Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 3/8 tsamba 22-24
  • Kodi Ndingakhale Bwenzi la Mulungu Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingakhale Bwenzi la Mulungu Motani?
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kumdziŵadi Bwino Mulungu
  • Mayendedwe Abwino Ngofunika
  • Funafunani Mabwenzi Abwino
  • Yehova Akhoza Kukhala Mnzanu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Yehova—Kodi Ndimnansi Wanu Kapena Bwenzi Lanu?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Kukhala Bwenzi la Mulungu Kudzandithandiza?
    Galamukani!—1995
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yokhala Ndi Anzathu?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 3/8 tsamba 22-24

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingakhale Bwenzi la Mulungu Motani?

“KUKHULUPIRIKA.” “Kumkonda munthu.” Ameneŵa ndiwo mawu omwe anthu amagwiritsira ntchito kaŵirikaŵiri pofotokoza unansi wawo ndi mabwenzi awo apamtima. Kodi mukudziŵa kuti mawu ameneŵa angafotokozenso unansi wa munthu ndi Mlengi Wamkulu wa chilengedwe chonse choopsachi—kuti Mulungu mwiniyo angakhale bwenzi lanulanu? Inde, Baibulo limanena za kudzipereka kwaumulungu, ndipo liwulo silimangotanthauza kumvera chabe, komanso kumkondadi Mulungu, unansi umene umachokera mumtima woyamikira.

Nkhani za mmbuyomu zampambo womwe uno zinasonyeza kuti unansi woterowo ngwotheka ndipo ngwopindulitsa.a Koma ndiye ubwenzi umenewu ndi Mulungu mungakhale nawo motani? Si kanthu kena kamene munangobadwa nako kapena kamene munangolandira monga choloŵa kwa makolo opembedza. M’malo mwake, ndi kanthu kena komwe kamakhalapo mwa kuyesayesa kwenikweni. Mtumwi Paulo anauza Timoteo wachinyamata kuti ‘adziphunzitse nakhale ndi kudzipereka kwaumulungu monga chonulirapo chake,’ Inde, anayenera kuyesayesa mwa njira imene wothamanga liŵiro amachitira poyeseza! (1 Timoteo 4:7, 8, 10, NW) Muyenera kuchita zofananazo ngati mukufuna Mulungu kukhala bwenzi lanu. Koma kodi mungayambe motani kuphunzira kumeneku?

Kumdziŵadi Bwino Mulungu

Popeza kuti kudzipereka kwaumulungu kumachokera mumtima, muyenera kudzaza mtima wanuwo ndi chidziŵitso cha Mulungu. Momvetsa chisoni, pamene achichepere oposa 500 anafunsidwa kuti “Kodi mumaŵerenga Baibulo kangati ngati muli nokha?” Achichepere okwanira 87 peresenti anati “kamodzikamodzi,” “patalipatali” kapena “mpang’ono pomwe.” Achichepere ambiri mwachionekere amaganiza kuti kuŵerenga Baibulo nkosakondweretsa ndipo kumagwetsa ulesi. Koma sikuyenera kukhala kotero! Talingalirani: Kodi achichepere ena amaloŵezeranji malipoti a zamaseŵera kapena kuphunzira mawu a nyimbo zawo zapamtima? Chifukwa zinthu zimenezo zimawasangalatsa. Mofananamo, kuphunzira Baibulo kumakhala kosangalatsa ngati mumatengeka nalo. (1 Timoteo 4:15) Mtumwi Petro analangiza kuti: “Kulitsani chilakolako cha mkaka wosasukuluka wa mawu.” (1 Petro 2:2, NW) Inde, muyenera kuchita chidwi mofananamo ndi Malemba. Zimenezi zimafuna khama, koma zili ndi mapindu ake.b

Makamaka chinthu china, kuŵerenga ndi kuphunzira Mawu a Mulungu ndi zofalitsa zozikidwa pa Baibulo kudzavumbula “kukongola kwake kwa Yehova.” (Salmo 27:4) Mkristu wina wachichepere wotchedwa Amber anatsimikiza kuliŵerenga Baibulo lonse. Kunamtengera pafupifupi chaka. “Sindidziŵa kuti padzakhalanso zinthu zambiri m’moyo wanga zimene zimafuna nthaŵi ndi kuyesayesa koteroko koma zimene zimapindulitsa kwambiri,” anafotokoza choncho Amber. “Mmene ndimaliŵerenga, kunali ngati kuti Yehova wandikhazika pamiyendo yake monga atate ndi kumandiphunzitsa. Ndinaphunzira zochuluka ponena za Yehova—zinthu zimene zinandiyandikiza kwa iye ndi kundisonkhezera kumuopa kwa moyo wanga wonse.”

Pamene muŵerenga Baibulo, mumaphunzira zochitika zambiri pamene Mulungu mokhulupirika anachirikiza mabwenzi ake. (Salmo 18:25; 27:10) Mudzapeza kuti miyezo yake nthaŵi zonse njabwino ndipo njotithandiza kosatha. (Yesaya 48:17) Kuŵerenga za mikhalidwe yosayerekezereka ya Mulungu, yonga chikondi ndi nzeru yake, kumakusonkhezerani kumtsanzira. (Aefeso 5:1) Koma kuti chidziŵitso chimenecho chikukhudzeni mtima, muyeneranso kusinkhasinkha. Pamene mukuŵerenga, dzifunseni kuti: ‘Kodi zimenezi zikundiuza chiyani ponena za Yehova? Kodi ndingazigwiritsire ntchito motani pakaganizidwe ndi zochita zanga? Kodi zimenezi zikusonyeza motani kuti kulibe bwenzi lina lapamtima limene ndingakhale nalo koposa Mulungu?’

Chidziŵitso chimene mumapeza ponena za Mulungu kupyolera m’phunziro laumwini ndi la mpingo chidzakuthandizani kuyandikana naye kwambiri mwanjira inanso. Mwambi wachifalansa umati: “Mabwenzi oona ndi amene amaganiza mofanana.” Koma kodi mungachite motani kuti “muganize mofanana” ndi Mulungu? Denise wachichepere akufotokoza kuti: “Pamene mukuphunzira ndi kufufuza nkhani kwambiri, mpamenenso mumadziŵa kwambiri lingaliro la Yehova pankhaniyo. Zimathandiza ngati mwadziŵa mmene amaonera zinthu zina.”

Mayendedwe Abwino Ngofunika

Mulungu amasankha kokha aja amene amalemekeza miyezo yake ya makhalidwe kuti akhale mabwenzi ake. “Iye ndi bwenzi la oongoka,” ikutero Miyambo 3:32, [NW]. Wachichepere yemwe akuyesayesa kukhala woongoka ‘adzasamalira kuyenda m’chilamulo cha Yehova.’ (2 Mafumu 10:31) Kodi khalidwe lomvera loterolo lingamyandikize munthu kwa Mulungu mpaka pati? Yesu Kristu anati: “Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.” (Yohane 14:21-24) Nchithunzi chokondweretsa mtimatu chimenecho! Tangolingalirani, anthu aŵiri aakulu koposa m’chilengedwe chonse akumam’ganizira munthu ndi kumsamala mosalekeza! Zimenezo zingakuchitikireninso ngati musamalira kuyenda m’chilamulo cha Yehova.

Kodi kukhala woongoka kumatanthauza kuti muyenera kukhala wangwiro? Kutalitali! Kuchita cholakwa chifukwa cha kufooka sikumatanthauza kuti mwasiya ‘kuyenda m’malamulo a Mulungu.’ (Salmo 119:35) Talingalirani zimene Baibulo limatiuza ponena za Mfumu Davide. Ngakhale anali bwenzi lokhulupirika la Mulungu, anachita zolakwa zina zazikulu chifukwa cha kufooka. Ngakhale zinali choncho, Yehova anati anayenda ndi “mtima woona ndi wolungama.” (1 Mafumu 9:4) Nthaŵi zonse Mfumu Davide ankalapa moona mtima akachita cholakwa china chilichonse ndipo ankayesetsa kuchita chomkodweretsa Mulungu.—Salmo 51:1-4.

Ngakhale kuti Davide ankakonda Mulungu, anadziŵa mmene nthaŵi zina kunalili kovuta kuchita choyenera. Nchifukwa chake anampempha Mulungu kuti: “Munditsogolere m’choonadi chanu.” Inde, anafikira pakukhala ndi mantha enieni, kapena kuopa kulakwira Mulungu. Chotero Davide anati: “Ubwenzi ndi Yehova ngwa iwo akumuopa iye.” (Salmo 25:5, 14, NW) Ameneŵa si mantha oipa iyayi koma ndiko kulemekeza Mlengi mwakuya ndi kuopa kwabwino kosafuna kumkhumudwitsa. Mantha aumulungu ameneŵa ndiwo pozikapo khalidwe labwino. Mwachitsanzo, talingalirani chitsanzo cha Mkristu wachichepere wotchedwa Joshua.

Joshua analandira kalata kwa mnzake wapasukulu kumuuza kuti anamkonda ndipo anafuna kuti akhale “pachibwenzi.” Ngakhale kuti Joshua anakopedwa naye, anazindikira kuti kuyanjana ndi wosakhulupirira kukanamchititsa chisembwere ndipo kukanawononga unansi wake ndi Yehova. Choncho anamuuza momveka bwino kuti iye sanali kumfuna iyayi! Pambuyo pake pamene anauza mayi wake mmene anachitira ndi nkhaniyo, anadzuma asanaganizire: “O, Joshua, mwinamwaketu wamkhumudwitsa!” Joshua anati: “Koma Mayi. Ndiye ndi bwino kumkhumudwitsa iyeyo koposa Yehova.” Mantha ake aumulungu, kuopa kwake kukhumudwitsa Bwenzi lake lakumwamba, kunamchititsa kusunga mayendedwe abwino.

Funafunani Mabwenzi Abwino

Komabe, wachichepere wina wotchedwa Lynn anali kungoloŵa m’vuto. Vuto lake? Ankayenda ndi anthu oipa. (Eksodo 23:2; 1 Akorinto 15:33) Kulithetsa kwake? Kupeza mabwenzi atsopano! “Ngati uli ndi mabwenzi okonda Yehova,” anatero Lynn, “zimakuthandiza kukhala ndi chikumbumtima chamoyo ndi kupeŵa mavuto. Pamene iwo anyansidwa ndi choipa, umamva mofananamo.”

Kwenikweni, kusankha kwanu mabwenzi oipa ndiko kungadodometse kwambiri ubwenzi wanu ndi Mulungu. Ann wazaka 18 anavomereza kuti: “Mabwenzi amasonkhezera kwambiri. Posakhalitsa umafanana nawo. Amakupangitsa kuganiza ngati iwowo. Zonena zawo zimangokhala zakugonana basi. Zingakuchititse chidwi. Umafuna kudziŵa kuti kodi kumakhala bwanji.” Ann anachenjera atalumwa. Akutero kuti: “Ndikudziŵa kuti nzoona. Ndinachita chisembwere ndi kutenga pakati ndili ndi zaka 15.”

Potsirizira pake Ann anazindikira choonadi cha mawu a Baibulo akuti: “Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4) Inde, Ann anafuna kukhala—anatsimikiza kuti akhale—bwenzi la dziko. Ndiye anaona masoka okhaokha. Mwamwaŵi, Ann analeka chibwana. Anamva chisoni kwambiri ndi zochita zake ndipo anapempha makolo ake ndi akulu mumpingo mwake kuti amthandize. Anapezanso mabwenzi atsopano. (Salmo 111:1) Atayesayesa mwamphamvu, Ann anakhalanso bwenzi la Mulungu. Tsopano pambuyo pa zaka zingapo, akuti: “Unansi wanga ndi Yehova walimba kwambiri.”

Mwa phunziro la Baibulo laumwini, kusinkhasinkha, khalidwe loongoka, ndi mabwenzi abwino, inunso mungakhale ndi ubwenzi wolimba ndi Mulungu. Komabe, kuusamala ubwenziwo ndi nkhani ina. Kodi kungatheke motani ngakhale pali zovuta ndi zofooka za munthu? Nkhani yotsatira mumpambo womwe uno idzalongosola mfundo imeneyi.

[Mawu a M’munsi]

a Onani makope a Galamukani! a August 8, ndi December 8, 1995.

b Onani “Achichepere Akufunsa Kuti . . . Kodi Nkuŵerengeranji Baibulo?” m’kope lathu la June 8, 1986.

[Chithunzi patsamba 24]

Kodi mabwenzi anga angandithandize kukhala bwenzi la Mulungu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena