Nyama Zokhala Pangozi Kukula—Kwa Vutolo
A DODO akhala chizindikiro cha kusoloka. Yomalizira ya mbalame zosauluka zimenezi inafa cha m’ma 1680 pachisumbu cha Mauritius. Mbalame zambiri zimene zili pangozi zimakhalanso pa zisumbu. Pazaka 400 zapitazo, mitundu 85 mwa mitundu 94 ya mbalame zodziŵika kuti zinazimiririka yakhala ya mbalame za pa zisumbu.
Nyama zokhala pa makontinenti aakulu zilinso pangozi ya kusoloka. Talingalirani njuzi zimene kale zinali kumangodziyendera m’Russia yense. Tsopano kuli mtundu wa Amur ku Siberia, ndipo chiŵerengero chake chatsika kufika pafupifupi 180 mpaka 200. Malipoti amati chiŵerengero cha njuzi za kummwera kwa China chimachokera pa 30 mpaka 80 basi. Ku Indochina nyama zimenezi zidzasoloka “pazaka khumi,” ikutero The Times ya London. Momwemonso, ku India, mudzi wa njuzi zigawo ziŵiri mwa zitatu zapadziko lonse, akatswiri akulingalira kuti zolengedwa zazikulu zokongola zimenezi zingasoloke pazaka khumi.
Zipembere ndi akakwiyo akucheperachepera. Ku China ma panda aakuluwo amayenda m’magulu aang’ono kwambiri okhala ndi nyama khumi. Ma pine marten ali pafupi kusoloka ku Wales, ndipo agologolo ofiira “angazimiririke m’England ndi Wales pazaka khumi kufikira 20 zilinkudza,” ikutero The Times. Kudutsa nyanja ya Atlantic kufika ku United States, mileme ndiyo ili pangozi koposa pa nyama za pamtunda.
Zinthu m’nyanja za dziko sizili bwino konse. The Atlas of Endangered Species ikunena za nkhasi za m’nyanja kuti “mwinamwake ndizo gulu lokhala pangozi kowopsa” pa zolengedwa za m’nyanja. Nyama za m’madzi ndi kumtunda zikuoneka kuti zilipo bwino; komabe, malinga ndi magazini a New Scientist, mitundu 89 ya nyama za m’madzi ndi kumtunda yakhala “pangozi ya kusoloka” pazaka 25 zapitazo. Pafupifupi 11 peresenti ya mitundu ya mbalame za padziko lonse ilinso pangozi ya kusoloka.a
Koma bwanji ponena za zolengedwa zazing’ono, monga agulugufe? Zinthu zili zofanana. Oposa chigawo chimodzi mwa anayi a mitundu 400 ya agulugufe a ku Ulaya ali pangozi—mitundu 19 ili pangozi ya kusoloka posachedwapa. Gulugufe wamkulu wa ku Britain wotchedwa tortoiseshell mu 1993 analondola dodo pamzera wa zosoloka.
Nkhaŵa Yomakula
Kodi ndi mitundu ingati ya zolengedwa imene imasoloka chaka chilichonse? Yankho limadalira pa katswiri amene mwafunsa. Ngakhale kuti asayansi samavomerezana, onse akuzindikira kuti nyama zambiri zili pangozi ya kusoloka. Katswiri wa zamoyo ndi malo awo Stuart Pimm akuti: “Mkangano wonena za liŵiro limene tikutayirapo [nyama] kwenikweni ili nkhani yokhudza mtsogolo mwathu.” Akuwonjezera kuti: “Pazaka mazana ambiri zapitazo, tafulumiza liŵiro la kusoloka kwa nyama kuposa liŵiro la chibadwa. Chotero mtsogolo mwathu mwakhala mopanda pake.”
Pulaneti lathu, Dziko Lapansi, lili ngati nyumba. Anthu ena amene amasamala za nyama zokhala pangozi amaphunzira ecology, liwu lopangidwa chakumapeto kwa zaka za zana la 19 kuchokera ku liwu lachigiriki oiʹkos, “nyumba.” Maphunziro ameneŵa amafotokoza kwambiri za kugwirizana kwa zamoyo ndi malo awo okhala. Zaka za zana la 19 zinaona chidwi chomakula cha kutetezera nyama, chimene mosakayikira chinakula chifukwa cha malipoti onena za kusoloka kwa nyama zina. Ku United States, zimenezi zinachititsa nkhalango zosungira nyama kukhazikitsidwa ndi malo otetezereka osungira zolengedwa. Lero, pali malo pafupifupi 8,000 odziŵika padziko lonse otetezera nyama zakuthengo. Limodzi ndi malo enanso 40,000 othandiza kusamalira nkhalango, iwo amapanga pafupifupi 10 peresenti ya nthaka ya dziko lonse.
Anthu ambiri odera nkhaŵa tsopano akuchirikiza nkhani za malo okhala, kaya kupyolera m’magulu amene amalalikira za ngozi ya kusoloka kapena amene amangophunzitsa anthu za kudalirana kwa zamoyo. Ndipo kuyambira pamsonkhano wa Rio Earth Summit mu 1992, maboma ambiri adziŵa kwambiri za nkhani zokhudza malo okhala.
Vuto la nyama zokhala pangozi lili padziko lonse ndipo likukula. Koma kodi nchifukwa ninji? Kodi pali njira zilizonse zoyesa kuletsa kusoloka kwa nyama zimene zapambana? Ndipo bwanji za mtsogolo? Kodi inu mukukhudzidwa motani? Nkhani zathu zotsatira zidzapereka mayankho.
[Mawu a M’munsi]
a Nyama yosoloka amati ndi ija imene yakhala yosapezeka m’nkhalango kwa zaka 50, pamene nyama zokhala pangozi ndi zija zimene zili pangozi ya kusoloka ngati mikhalidwe yawo siikusintha.