Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g01 12/8 tsamba 19
  • Anthu Akupulula Zinthu Zachilengedwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anthu Akupulula Zinthu Zachilengedwe
  • Galamukani!—2001
  • Nkhani Yofanana
  • Zachilengedwe Zimadalirana M’njira Zovuta Kuzimvetsa
    Galamukani!—2001
  • Nyama Zokhala Pangozi Kukula—Kwa Vutolo
    Galamukani!—1996
  • Nyama za Kuthengo Zimene Zikuzimiririka Padziko Lapansi
    Galamukani!—1997
  • Kutetezera Nyama Kulimbana ndi Kuzisolotsa
    Galamukani!—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—2001
g01 12/8 tsamba 19

Anthu Akupulula Zinthu Zachilengedwe

“Masiku ano anthu ayenera kuvomereza kuti ndiwo akuwononga kwambiri mitundu yosiyanasiyana ya zinthu zachilengedwe.” JANE GOODALL, KATSWIRI WOONA NDI KUTETEZA ZINTHU ZACHILENGEDWE ANATERO.

ZAMOYO padziko lapansi zimachita ntchito zochuluka zedi ndipo zimadalirana. Nafenso anthu tili m’gulu la zinthu zamoyo. Timadalira zinthu zamoyo zimene zili m’dzikoli kuti tipeze chakudya ndi mankhwala, mpweya umene timapuma ndiponso zinthu zimene zimapanga thupi lathuli. Pakutha pa tsiku lililonse, anthu onse amene ali padziko pano amagwiritsa ntchito mitundu ya zinthu zamoyo yoposa 40,000. Mitundu yonse ya zinthu zachilengedwe padziko lapansi imadalirana m’njira zosiyanasiyana zovuta kufotokoza.

Komabe akatswiri ambiri amene amaphunzira za kuchuluka kwa mitunduyi akuti zinthu zachilengedwezi zikupululidwa. N’kutheka kuti munamvapo zakuti nyama zinazake monga zipembere, akambuku ndiponso nsomba zazikulu kwambiri za m’nyanja zayamba kusoŵa. Asayansi ena akuti pakutha pa zaka 75, theka la mitundu ya zomera ndiponso zinyama zonse lidzakhala litatha. Ofufuza akuda nkhaŵa kuti mwina mitundu ina ya zinthu zachilengedwe ikhoza kutha mofulumira kwambiri poyerekezera ndi mmene imathera mwachibadwa malingana ndi mmene asayansi amanenera. Katswiri wina anati pa mphindi 10 kapena 20 zilizonse mtundu winawake wa zachilengedwe umatheratu.

Asayansi akukhulupirira kuti kale kwambiri, mitundu ya zinthu zamoyozi inkatha makamaka chifukwa cha zinthu zina zochitika m’chilengedwe. Koma akuti masiku ano chinthu chachikulu chimene chikuchititsa vutoli si zimenezonso ayi. N’zosachita kufunsa kuti masiku ano zochita za anthu ndizo zikupulula mitundu ya zinthu zachilengedwe. Wasayansi wina anati anthu ndiwo ‘akupulula mitundu ya zinthu zachilengedwe.’

Kodi zochita za anthu n’zimenedi zikuchepetsa kwambiri mitundu ya zinthu zachilengedwe? Ngati ndi choncho, zikuchitika bwanji? Kodi tingakhale ndi moyo ngati dzikoli litakhala lopanda zinthu zochititsa chidwi zosiyanasiyana zachilengedwe? Kodi anthu achitapo chilichonse kuti aletse vuto la kutha kwa zachilengedwe limene ambiri akuti lakula kwambiri padziko?

[Mawu a Chithunzi patsamba 19]

WHO

NOAA

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena