Nchifukwa Ninji Pali Chidani Chochuluka?
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU GERMANY
“NCHIFUKWA NINJI”—ndi mawu aafupi amenewo, koma amafuna yankho. Mwachitsanzo, pamene anaonedwa atalembedwa pakapepala pa mulu wa maluŵa ndi zidole kunja kwa sukulu ina yake ku Dunblane, Scotland, mu March 1996. Masiku oŵerengeka okha zisanachitike zimenezo, mwamuna wina analoŵa mofulumira nawombera mfuti ana 16 ndi mphunzitsi wawo kuwapha. Anavulazanso ena ambiri ndiyeno nkudzipha. Mwachionekere, mtima wake unadzala chidani chokhachokha—pa iye mwini, pa ena, ndi anthu onse. Makolo olira ndi mabwenzi limodzinso ndi anthu mamiliyoni ambirimbiri padziko lonse akufunsa funso limodzimodzilo, ‘Nchifukwa ninji? Nchifukwa ninji ana opanda mlandu amafa mwanjira imeneyo?’
Inunso simunalephere kuona kuti dziko ladzala chidani chanjiru ndi chosafotokozeka. Ndipotu, pazifukwa zosiyanasiyana, mwina inu mwininu ena anakudanipo. Mwinanso mwafunsapo kuti, ‘Nchifukwa ninji?’—mwina kangapo ndithu.
Chidani Choyenera ndi Chosayenera
“Chidani” ndicho “kuipidwa kwambiri ndiponso kunyansidwa.” Inde, “kuipidwa kwambiri ndiponso kunyansidwa” ndi zinthu zovulaza kapena zimene zingawononge unansi wako ndi anthu ena kumathandiza. Ngati aliyense anali ndi chidani choterechi, dziko likanakhaladi malo abwino kukhalamo. Komabe, nzachisoni kuti anthu opanda ungwiro amada zinthu zosayenera kuzida ndiponso pazifukwa zolakwikanso.
Chidani chowononga zinthu chimakhalapo chifukwa cha tsankhu, umbuli, kapena chidziŵitso cholakwika ndipo nthaŵi zambiri chimayamba chifukwa cha “mantha, mkwiyo, kapena kuopa kuvulala,” malinga ndi kutanthauzira kwina. Popanda maziko enieni, chidani chimenechi chimadzetsa zoipa ndipo mobwerezabwereza chimabutsa funso lakuti, ‘Nchifukwa ninji?’
Tonsefe tikuwadziŵa anthu amene khalidwe lawo kapena zizoloŵezi zawo zimatikwiyitsa nthaŵi zina amenenso zimativuta kugwirizana nawo. Koma kukwiya ndi nkhani ina; kufuna kuvulaza anthu ndi nkhani inanso. Chotero, zimativuta kumvetsa chifukwa chake munthu angakhalire ndi chidani pa magulu onse a anthu, kaŵirikaŵiri anthu amene sakuwadziŵa nkomwe. Iwo sangagwirizane ndi malingaliro ake a ndale, angakhale a chipembedzo china, kapena fuko lina, koma kodi chimenecho ndicho chifukwa chowadera?
Komabe, chidani chotero chilipo! Mu Afirika chidani chinasonkhezera mtundu wa Ahutu ndi wa Atusi kuphana ku Rwanda mu 1994, zimene zinapangitsa mtolankhani wina kufunsa kuti: “Kodi chidani chachikulu motero chinakula motani m’dziko laling’onolo?” Ku Middle East, chidani nchimene chachititsa uchigaŵenga wa Aluya ndi Aisrayeli oyaluka. Ku Ulaya chidani chinanyonyotsola dziko lomwe kale linali Yugoslavia. Ndipo malinga ndi lipoti lina la m’nyuzipepala, ku United States kokha “magulu ngati 250 ochirikiza chidani” akuwanditsa mzimu wa ufuko. Nchifukwa ninji pali chidani chochuluka? Nchifukwa ninji?
Chidani nchozika mizu kwambiri koti ngakhale pamene mikangano imene chimabutsa yatha, chimapitirizabe. Kodi tingafotokozenso motani vuto limene limakhalapo posungitsa mtendere ndi kuletsa kumenyana m’maiko osakazidwa ndi nkhondo ndi zauchigaŵenga? Kodi tingazifotokozenso motani zimene zinachitika pambuyo posainirana pangano la mtendere kumapeto kwa 1995 ku Paris limene linati mzinda wa Sarajevo ugwirizane pansi pa Fedareshoni ya Bosnia ndi Herzegovina-Croatia? Asebu ambiri okhala mumzindawo anayamba kuthaŵamo ndi m’miraga yake kuopa kulangidwa. Posimba kuti anthu anali kufunkha nyumba zomwe anali kusiya atazitentha, magazini ya Time inamaliza kuti: “Sarajevo wagwirizananso; koma anthu ake sanagwirizane.”
Kwenikweni mtendere pakati pa anthu omwe amadana umangokhala mtendere wonyenga, wopanda pake monga ndalama zonyenga. Popanda china chamtengo wapatali chouchirikiza, umasweka zinthu zitangovuta pang’ono. Koma m’dziko muli chidani chochuluka ndi chikondi chochepa. Nchifukwa ninji?
[Mawu Otsindika patsamba 4]
Chidani chowononga zinthu chimakhalapo chifukwa cha tsankhu, umbuli, kapena chidziŵitso cholakwika