Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 8/8 tsamba 25-26
  • Nyama Zokhala Pangozi Mmene Inu Mukuloŵetsedweramo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyama Zokhala Pangozi Mmene Inu Mukuloŵetsedweramo
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chingalaŵa Chopulumukira
  • Nyama m’Dziko Latsopano
  • “Nowa Anayenda ndi Mulungu Woona”
    Nsanja ya Olonda—2013
  • Nyama Zokhala Pangozi Kukula—Kwa Vutolo
    Galamukani!—1996
  • “Anayenda Ndi Mulungu Woona”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Nowa Akhoma Chingalawa
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 8/8 tsamba 25-26

Nyama Zokhala Pangozi Mmene Inu Mukuloŵetsedweramo

NJUZI, nkhasi, zipembere, agulugufe—inde, mpambo wa nyama zokhala pangozi ukuoneka kukhala wosatha! Mosakayikira mukuvomereza kuti munthu ndiye ali ndi thayo lalikulu. Koma kodi zimenezi zimakukhudzani motani?

Chifukwa cha vuto la zachuma la dziko lonse, kodi kuli koyenera kuyembekezera kuti anthu odera nkhaŵa za umoyo wawo angachirikize maprogramu a kutetezera nyama, ngakhale kuti angakhale abwino motani? “Sikwapafupi konse kuchirikiza nkhani za malo okhala kumadera ochuluka a Afirika kummwera kwa Sahara, kumene anthu mamiliyoni ambiri akuyang’anizana ndi chipwirikiti cha ndale, nkhondo za mafuko, njala ndi miliri ya matenda,” ikutero Time. Ndi mmenenso zilili kwina.

Pafunikira masinthidwe aakulu kuti vuto la nyama zokhala pangozi lithetsedwe. Malinga ndi kunena kwa The Atlas of Endangered Species, masinthidwe ameneŵa “ngaakulu kwambiri kwakuti ndi maboma okha omwe akhoza kuwachita.” Ndiyeno ikulangiza kuti: “Kumene maboma amakhalako mwa masankho, lili thayo la munthu aliyense kutsimikizira kuti podzafika chaka cha 2000 andale osamala za malo okhala ndiwo okha ayenera kusankhidwa.”

Kodi chimenechi ndi chiyembekezo chotheka? Malinga ndi umboni wa m’mbiri, titha kunena kuti “wina apweteka mnzake pomlamulira”—ndi nyama zomwe. (Mlaliki 8:9) Inde, ambiri otetezera chilengedwe amakhulupirira kuti zomera ndi nyama za dziko lapansi ndizo zimasonyeza mkhalidwe wa malo okhala. Zimenezi zitakhala pangozi, ifenso anthu timakhala pangozi. Koma imeneyi si nthaŵi yoyamba m’mbiri ya munthu kuti zamoyo zonse padziko lapansi zikhale pangozi ya kusoloka.

Buku la mbiri lakale koposa onse lili ndi mawu awa: “Ine ndidzadzetsa chigumula cha madzi padziko lapansi, kuti chiwononge zamoyo zonse, mmene muli mpweya wa moyo pansi pa thambo; zinthu zonse za m’dziko lapansi zidzafa.” (Genesis 6:17) Ngakhale zinali tero, si munthu aliyense kapena chamoyo china chilichonse chimene chinafa, pakuti Mulungu anakonza njira yopulumukira.

Chingalaŵa Chopulumukira

Asayansi amakhulupirira kuti njira yabwino koposa yothetsera vuto la nyama zokhala pangozi lerolino limaphatikizapo kusunga malo awo okhala. Chokondweretsa nchakuti New Scientist ikusimba za zimenezi ndipo ikutchula kugwiritsira ntchito kwa otetezera nyama “phiphiritso la Chingalaŵa cha Nowa.” Chingalaŵa cha Nowa ndicho chinali njira imene anthu ndi nyama anapulumukira Chigumula cha m’tsiku la Nowa.

Mulungu anapatsa Nowa mapulani a chingalaŵa, chibokosi chachikulu cha matabwa, chimene chinayenera kuyandama pamwamba pa madzi osefukira. Chimenechi chinasunga moyo wa Nowa, mkazi wake, ana awo atatu ndi azikazi awo, pamodzi ndi nyama zamitundumitundu, zakuthengo ndi zoŵeta zomwe—inde, ‘zamoyo zonse, mmene munali mpweya wa moyo.’ (Genesis 7:15) Kuchuluka kwa mitundu ya zamoyo zimene zilipo lerolino kumasonyeza mmene chingalaŵacho chinakwaniritsira chifuno chake bwino lomwe.

Komabe, onani kuti kupulumuka sikunadalire chabe pa kuyesayesa kwa munthu. Nowa ndi banja lake anayenera kumvera Mulungu, amene anali ndi mphamvu ya kuwasunga amoyo. Mulungu ndiye anathetsa kulimbana, chiwawa, ndi umbombo wa zimene zinali m’dziko la Chigumula chisanakhale.—2 Petro 3:5, 6.

Nyama m’Dziko Latsopano

Yehova Mulungu walonjeza kuti kumvera malamulo ake kungasinthe anthu kukhala onga nyama zofatsa ndi zodekha m’malo mwa kukhala ngati nyama zolusa zakuthengo. (Yesaya 11:6-9; 65:25) Ngakhale tsopano, umboni wa zimenezi ngwochuluka. Pitani kumsonkhano pa Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova pafupi ndi kwanu, ndipo mudzadzionera nokha. Ngati Yehova angachititse masinthidwe aakulu chonchi pakati pa anthu, kodi sangalinganizenso kuti nyama zizikhala pamodzi mu mtendere ndi chisungiko, ngakhale ngati zimenezi zingafune kusintha mikhalidwe yawo ya lero? Kwenikweni, iye akulonjeza kuti: “Tsiku lomwelo ndidzawachitira pangano ndi nyama za kuthengo, ndi mbalame za mlengalenga, ndi zokwawa pansi; . . . ndi kuwagonetsa pansi mosatekeseka.”—Hoseya 2:18.

Mtumwi Petro analemba za “tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza” la mtsogolo. (2 Petro 3:7) Kuloŵererapo kwa Mulungu kolamulirika kudzangowononga anthu osapembedza. Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’—Chivumbulutso 11:18.

Tangolingalirani kusangalatsa kwake kwa kukhala ndi moyo m’dziko limene zolengedwa sizilinso pangozi. Padzakhala zochuluka chotani nanga zophunzira kwa nyama zakuthengo zimene zidzatizinga! Inde, njuzi, mikango, njovu, zidzadziyendera zokha popanda choziwopsa. Zamoyo za m’madzi zidzachuluka, limodzinso ndi zokwawa, tizilombo, ndi mbalame zamitundumitundu, kuphatikizapo za mtundu wa macaw—zonse zochirikizana bwino. Pokhala ndi anthu omvera obwezeretsedwa ku ungwiro waumunthu mu Ufumu Waumesiya, padzakhala kugwirizana kwangwiro kwa zamoyo ndi malo awo okhala.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena