Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 2/8 tsamba 31
  • Umphaŵi ‘Ngozi Yamseri’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Umphaŵi ‘Ngozi Yamseri’
  • Galamukani!—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Akapolo a Umphaŵi
    Galamukani!—1998
  • Zimene Ena Achita Pofuna Kuthetsa Umphawi
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Mapeto a Umphaŵi Ayandikira
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 2/8 tsamba 31

Umphaŵi ‘Ngozi Yamseri’

“TIMAMVA zambiri ponena za ngozi zoopsa za kutentha kwa dziko lapansi ndi miyalo ya ozoni ndi kuipitsa nyanja,” anatero phungu wa United Nations Dr. Mahbub Ul-Haq, koma anawonjezera kuti: “Kutentha kwa dziko lapansi ndi ngozi zina zoopsa zidzapha aliyense mtsogolo [pamene kuli kwakuti] ngozi zamseri zikuwononga miyoyo yambiri m’maiko osauka tsiku lililonse.” Dr. Ul-Haq anachitira ndemanga pa imodzi ya ngozi zamseri zimenezo. Anatero kuti: “umphaŵi ndiwo wakupha kopambana.” Motani?

Kwa ochuluka mwa anthu [1,300,000,000] padziko lonse amene patsiku lililonse amalandira dola imodzi kapena kucheperapo, umphaŵi ulidi ngozi yakupha. Magazini a UN Chronicle analengeza kuti chaka chilichonse anthu mamiliyoni 18 amafa “chifukwa cha umphaŵi.” Ndiye nchiŵerengero chachikulutu! Talingalirani mitu yankhani yoopsayo, mwachitsanzo, ngati anthu onse a mu Australia okwanira mamiliyoni 18 akanafa ndi njala m’chaka chimodzi! Komabe, UN Radio inati imfa zimenezi za mamiliyoni a anthu osaukawo “sizimatchulidwatchulidwa.” Limeneli ndilodi ‘tsoka lamseri.’

Kuti ayambe kulitchula vutolo, oimira a maiko 117 opezeka pa Msonkhano Wadziko woyamba wa Chitukuko cha Makhalidwe a Anthu ananena za njira zothetsera vuto la umphaŵi wadziko umenewu. “Zaka zana limodzi ndi makumi asanu zapitazo dziko linayambitsa njira zothetsera ukapolo,” anawakumbutsa choncho James Gustave Speth, mkulu wa United Nations Development Programme. “Lero tiyenera kuyambitsa njira zothetsera umphaŵi wa onse.” Kuderanji nkhawa? Anachenjeza kuti, umphaŵi “ukuwonjezera kupsinjika mtima ndi kusautsika maganizo ndipo ukuvutitsa dziko lathu.”

Komabe, ngakhale pamene nthumwizo zinali kumakambitsirana za njira zothetsera umphaŵi, ‘koloko ya umphaŵi,’ yosonyeza chiŵerengero cha ana obadwira m’mabanja osauka tsiku lililonse inasonyeza kuti mkhalidwe waumphaŵi wadziko lonse unali kuipiraipira. Kolokoyo, yoonetsedwa kumalo amsonkhanowo, inasonyeza kuti mkati mwa msonkhano wa mlungu umodziwo, makanda ongobadwa kumene pafupifupi 600,000 anawonjezeredwa pamzera wautali kale wa amphaŵi. Kumapeto kwa tsiku lotsiriza la msonkhanowo, kolokoyo inaimikidwa; koma, kwenikweni, monga mmene Speth ananenera, “kolokoyo ikuyendabe.” Tsopano funso nlakuti: Kodi vutolo lidzasamalidwa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena