinthu zonse.—Chivumbulutso 7:9; 1 Akorinto 10:31-33.
Mboni iliyonse payokha simaipidwa ndi chikhalidwe cha ena. Ngakhale aja amene amakhala Mboni samasiya chikhalidwe chimene anakuliramo, ngati sichiwombana ndi mapulinsipulo a Baibulo. Pochita zimenezo amasintha moyo wawo. Amazindikira kuti chikhalidwe chilichonse chili ndi mbali zake zotamandika ndi kuti zimenezo zimalimba mwa anthu amene amalandira kulambira koona.
Amayesa kuona pulaneti lathu monga momwe Mulungu mosakayikira amalionera—loŵala ndi labluu ndi lokongola—likumazungulira m’mlengalenga. Ndi pulaneti lokhala ndi anthu osiyanasiyana ndi chikhalidwe chosiyanasiyana. Mboni za Yehova zikuyembekezera nthaŵi pamene dziko lonse lapansi lidzasangalala ndi moyo monga banja limodzi logwirizanadi.
[Chithunzi patsamba 8]
Mboni za Yehova zaphunzira mmene zingagwetsere zopinga za chikhalidwe