Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 7/8 tsamba 9-11
  • Pamene Dziko Lonse Lapansi Lidzakhala Malo Achisungiko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Dziko Lonse Lapansi Lidzakhala Malo Achisungiko
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nchifukwa Ninji Khama Lonselo Likulephera?
  • Zokha Zomwe Tikuyembekezera Kusinthadi Dziko Lapansi Kukhala Lachisungiko
  • Malo Osungiramo Nyama—Kodi Ndiwo Okha Adzapulumutsa Nyama za Kuthengo?
    Galamukani!—1997
  • Kodi Munapitako ku Malo Osungira Nyama?
    Galamukani!—2012
  • “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
    “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
  • Kodi Anthu Apitiriza Kuwononga Dzikoli N’kufika Poti Silingakonzedwenso?
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 7/8 tsamba 9-11

Pamene Dziko Lonse Lapansi Lidzakhala Malo Achisungiko

KODI mukufuna kuona cholengedwa choopsa koposa padziko? Yang’anani m’kalirole! Inde, ifeyo, anthu, ndife olusira dziko lapansi koposa! Ndipotu timapululutsana tokhatokha.

Kuti dziko lapansi likhale malo otetezereka a nyama zamtchire, ngakhale m’malo osungiramo nyama—makamaka ngati iwo adzakhala malo okha opulumukirako—nkhondo, mliri pa anthu, iyenera kutha. Panyama 12,000 za m’Berlin Zoo, 91 peresenti yokha ndizo zinapulumuka Nkhondo Yadziko II. Malo ena ambiri osungiramo nyama anaonanso tsoka limodzimodzilo. Pankhondo yaposachedwa kumaiko a Balkan, antchito olimba mtima a malo osungiramo nyama anapulumutsa nyama zambiri; koma zinanso mazanamazana, kuphatikizapo deer, nyama zapachibale ndi mkango, zimbalangondo, ndi mimbulu, zinaphedwa. Posachedwa, m’nkhalango za ku Cambodia, malinga ndi akuluakulu a boma ogwidwa mawu m’nyuzipepala yakuti The Australian, a Khmer Rouge apha dala nyama zosapezekapezeka. Chifukwa? Kuti asinthanitse zikumba zake ndi ziŵalo zake zina ndi zida za nkhondo!

Choipa china choyenera kutha kuti nyama zikhale pamtendere, mkati ndi kunja kwa malo ozisungiramo, ndicho kuwononga dala malo konga kuja kunachitika kuzisumbu zakutali za Peron Islands, kummwera koma chakumadzulo kwa Darwin, ku Australia. Kaŵiri pazaka zitatu, anatentha zisa za avuwo pazisumbuzo, mwachionekere popanda chifukwa china chilichonse kusiyapo kungofuna kupha mwankhalwe zedi ana a mbalame omwe sanayambebe kuuluka.

Komabe, pazaka makumi zapitazi, mitundu ya zamoyo yatayika si chifukwa cha njiru ayi; koma chifukwa cha kuwonjezeka kwa chiŵerengero cha anthu ofuna malo okhala ndi olima. Chifukwa chowononga nkhalango za nyama mosaleka ndi kuipitsa kumene kumatsatirapo, The World Zoo Conservation Strategy ikuchenjeza kuti: “Sitikuyembekezera kuti zinthu zachilengedwe za dziko lapansi zidzakhala bwino m’zaka za zana la 21 ayi. Palibe umboni wakuti kuwononga zinthu kumene kukuchitika kumbali zonse za dziko kudzatha posachedwa.”

Chifukwa cha nkhaŵa imene ambiri akukhala nayo ponena za mmene dziko lapansi lidzakhalira mtsogolo, nthaŵi imene pulaneti lonseli lidzakhala malo achisungiko ikumveka ngati yosatheka chifukwa yanyanya kukoma. Ayi, chiyembekezo chimenecho maziko ake ngolimba, ndipo si anthu osaona pataliwa ayi—amene pazaka zochepa chabe zokwanira 50 zapitazo, malinga ndi wina wolemba za sayansi, sanadziŵe za kuwononga zamoyo ndi malo ake kumene kwachitikaku—koma ndi iye amene anaoneratu zimenezi, Yehova Mulungu. Zaka zoposa mazana khumi ndi asanu ndi anayi zapitazo, iye analosera kuti anthu, panthaŵi yathu, adzakhala “akuwononga dziko.” (Chivumbulutso 11:18) Popeza ulosiwo anaunena pamene dziko lapansi linalibe anthu ambiri, ungakhale unaoneka ngati maloto kwa ambiri amoyo panthaŵiyo, komatu wakhala woona kwambiri!

Zodabwitsa nzakuti kuwononga kumeneku kukuchitika panthaŵi imene sayansi ndi tekinoloji zikuoneka ngati zangotsala pang’ono kuchita zozizwitsa: tizipangizo totumiza mauthenga totchedwa microtransmitter ndi masetilaiti zimayang’anira nyama zimene zili pafupi kusoloka, nkhalango za mvula zowonongeka amazipima kufika pa square meter ali mumlengalenga, ndipo kuipa kwa mpweya amakupima kufika pa mlingo waung’onong’ono. Koma nthaŵi zambiri munthu amachita ngati satha kuchitapo kanthu pa chidziŵitso chochuluka chonsechi. Mwina tinene kuti munthu ali ngati woyendetsa sitima yothamanga kwambiri imene yakana kuima. Kachipinda kake kali ndi zonse zofunikira poiwongolera ndi makina omusonyeza zonse zomwe zikuchitika, koma iye satha kuiimitsa sitimayo!

Nchifukwa Ninji Khama Lonselo Likulephera?

Tayerekezerani kuti m’fakitale yaikulu, manijala wina wonyada ndi wopanda khalidwe wamva mwini fakitaleyo akunena kuti iyeyo sadzamkweza pantchito koma m’malo mwake, adzamchotsa ntchito miyezi ingapo ikudzayo. Pokhala waipidwa ndipo wadzaza njiru, ayamba kunena mabodza, kupatsa ena ziphuphu, ndi kuchita machenjera amtundu uliwonse kuti antchito ambiri ayambe msokonezo. Iwo akupha dala makina, ntchito iyamba kuchedwa, ndipo zimene apanga sizikhala zabwino ayi—koma achita zonsezo mwamachenjera kuti asaoneke amlandu. Zili choncho, antchito oona mtima, posadziŵa zimene zikuchitika kwenikweni, akuyesa kukonza makina; koma akamayesetsa kwambiri, zinthu zikuipiraipiranso kwambiri.

Mofanana ndi ameneyo, “manijala” wosaona mtima wa dzikoli wachitira anthu ndi dziko lapansi chiwembu. Koma ife sitiyenera kukhala “osadziŵa machenjerero ake,” pakuti Baibulo limang’amba chinyau chake ndi kuvumbula cholengedwa chauzimu chanjiru—Satana Mdyerekezi—mngelo amene anadzitukumula nalakalaka kulambiridwa. (2 Akorinto 2:11; 4:4) Mulungu anampitikitsa m’banja Lake lakumwamba namweruzira kuchiwonongeko.—Genesis 3:15; Aroma 16:20.

Mofanana ndi manijala uja wosaona mtima wa fakitale, “atate wake wa bodza” ameneyu amagwiritsiranso ntchito njira zamachenjera kusonyeza mkwiyo wake. Amada Yehova Mulungu ndipo akufuna kuwononga chilengedwe Chake. (Yohane 8:44) Zida zamphamvu kwambiri zimene Satana amagwiritsira ntchito ndizo manenanena onama, umbombo, kukonda chuma, ndi ziphunzitso zovulaza za zipembedzo. Ndi zimenezi, ‘wanyenga dziko lonse’ ndipo wasandutsa anthu—amene anayenera kuliyang’anira dziko lapansi—kukhala olifunkha mopanda chisoni, kwenikweni, ophunzira a Nimrode wakale, “mpalu wamphamvu wotsutsana ndi Yehova.”—Chivumbulutso 12:9, 12; Genesis 1:28; 10:9, NW.

Zokha Zomwe Tikuyembekezera Kusinthadi Dziko Lapansi Kukhala Lachisungiko

Komabe, nzotheka kuwalaka anthu ndi makamu a mizimu amene akusolotsa zinthu. Mlengi wamphamvuyonse wa zamoyo zonse atha kutipulumutsa pangozi imeneyi yoopsa, ndipo walonjeza kuchita zimenezo mwa boma lake lakumwamba. Walonjeza kuwononga anthu olusa amenewo amene akuwononga dziko lapansi. Timapempherera zomwezi tikamati: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitike m’dziko, monga kulili kumwamba.”—Mateyu 6:9, 10, King James Version; Chivumbulutso 11:18.

Kodi mwaona kuti kudza kwa Ufumu kwagwirizana ndi kuchitika kwa chifuniro cha Mulungu padziko lapansi? Zili choncho chifukwa Ufumu wa Mulungu ndiwo boma la Mulungu lolamulira dziko lapansi. Ndipo pokhala ufumu, uli ndi mfumu yake—Yesu Kristu, “Mfumu ya Mafumu, ndi Mbuye wa Ambuye.” (Chivumbulutso 19:16) Ulinso ndi anthu ake. Kwenikweni, Yesu anati: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” (Mateyu 5:5) Inde, ofatsa ameneŵa ndiwo anthu ake a padziko lapansi, ndipo mothandizidwa ndi Ufumu wa Mulungu, adzasamalira choloŵa chawo mwachikondi, kuchisandutsa paradaiso wodzala zamoyo. Ndipotu ngakhale buku la Strategy limati: “Mtsogolo mwa anthu ndi dziko lapansi mudzakhala mwabwino kokha ngati anthu onse angakhale ndi chimvano chatsopano ndi dziko lapansi.”

Mbiri yakale ndi kupanda ungwiro kwa chibadwa cha munthu zimasonyeza kuti nzosatheka kwa “anthu onse” lero kukhala ndi “chimvano chatsopano” chimenecho ndi dziko lapansi, pakuti iwo amnyalanyaza Yehova. Ndiye chifukwa china chimene Mulungu walolera dzikoli kupitiriza nthaŵi yaitali chonchi, kuti asonyeze kuti kudzilamulira kwa anthu nkwachabe. Koma posachedwa, amene amalakalaka ulamuliro wa Kristu adzakhala ndi mtendere wochuluka. Yesaya 11:9 akutsimikiza zimenezo, ndipo akusonyezanso chifukwa chake ameneŵa okha adzakhala ndi “chimvano chatsopano” ndi dziko lapansi: ‘Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’ Inde, maphunziro aumulungu ndiwo adzachititsa zimenezo. Ndipo zimenezo si zoyenera nanga, pakuti ndani wina ali ndi nzeru ngati za Mlengi wa dziko lapansi?

Nanga bwanji za aja amene aumirira kunyalanyaza Yehova? “Koma oipa adzalikhidwa m’dziko,” imatero Miyambo 2:22. Inde, liuma lawo kapena mphwayi yawo idzawawonongetsa pa “chisautso chachikulu” chomwe chayandikira kwambiri—njira imene Mulungu adzaperekera chiweruzo pa iwo onse olimbikira kufunkha chilengedwe chake mwadyera ndi kuchiwononga.—Chivumbulutso 7:14; 11:18.

Kodi mukufuna kudzachita nawo ntchito yokonza dziko lapansi? Ndiye phunzirani chonde zimene Mulungu akufuna kwa inu mwa kuphunzira Baibulo. Ndi lokhalo lomwe lili ndi mphamvu yosintha maganizo anu kuti akhale ngati a Mlengi. (2 Timoteo 3:16; Ahebri 4:12) Ndiponso, mwa kutsatira zomwe mukuphunzira, simudzangokhala nzika yabwino tsopano koma mudzasonyezanso kuti mulidi mtundu wa munthu amene Yehova adzapatsa “dziko latsopano” lomwe layandikira kwambiri.—2 Petro 3:13.

Ofalitsa magazini ino kapena mpingo wapafupi kwambiri ndi kwanu wa Mboni za Yehova angakonde kukuthandizani kuphunzira Baibulo kwaulere panyumba panu kapena kukupatsani mabuku enanso ofotokoza zinthu zimenezi ngati mukufuna.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena