Kodi Mulungu Amavomereza Chipembedzo Chiti?
MWATSOKA lake, kudana kwa zipembedzo ku France m’zaka za zana la 16 sikunathe ayi. M’zaka za zana lotsatira, tsankhu lalikulu linagaŵa Ulaya pakati, pamene Akatolika ndi Aprotesitanti anamenyananso pa Nkhondo ya Zaka Makumi Atatu (1618-48). Odzitcha Akristu amenewo anayambanso kumaphana mwankhalwe m’dzina la Mulungu.
Zipembedzo sizinasiye kumadana ndi kumaphana. Masiku ano Akatolika ndi Aprotesitanti aphana ku Ireland, ndipo a Orthodox ndi a Roma Katolika achitanso chimodzimodzi kudera lomwe kale linali Yugoslavia. Ngakhale zikuoneka zovuta kukhulupirira, Akatolika ndi Aprotesitanti omwe anapha okhulupirira anzawo zikwi mazanamazana a m’zipembedzo zawo mkati mwa Nkhondo Yadziko I ndi II. Kodi tingati kuphana kumeneku kunali bwino chabe? Kodi Mulungu amakuona bwanji?
Alimbikira Kulungamitsa Kuphana
Buku la 1995 Britannica Book of the Year linati: “Anthu osiyanasiyana anayesa kupereka zifukwa zaumulungu mu 1994 pofuna kulungamitsa chiwawa.” Zaka zoposa 1,500 zapitazo, Mkatolika wafilosofi, Augustine “Woyera Mtima,” anayesanso kulungamitsa kuphana. Malinga ndi New Catholic Encyclopedia, iyeyo ndiye “anayambitsa chiphunzitso chakuti pali nkhondo yolungama,” ndipo insaikulopediyayo imatero kuti malingaliro ake ‘akali amphamvu ngakhale masiku ano.’
Matchalitchi a Katolika, Orthodox, ndi Protesitanti alola, ngakhale kusonkhezera anthu kuphana m’dzina la Mulungu. Ngakhale kuti mbiri ya zipembedzo zimenezi njamwazi wokhawokha, zipembedzo zina zambiri padziko lonse sizinasiyane ayi. Nanga mungawadziŵe bwanji anthu amene ali ndi kulambira koona?
Si mwa kungomvetsera zonena zawo zakuti ali ndi chikhulupiriro. Za nkhani imeneyi, Yesu Kristu anachenjeza kuti: “Chenjerani ndi aneneri onyenga amene amadza kwa inu akunamizira kuti ndi nkhosa koma mkati mwake ali mimbulu yolusa. Mudzatha kuwadziŵa ndi zipatso zawo. . . . Mtengo wabwino umabala zipatso zabwino koma mtengo woipa, zipatso zoipa. . . . Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino audula nautaya pamoto.” (Kanyenye ngwathu.)—Mateyu 7:15-20, The New Jerusalem Bible.
Adziŵika ndi Zipatso Zawo
Anthu mamiliyoni ambiri oona mtima akuzindikira tsopano kuti zipembedzo za dzikoli zili ‘mitengo yoipa’ imene yabala “zipatso zoipa,” makamaka, mwa kusonkhezera nkhondo zamwazi. Baibulo limafotokoza kuti ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga ndiye mkazi wachigololo wauzimu wotchedwa ‘Babulo Wamkulu.’ Baibulo limatero kuti “momwemo [mwa mkaziyo] munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.”—Chivumbulutso 17:3-6; 18:24.
Chotero, m’malo movomereza nkhondo zimene atsogoleri achipembedzo azidalitsa, Mulungu posachedwa adzaweruza zipembedzo zimene zapha anthu m’dzina lake. Adzatero kukwaniritsa ulosi wa Baibulo womwe umati: “Babulo, mudzi waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.” Pamene chochitika chosangalatsa chimenecho chipita, Mulungu adzakhala ‘ataweruza mkazi wachigololo wamkulu’ ndi ‘kubwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.’—Chivumbulutso 18:21; 19:2.
Anthu amene anyansidwa ndi kuphana kumene kwachitika m’dzina la Mulungu angafune kudziŵa ngati alipo Akristu amene amatsatiradi ulosi wa Baibulo wakuti: “Adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yesaya 2:4) Kodi mukuwadziŵa anthu oopadi Mulungu amene atsutsa nkhondo?
Chipembedzo Chimene Mulungu Amavomereza
Nkhani yofufuza za kakhalidwe ka anthu yakuti “Zochuluka Ponena za Kulungamitsa Chiwawa,” imene Yunivesite ya Michigan inafalitsa, inati: “Kuchokera pamene zaka za zana lino zinayamba, Mboni za Yehova zapitiriza kosasintha ndi chikhulupiriro chawo cha ‘Uchete Wachikristu’ wopanda chiwawa pankhondo zadziko ziŵiri zazikulu ndi nkhondo zotsatirapo mkati mwa nyengo ya ‘Nkhondo ya Mawu.’” Posonyeza chifukwa chimene Mboni zimasungira uchete, ofufuzawo anati: “Maziko a ziphunzitso za Mboni za Yehova ndiwo chikhulupiriro chawo chakuti Baibulo lili mawu a Mulungu ouziridwa.”
Inde, Mboni za Yehova zimatsatira Baibulo, lomwe limaphunzitsa kuti: ‘Mmenemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a Mdyerekezi: yense wosachita chilungamo saali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake. . . . Tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini . . . anapha mbale wake.’—1 Yohane 3:10-12.
Nthaŵi zambiri Mboni za Yehova zauza anthu za mlandu wa mwazi umene zipembedzo za dzikoli zili nawo. Zalengezanso pempho lochonderera ndi lofulumiza la m’Baibulo lakuti: “Tulukani mmenemo [m’Babulo Wamkulu], anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake; pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira m’Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.”—Chivumbulutso 18:4, 5.
Anthu ambiri oona mtima akulabadira chiitano chimenechi chakuti achoke mu ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Ngati mukuchitadi kakasi ndi kuphana kochitika m’dzina la chipembedzo, tikupemphani kuonana ndi munthu amene anakupatsani magazini iyi kapena kulembera kukeyala yosonyezedwa patsamba 5. Mboni za Yehova zidzakonda kukuthandizani kuphunzira za malonjezo a Baibulo onena za dziko latsopano lolungama, limene simudzakhalanso nkhondo.—Salmo 46:8, 9; 2 Petro 3:13.
[Chithunzi patsamba 10]
“Avomereza kuti adziŵa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana iye.” Tito 1:16