Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g96 10/8 tsamba 9-11
  • Potsirizira Pake—Boma Limene Lidzathetsa Upandu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Potsirizira Pake—Boma Limene Lidzathetsa Upandu
  • Galamukani!—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Tsoka la Dziko Lonse”
  • Boma Limene Lidzathetsa Upandu
  • Dziko Lopanda Upandu
  • Pamene Kunalibe Upandu
    Galamukani!—1998
  • Nchifukwa Ninji Pali Upandu Wochulukira Chotero?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kuyesayesa Kuthetsa Upandu
    Galamukani!—1996
  • Kulimbana ndi Upandu Kukulephereka
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1996
g96 10/8 tsamba 9-11

Potsirizira Pake—Boma Limene Lidzathetsa Upandu

BAIBULO linalosera kuti m’tsiku lathu anthu adzakhala “odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino.” (2 Timoteo 3:2, 3) Anthu otero amachita upandu.

Popeza kuti anthu ndiwo amachita upandu, ngati iwo asintha kukhala abwino, upandunso umachepa. Komatu sikunakhalepo kwapafupi kwa anthu kusintha kukhala abwino. Lerolino nkovuta koposa ndi kale lonse, pakuti kuyambira 1914, deti loikika mwa kuŵerengera zaka za m’Baibulo, takhala mu “masiku otsiriza” a dongosolo ili la zinthu. Malinga ndi ulosi wa Baibulo, nyengo imeneyi ili ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa.” Nthaŵi zoŵaŵitsa zimenezi zimadzetsedwa ndi Satana Mdyerekezi, mpandu wamkulu koposa onse, “wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.”—2 Timoteo 3:1; Chivumbulutso 12:12.

Nchifukwa chake pali kuwonjezereka kwa upandu lerolino. Satana akudziŵa kuti iye ndi dongosolo lake ali pafupi kuwonongedwa. Panthaŵi yaifupi yotsalayo, akufunafuna mwa njira iliyonse yotheka kukulitsa mikhalidwe yoipa mwa anthu yotchulidwa mu 2 Timoteo chaputala 3. Chotero, kuti boma lithetse upandu, liyenera kuchotsa chisonkhezero cha Satana ndiponso kuthandiza anthu kusintha kuti asamachitenso zinthu zotchulidwazo. Koma kodi pali boma limene likhoza kuchita ntchito imeneyi imene munthu sangachite?

Kulibe boma la munthu limene likhoza kuchita zimenezo. J. Vaskovich, mphunzitsi wa zamalamulo ku Ukraine, akunena kuti pakufunikira “bungwe limodzi lokhoza, limene lingagwirizanitse zoyesayesa za maboma onse ndi magulu a anthu.” Ndipo Pulezidenti Fidel Ramos wa ku Philippines anati pamsonkhano wa dziko lonse wonena za upandu: “Popeza kuti kutsungula kwachepetsa dziko lathu, upandu watha kudutsa malire a maiko ndipo wakula kukhala vuto la maiko onse. Choncho njira zouthetsera ziyeneranso kukhala za maiko onse.”

“Tsoka la Dziko Lonse”

United Nations ndi bungwe la maiko onse. Kuchokera pa chiyambi chake, layesetsa kuthetsa upandu. Koma lilibe mayankho mofanana ndi maboma a maikowo. Buku lakuti The United Nations and Crime Prevention likuti: “Maiko alandidwa mphamvu ndi upandu wake ndipo upandu wa maiko onse wawonjezereka kwambiri moti bungwe la maiko onse silingauthetse. . . . Upandu wa timagulu ta apandu tolinganizidwa wakula kowopsa, ukumakhala ndi zotulukapo zoipa kwambiri monga chiwawa pa anthu, kuwopsa akuluakulu a boma ndi kuwapatsa ziphuphu. Uchigaŵenga waphetsa anthu osalakwa zikwi makumi ambiri. Malonda adyera a anamgoneka omwerekeretsa akhala tsoka la dziko lonse.”

James Madison, pulezidenti wachinayi wa United States, anati panthaŵi ina: “Pokonza boma limene anthu adzalamulira nalo anthu anzawo, vuto lalikulu limakhala lakuti: choyamba muyenera kulola boma kulamulira olamuliridwa; ndiyeno kulikakamiza kudzilamulira lokha.” (Yerekezerani ndi Mlaliki 8:9.) Chotero njira yabwino ingakhale kuchotsa maboma ‘amene anthu amalamulira nawo anthu anzawo’ ndi kuikapo njira imene Mulungu angalamulire nayo. Koma kodi njira imeneyo njotheka?

Boma Limene Lidzathetsa Upandu

Akristu oona amakhulupirira zimene Baibulo limanena pa Ufumu wa Mulungu.a Ndiwo boma lenileni. Ngakhale kuti Ufumuwo ngwosaoneka chifukwa chakuti uli kumwamba, zochita zake padziko lapansi zimaoneka. (Mateyu 6:9, 10) Wapangidwa ndi Kristu Yesu ndi anthu 144,000 ‘a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse . . . kuchita ufumu padziko.’ Boma lamphamvu limeneli lidzalamulira “khamu lalikulu” la nzika limenenso, malinga ndi ulosi wa Baibulo, likuchokera ‘mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.’ (Chivumbulutso 5:9, 10; 7:9) Chotero, olamulira ndi olamuliridwa omwe achokera m’mitundu yonse, anthu ogwirizanadi a mafuko onse, okhala ndi chiyanjo cha Mulungu.

Pokhala zitalandira ulamuliro wa Mulungu, Mboni za Yehova zagonjetsa pamlingo waukulu vuto la upandu pakati pawo. Motani? Mwa kuphunzira kuzindikira nzeru ya mapulinsipulo a Baibulo, mwa kuwagwiritsira ntchito m’moyo wawo, ndi mwa kulola mphamvu yaikulu koposa m’chilengedwe, mzimu wa Mulungu, ndi chipatso chake—chikondi, kuwasonkhezera. Mawu a Mulungu amati: “Khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.” (Akolose 3:14) M’maiko oposa 230, Mboni za Yehova zimasonyeza chikondi chimenechi ndi umodzi, zikumasonyeza mmene Ufumu wa Mulungu wayambira kale kuchitapo kanthu kuthetsa upandu.

Zimenezi zingasonyezedwe ndi zotulukapo za kufufuza kwa mu 1994 kumene Mboni za Yehova zokwanira 145,958 zinatengamo mbali ku Germany. Ambiri a iwo anavomera kuti anagonjetsa zofooka zazikulu kuti akhale Mboni. Chimene chinawasonkhezera kuchita zimenezo ndi phunziro lawo la Baibulo. Mwachitsanzo, 30,060 anagonjetsa kumwerekera kwawo ndi fodya kapena anamgoneka; 1,437 anasiya juga; 4,362 anawongolera khalidwe lawo lachiwawa kapena laupandu; 11,149 anagonjetsa mikhalidwe yonga nsanje kapena chidani; ndipo 12,820 anakhazikitsanso mtendere m’mabanja awo osamvana.

Ngakhale kuti zimenezi zinapezeka kwa Mboni za Yehova za m’dziko limodzi lokha, ndiwo mkhalidwe wa Mboni padziko lonse. Mwachitsanzo, talingalirani Myukreniya wachichepere wotchedwa Yuri. Pamene anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anali wopisa anthu m’matumba. Anali atapita ngakhale ku Moscow kumene anadziŵa kuti makamu a anthu adzampeputsira “ntchito” yakeyo.

Mu 1993, Yuri analinso ku Moscow, pakati pa makamu a anthu. Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa anthu oposa 23,000 amene anali m’Locomotive Stadium pa Lachisanu, July 23, amene anamuwopa, pakuti tsopano anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Inde, Yuri anali pa pulatifomu m’programu imene inali kuperekedwa kwa omvetsera a m’mitundu yonse. Popeza anasintha kukhala wabwino, amamvera lamulo la Baibulo lakuti: “Wakubayo asabenso.”—Aefeso 4:28.

Enanso ambiri onga Yuri asiya moyo waupandu kuti ayenerere moyo m’dziko latsopano lolungama la Mulungu. Zimenezi zikugogomezera choonadi cha mawu a Bwana Peter Imbert, amene kale anali mkulu wapolisi wachibritishi, akuti: “Upandu ungathetsedwe mosavuta ngati aliyense anali wokonzekera kuyesetsa.” Programu ya maphunziro a Baibulo yoperekedwa ndi boma la Mulungu imapatsa anthu oona mtima mphamvu yofunika yochitira “kuyesetsa” kumeneko.

Dziko Lopanda Upandu

Upandu wa mtundu uliwonse umasonyeza kusakonda ena. Akristu amatsatira chitsanzo cha Yesu, amene anati: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” Ndipo, “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini.”—Mateyu 22:37-39.

Boma lokha lodzipereka pa kuthetsa upandu mwa kuphunzitsa anthu kumvera malamulo aakulu aŵiri ameneŵa ndilo Ufumu wa Mulungu. Lerolino, Mboni za Yehova zoposa mamiliyoni asanu zikupindula ndi malangizo ameneŵa. Zili zotsimikiza kusalola mikhalidwe yaupandu kuzika mizu m’mitima yawo, pokhala zokonzekera aliyense payekha kuchita zilizonse zofunikira kuti zichirikize dziko lopanda upandu. Zimene Mulungu wachita m’moyo wawo zangokhala kulaŵa chabe zimene adzachita m’dziko lake latsopano lolamuliridwa ndi boma lake lakumwamba. Tayerekezerani dziko losafunikira apolisi, oweruza, maloya, kapena ndende!

Kuchita zimenezi padziko lonse kudzafuna kusintha kwa boma kwakukulu koposa m’mbiri, kumene Mulungu mwini adzachita. Danieli 2:44 amati: “Masiku a mafumu aja [okhalapo lerolino] Mulungu wakumwamba adzaika ufumu [wakumwamba] woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.” Posachedwapa Mulungu adzaphwanyanso Satana, akumathetsa chisonkhezero chake choipa.—Aroma 16:20.

Maboma aumunthu ataloŵedwa m’malo ndi boma lakumwamba la Mulungu, anthu sadzalamulirananso. Mafumu akumwamba—mafumu oposa ngakhale angelo omwe—adzaphunzitsa anthu njira zachilungamo. Ndiyeno, sikudzakhalanso kuphedwa ndi mfuti, gasi ya poizoni, kapena mabomba a zigaŵenga! M’chitaganya simudzakhalanso chisalungamo chimene chimasonkhezera upandu! Sikudzakhalanso osauka ndi olemera!

Profesa S. A. Aluko, wa pa Obafemi Awolowo University ku Nigeria, anati: “Osauka saona tulo usiku chifukwa amakhala ndi njala; olemera saona tulo chifukwa osauka amakhala maso.” Koma posachedwapa aliyense adzakhoza kugona tulo tabwino podziŵa kuti boma—boma la Mulungu—lathetsa upandu potsirizira pake!

[Mawu a M’munsi]

a Ngati mufuna mafotokozedwe atsatanetsatane a chimene Ufumu wa Mulungu uli ndi mmene udzapindulitsira anthu okhulupirira, chonde ŵerengani buku la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Chithunzi patsamba 10]

Yemwe kale anali mbala ndi amene anamubera, tsopano ali ogwirizana monga abale achikristu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena