Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 9/8 tsamba 30-31
  • Nanga Angathetsedwe Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nanga Angathetsedwe Bwanji?
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Maziko a Chiyembekezo Chodalirika
  • Zimene Mulungu Adzachita
  • Kumene Kuli Mavuto Aakulu
    Galamukani!—1997
  • Kufufuza Madzi Amoyo
    Galamukani!—2001
  • Kodi Padzikoli Madzi Akutha?
    Galamukani!—2001
  • Madzi Opatsa Moyo Wosatha
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 9/8 tsamba 30-31

Nanga Angathetsedwe Bwanji?

AKATSWIRI akukambirana mwamphamvu njira zothetsera mavuto aakulu a anthu a kusoŵa madzi. World Bank ikufuna $600,000,000,000 zoti zidzathandize pantchito yotaya zinyalala ndi ntchito za madzi m’zaka khumi zikudzazi. Ndalama zowonongedwa chifukwa chonyalanyaza kuchita zimenezo zingakhale zochuluka. Mwachitsanzo, ku Peru mliri wa kolera wamilungu khumi, wofalitsidwa ndi madzi auve, posachedwapa unawonongetsa ndalama zokwana $1,000,000,000—kuŵirikiza katatu ndalama zimene zinawonongedwa pantchito yobweretsa madzi m’dzikomo m’zaka za m’ma 1980.

Komabe, ngakhale kuti anthu amene amalimbikitsa ntchitozi amakhala nzolinga zabwino, ntchito za madzi kaŵirikaŵiri sizithandiza kwenikweni anthu osauka kwambiri. Mizinda yaikulu ya m’maiko omatukuka ikukula mofulumira kwambiri ndiponso mosalongosoka. Anthu osauka amakhala m’zithando zothinana, zosasamalika, zopanda madzi a m’mipope ndi zimbudzi. Popeza kuti kulibe utumiki wa madzi, iwo amagula madzi kwa anthu wamba pa mtengo wokwera, kaŵirikaŵiri madzi auve.

Ndithudi, mavuto a madzi padziko lonse lapansi ngaakulu ndipo amaphatikizapo zinthu izi: kusoŵa, kuipitsa, umphaŵi, matenda, ndi chiŵerengero chomakula cha anthu osoŵa madzi. Nzodziŵikiratu kuti anthu sangathetse mavuto ameneŵa.

Maziko a Chiyembekezo Chodalirika

Komabe, mtsogolomu zinthu sizidzafika poipa monga momwe anthu ambiri amaganizira. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti si anthu amene angathetse mavuto a kusoŵa kwa madzi; angachite zimenezo ndi Mulungu. Ndi yekhayo amene angathe komanso amene ali ndi chifuno chothetsa mavuto a madzi.

Zoti Yehova Mulungu ndiye angathetse mavutowa nzosachita kufunsa. Iye ndiye Mpangi ndi Mlengi osati wa dziko lapansi lokha komanso madzi opezeka mmenemo. Ndi iyeyo amene anayambitsa kuti madzi aziyenda mosalekeza pamodzi ndi zinthu zina zambiri zimene zimayenda mosalekeza zopangitsa kuti padziko lapansi pakhale moyo. Chivumbulutso 14:7 chimatchula Yehova kuti ndi “Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe a madzi.”

Yehova ali ndi mphamvu yolamulira madzi a padziko lapansi. Iye ndiye “amene avumbitsa mvula panthaka, natumiza madzi paminda.” (Yobu 5:10) Ponena za iye Baibulo limati: “Asanduliza chipululu chikhale thawale, ndi dziko louma likhale akasupe a madzi.”—Salmo 107:35.

Mobwerezabwereza, iye wasonyeza mphamvu yake yobweretsa madzi. Mwachitsanzo, anapatsa madzi Aisrayeli pamene anali m’chipululu kwa zaka 40, nthaŵi zina mozizwitsa. “Anatulukitsa mitsinje m’thanthwe, inde anatsikitsa madzi ngati mitsinje,” limatero Baibulo. “Taonani, anapanda thanthwe, ndi madzi anayendako ndi mitsinje inasefuka.”—Salmo 78:16, 20.

Zimene Mulungu Adzachita

Mulungu sadzalola mavuto a madzi kupitirizabe mpaka muyaya. Baibulo limaneneratu kuti ikudza nthaŵi imene iye adzathandiza onse padziko lapansi amene akufuna kudzakhala pansi pa ulamuliro wachikondi wa boma lake lakumwamba, limene posachedwapa lidzalamulira dziko lapansi.—Mateyu 6:10.

Boma limenelo, kapena Ufumu, lidzathetsa matenda ofalitsidwa ndi madzi, pamodzi ndi matenda ena onse. Baibulo likutsimikizira anthu okhulupirika a Mulungu kuti: ‘[Mulungu] adzadalitsa chakudya chako, ndi madzi ako; ndipo adzachotsa nthenda pakati pa iwe.’ (Eksodo 23:25) Ndiponso, anthu owononga dziko adzatha psiti pamene iye ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’—Chivumbulutso 11:18.

Dziko lonse lapansi lidzakondwa posamalidwa ndi Mulungu. Anthu sadzavutikanso kupeza madzi abwino, oyera. Mulungu Wamphamvuyonse, amene amanena zoona nthaŵi zonse, anauzira mneneri wake kulemba za mtsogolo kuti: “Pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se. Ndipo mchenga wong’azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime za madzi.”—Yesaya 35:6, 7; Ahebri 6:18.

[Chithunzi patsamba 30]

Mulungu akulonjeza kuti: “M’chipululu madzi adzatuluka, . . . ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime za madzi.”—Yesaya 35:6, 7

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena