Bwenzi Lathu Lapamtima Lili m’Malo a Mizimu
BAIBULO limatipatsa chithunzi chabwino cha aja amene amakhala m’malo a mizimu. Yehova Mulungu ndiye wapamwambamwamba kumwamba. Yesu Kristu ndiye wachiŵiri kwa Yehova mu mphamvu ndi mu ulamuliro. Angelo okhulupirika kwa Mulungu amatumikira monga atumiki kwa Mulungu ndiponso kwa anthu ake padziko lapansi. Satana ndi ziŵanda zake amatsutsa Mulungu ndi kusokeretsa anthu. Akufa ali m’tulo ta imfa kufikira Mulungu atawaukitsa.
Ziŵanda Zimafuna Kuti Tizizilambira
Popeza kuti akufa alibe moyo, sitingapindule kalikonse mwa kuwalambira. Kupereka nsembe kwa akufa kumangochirikiza mabodza a Satana ndi ziŵanda.
Kodi angelo a Mulungu amafuna kuti tiziwalambira? Kutalitali! Angelo okhulupirika amalemekeza Mulungu ndi kulimbikitsa anthu kuchita mofananamo. Mtumwi Yohane anayesa kaŵiri kulambira angelo, koma iwo anamdzudzula, akumati: “Tapenya, usatero; . . . Lambira Mulungu.”—Chivumbulutso 19:10; 22:8, 9.
Satana ndi ziŵanda zake, mosiyana ndi angelo okhulupirika, amafuna kuti azilambiridwa ndi kulemekezedwa komwe. Zimenezi zinaoneka pamene Satana anayesa Yesu pamene Yesuyo anali munthu pano padziko lapansi. Baibulo limasimba kuti: “Mdyerekezi anamuka naye [Yesu] ku phiri lalitali, namuonetsa maiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo; nati kwa Iye, Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine.”—Mateyu 4:8, 9.
Yesu anayankha kuti: “Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.” (Mateyu 4:10) Yesu anadziŵa Chilamulo cha Yehova, ndipo anakana kuchiswa.—Deuteronomo 6:13.
Ngakhale kuti Satana sanakhoze kuchititsa Yesu kumlambira, iye wakhoza kutero pa ena. Zoonadi, anthu ochepa amalambira Satana mwadala. Chikhalirechobe, mwa njira yaukathyali, yachinyengo, ndi yamabodza, ndi yowopseza, Satana ndi ziŵanda zake wachotsa anthu ambiri pa kulambira Yehova koyera kwakuti mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Awo amene amalambira mosiyana ndi Mawu a Mulungu amalemekeza Satana, osati Yehova. Baibulo limachenjeza kuti: “Zinthu zimene amitundu apereka nsembe amazipereka kwa ziŵanda, ndipo osati kwa Mulungu.”—1 Akorinto 10:20, NW.
Kulambira ndi kwa Yehova
Kulambira kwathu kuyenera kulunjikitsidwa kwa Mulungu yekha. Yehova anauza Mose kuti: “Usakhale nayo milungu ina koma Ine ndekha. Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje.”—Eksodo 20:3-5.
Ngakhale kuti Yehova ali ndi ulemerero wochititsa mantha, iye ngwofikirika. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu.” (Yakobo 4:8) Mtumwi Paulo anati: “[Mulungu] sakhala patali ndi yense wa ife.” (Machitidwe 17:27) Ndipo mtumwi Yohane analemba kuti: “Uku ndi kulimbika mtima kumene tili nako kwa [Yehova], kuti ngati tipempha kanthu monga mwa chifuniro chake, atimvera; ndipo ngati tidziŵa kuti atimvera chilichonse tichipempha, tidziŵa kuti tili nazo izi tazipempha kwa Iye.”—1 Yohane 5:14, 15.
Onani kuti Yohane analemba kuti Yehova adzayankha mapempho athu ngati tipempha “monga mwa chifuniro chake.” Kuti tidziŵe chifuniro cha Mulungu, tiyenera kuphunzira zimene Baibulo limaphunzitsa. Mboni za Yehova zikufuna kukuthandizani kumvetsa Baibulo.
Pamene muphunzira zambiri ponena za Yehova, mudzapeza chidziŵitso chambiri cha aja amene amakhala kumalo a mizimu. Chidziŵitso chimenechi chimadzetsa chimasuko ku zamizimu, zikhulupiriro, ndi miyambo imene Satana amagwiritsira ntchito kuchititsa anthu kukhala amantha ndi akapolo. Kupyolera m’chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu, mudzadziŵa kukhulupirira mwa iye kuti akuthandizeni kupeŵa kapena kugonjetsa mavuto a moyo atsiku ndi tsiku. Mungakhale bwenzi la Mulungu. Ndipo Mulungu adzakhala kwa inu “pothaŵirapo . . . ndi mphamvu, . . . thandizo lopezekeratu m’masautso.”—Salmo 46:1.
Magulu Oipa Adzachotsedwa
Musakayikire konse kuti magulu amizimu yabwino adzagonjetsa magulu amizimu yoipa. Nkhondo yamenyedwa kale kumalo a mizimu imene yayeretsa miyamba mwa kuchotsa Satana ndi mabwenzi ake oipa. Buku la Chivumbulutso limati: “Munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli [Yesu Kristu woukitsidwayo] ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka, chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.”—Chivumbulutso 12:7-9.
Kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo chake pa nkhondoyo? Lipotilo limapitiriza kuti: “Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:12) Aja amene ali kumwamba anakondwera, pakuti Satana ndi ziŵanda zake sanalinso kumeneko kuti azivutitsa. Komabe, kuponyedwa kwake kuchokera kumwamba kwabweretsa tsoka lalikulu, mavuto aakulu, kwa okhala padziko lapansi. Tikukhala mu nthaŵi imeneyo ya tsoka tsopano.—2 Timoteo 3:1-5.
Mtsogolo Mopanda Kuipa
Komabe, Baibulo limaperekanso chiyembekezo. Limatitsimikizira kuti Mdyerekezi watsala ndi “kanthaŵi” kuti alandidwe mphamvu. Pamene zimenezo zichitika, Yehova adzabweretsa madalitso okondweretsa kwa onse okhala padziko lapansi amene akufuna kuchita naye ubwenzi. Lingalirani za malonjezo ake angapo amtsogolo:
“M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.”—Salmo 72:16.
“Osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo. Iwo sadzagwira ntchito mwachabe.”—Yesaya 65:22, 23.
“Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.
“Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzaimba.”—Yesaya 35:5, 6.
“Ndipo [Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.
“Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
Yehova yekha, Mulungu woona, angakwaniritse malonjezo aakulu amenewo. Palibe chimene chingamletse kukwaniritsa chifuno chake. “Palibe mawu amodzi akuchokera kwa Mulungu adzakhala opanda mphamvu.”—Luka 1:37.
[Zithunzi patsamba 9]
Mutakhala bwenzi la Mulungu, iyeyo adzakuthandizani kulimbana ndi mavuto a moyo