Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 4/8 tsamba 8-10
  • Njira Yobwerera kumudzi wa Paradaiso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira Yobwerera kumudzi wa Paradaiso
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Paradaiso—Kumwamba Kapena pa Dziko Lapansi?
  • Paradaiso Wobwezeretsedwa
  • Chifukwa Chake Ena Amapita Kumwamba
  • Paradaiso Wauzimu Akulambula Njira
  • Kodi Paradaiso Amene Baibulo Limatchula ali Kuti?
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Paradaiso wa Chisangalalo kaamba ka Anthu Onse
    Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
  • Kodi Chifuno cha Mulungu cha Dziko Lapansi N’chiyani?
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • “Tidzaonana M’Paradaiso”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 4/8 tsamba 8-10

Njira Yobwerera kumudzi wa Paradaiso

POGANIZIRA za kulakalaka Paradaiso kwa munthu ndi zoyesayesa zake zazikulu ndi zazing’ono zomwe za kumpanganso, wina angaganize kuti podzafika lero dziko lapansi likanakhala paradaiso weniweni. Koma sizinachitike.

M’malo mwake, mtundu wa munthu watsogoza umbombo, umene nthaŵi zambiri wawonongetsa malo okhala ndi zamoyo zamitundumitundu. Pokhulupirira kuti chuma chakuthupi ndicho chidzalamulira zinthu, anthu ambiri ataya chiyembekezo chonse chakuti dziko lapansili kutsogoloku lidzasanduka paradaiso wonga Edene. M’malo mwake, iwo amaona kuti chiyembekezo chawo chokha cha Paradaiso ndicho moyo wa pambuyo pa imfa kumwamba. Lingaliro limeneli, choyamba, limatanthauza kuti kulakalaka kwathu Edene kwachibadwa sikudzakhutiritsidwa konse ndi kuti, chachiŵiri, pulanetili Mulungu walisiyira utsiru ndi umbombo wa anthu. Kodi ndi mmene zakhalira? Kodi mtsogolomu mulinji kwenikweni? Ndipo mtsogolomo mudzakhalira kuti?

Paradaiso—Kumwamba Kapena pa Dziko Lapansi?

Pafupifupi zaka 2,000 zapitazo, polankhula ndi mbala yolapa yopachikidwa pafupi naye chapambali, Yesu Kristu anati: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” (Luka 23:43) Kodi Yesu anatanthauza kuti mbalayo idzapita naye kumwamba? Ayi.

Wochita zoipayo sakanalingalira zimenezi nkomwe. Chifukwa ninji? Chifukwa ayenera kuti anadziŵa Malemba Achihebri amene analiko panthaŵi yake, monga mbali yoyamba ya Salmo 37:29: ‘Olungama adzalandira dziko lapansi.’ Yesu anaphunzitsa choonadi chimodzimodzicho, nalengeza kuti: ‘Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.’ (Mateyu 5:5) Lembali likugwirizana ndi limene ambiri amati Pemphero la Ambuye, limene limati: “Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:9, 10.

Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu analenga dziko lapansi kuti ndilo likhale kwawo kwa banja laumunthu, osati kumwamba. Mawu ake amati iye “sanalilenga mwachabe [dziko lapansi],” koma “analiumba akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Mpaka liti? “Anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthaŵi yonse.” (Salmo 104:5) Ndithudi, “dziko lingokhalabe masiku onse.”—Mlaliki 1:4.

Chifuno cha Mulungu nchakuti, dziko lapansi likhale mudzi wa unyinji wa amene akumtumikira kosatha. Onani mmene Mawu a Mulungu, Baibulo, amanenera pankhaniyi. Salmo 37:11 limaneneratu kuti: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” Mpaka liti? Salmo 37:29 limati: ‘Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.’ Panthaŵiyo lemba lidzakwaniritsidwa, lija limene limalengeza kuti: “Muolowetsa dzanja lanu [Mulungu], nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo,” kutanthauza chikhumbo chogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.—Salmo 145:16.

Nanga aja amene sakhumba kuchita chifuniro cha Mulungu? Miyambo 2:21, 22 imalengeza kuti: “Oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”

Paradaiso Wobwezeretsedwa

Kwatsala pang’ono tsopano kuti Mulungu apereke chiweruzo chake padziko loipali. (Mateyu 24:3-14; 2 Timoteo 3:1-5, 13) Koma Mulungu adzasunga “khamu lalikulu” la anthu pachiwonongeko chikudzacho ndi kuliloŵetsa m’dziko latsopano lokonzedwa ndi iye.—Chivumbulutso 7:9-17.

Kenako, Mulungu adzatsogolera ntchito yosangalatsa imene nzika zake zaumunthu zidzakhala nayo yosandutsa dziko lonse lapansi kukhala mudzi waparadaiso wa mtundu wa munthu. Baibulo likulonjeza kuti: “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duŵa. . . . Pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se.”—Yesaya 35:1, 6.

M’Paradaiso womafutukukayo, njala, umphaŵi, makomboni a anthu osauka, anthu opanda nyumba, kapena madera odzala ndi upandu kwambiri sizidzakhalakonso. “M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka.” (Salmo 72:16) “Mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zawo, ndi nthaka idzapereka zipatso zake.” (Ezekieli 34:27) “Adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya.” (Yesaya 65:21, 22) “Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa.”—Mika 4:4.

Chifukwa Chake Ena Amapita Kumwamba

Anthu ochuluka angavomereze kuti akumfuna kwambiri paradaiso wa padziko lapansi. Chimenecho nchachibadwa, chifukwa Mulungu sanawapatse chikhumbo cha kukhala kumwamba; iwo sangayerekezere nkomwe za mmene moyo ulili kumwamba. Mwachitsanzo, pokambitsirana ndi mtumiki wawo wa Church of England, Pat, ngakhale anali munthu wodzipereka wa tchalitchi chimenecho, anati: “Sindinayambe ndaganizapo zopita kumwamba. Sindikufuna kupitako, ndipotu ndingakachitekonji?”—Yerekezerani ndi Salmo 115:16.

Zoonadi, Baibulo limaphunzitsa kuti anthu angapo okha, 144,000, amapita kumwamba. (Chivumbulutso 14:1, 4) Ilo limafotokozanso chifukwa chake: ‘Mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.’ (Chivumbulutso 5:9, 10) Pamodzi ndi Mfumu yawo, Yesu Kristu, ameneŵa amapanga “ufumu,” boma lakumwamba latsopano la dziko lapansi, limene Akristu amapempherera. Bomali ndilo lidzayang’anira kukonzedwanso konse kwa dziko lapansi ndi mtundu wa munthu.—Danieli 2:44; 2 Petro 3:13.

Komabe, popeza anthu mwachibadwa alibe chikhumbo chokakhala kumwamba, mzimu wa Mulungu ‘umachita umboni’ mwa a 144,000 m’njira ina yake moti amamva ‘maitanidwe akumwamba’ apadera ameneŵa. (Aroma 8:16, 17; Afilipi 3:14) Koma ndithudi, ntchito imeneyi ya mzimu woyera siyofunikira kwa mtundu wonse wa munthu chifukwa chakuti mudzi wawo wachikhalire udzakhala padziko lapansi la paradaiso.

Paradaiso Wauzimu Akulambula Njira

Kodi munthu amayenerera motani kuti akakhale ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi? “Koma moyo wosatha ndi uwu,” anatero Yesu, “kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Posonyeza kuti maunansi amtendere a anthu ndi chidziŵitso cha Mulungu nzogwirizana, Yesaya 11:9 amati: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yerekezerani ndi Yesaya 48:18.

Komatu, chidziŵitso chimenechi si cha m’mutu chabe ayi. Chimakhudza umunthu wa munthu ndi kukulitsa mikhalidwe yaumulungu, monga “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” (Agalatiya 5:22, 23) Mboni za Yehova zimayesetsa kukulitsa mikhalidwe imeneyi, ndipo nchifukwa chake, ngakhale tsopano, zadalitsidwa ndi paradaiso wauzimu wabwino kwambiri.—Yesaya 65:13, 14.

Mmenetu mkhalidwe wawo wauzimu umasiyanirana ndi wa dziko, limene likumka likumirabe mu kusaopa Mulungu ndi chivundi! Ngakhale zili choncho, Mulungu posachedwapa adzaliwononga dziko loipali. Zinthu zidakali chonchi, Mboni za Yehova zikukuitanani kudzacheza—inde, kudzaona—paradaiso wauzimu amene zikusangalala naye. Dzipenyereni nokha kuti tsopano lino Yesu, Mfumu yosaoneka yakumwamba, mwakachetechete ikutsogoza nzika za dziko latsopano limenelo m’njira yopapatiza ya ku Paradaiso wa padziko lapansi ndi ku moyo wosatha!—Mateyu 7:13, 14; Chivumbulutso 7:17; 21:3, 4.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Opulumuka chimaliziro cha dzikoli adzasangalala kukhala ndi phande pakusandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena