Chenjerani! Akuba Ali Pantchito
YEREKEZERANI za chochitikachi. Kwaomba mkuntho. Mphepo yowononga yaleka kuomba mwamphamvu, ndipo madzi osefukira aja salinso angozi chifukwa aphwa tsopano. Anthu opulumuka amantha akutuluka komwe anabisala, pamene cha apo pakubwera anthu amantha ndi othedwa nzeru omwe anali atawatulutsa kunoko ndipo akubwera kudzaona zomwe mkunthowo wawononga. Madenga anyumba atengedwa ndi mphepo; mitengo yazulidwa ndipo ili pamwamba pa nyumba. Mawaya amagetsi aduka, zikumapangitsa kuimba telefoni ndi kutumiza uthenga wadzidzidzi kukhala kosatheka. Nyumba zina, zomwe kale munali mabanja osangalala zagwa—zawonongeka kosati nkukonzedwanso. Mudzi womwe kale unali wabata ndi wamtendere tsopano ndi mabwinja ndi wogwetsa mphwayi.
Anthuwo tsopano apezanso mphamvu—akonzeka kumanganso. Anthu akuthandizana wina ndi mnzake; ena mpaka tsopano sanadziŵane maina. Amuna akubwerekana zida ndi kugaŵana nzeru. Azimayi akuphikira gulu logwira ntchitolo chakudya pamene ana okulirapo akulera ana anzawo. Kuchokera mbali zina, kukubwera magalimoto ondondozana atanyamula anthu odzathandiza kugwira ntchito—amisiri okonza madenga, ochotsa mitengo, akalipentala, opaka penti. Komabe, kwabweranso anthu akuba pamodzi nawo, ali okonzeka kukwangwanutsa opulumukawo.
Akupempha kuwalipira dipoziti yaikulu asanakonze kanthu kalikonse. Eni nyumba othedwa nzeruwo akupereka ndalama zawo, nkungoona kuti amisiriwo apita, osadzaonekanso. Amisiri okonza madenga omwe amati “akonza bwino,” angokonza pamwambamwamba chabe mwakuti madengawo akudontha kutangogwa mvula yoyamba. Ochotsa mitengowo akunena kuti afuna akabwereke zida zamphamvu zodzagwirira ntchito maŵa, choncho akutengeratu kwa ovutikawo zikwizikwi za ndalama. Komatu maŵa lake litafika, sakuoneka.
Phatikizani kuwonongeka kwa katundu ndi kuwabera ndiye kukhumudwa kwa eni nyumba amene anapereka ndalama zambiri ku makampani a inshuwalansi akugwa kapena achinyengo amene tsopano akukana kupereka ndalama zokonzetsera zinthu zowonongekazo kapena omwe anatseka maofesi awo, ndipo eniwo anathaŵa. Amwaŵi omwe alandirako ndalama za inshuwalansi kuti akonzetse zowonongeka apeza kuti kaŵirikaŵiri amisiri osalongosoka ndi osadziŵa ntchito ndiwo apezeka kuti akonze zowonongekazo pamene oŵerengeka omwe alipo odziŵa ntchito sangakwanitse ntchito yonse. Zotsatira zake, pachitika ntchito yosalongosoka, zokhazokha zokhumudwitsa eni nyumba oŵawidwa mtimawo.
Opezeka m’ngozi amawabera nthaŵi ndi nthaŵi. Zomwe poyamba zimaoneka ngati kugwirizana kwa anthu ovutika kuti athandizane, zimasanduka zomvetsa chisoni kwa ena.
Kudera lina kutachitika namondwe, bisiketi zozuna zitalizitali zinakwera mtengo kufika pa $4, mtengo wosayembekezereka, ndi zakudya za ana zimadyera azimayi $6 chitini chimodzi. M’sitolo ina kuti ugule mabatire umayenera kugula kaye TV kapena wailesi. Ogulitsa katundu wofunika pazomangamanga anadzazitsa matumba awo a ndalama tololo mwa kugulitsa katundu pamtengo wokwera kwambiri. Pa chochitika china eni nyumba zochita kukoka zomwe zinakokedwera kumtunda madzi atasefukira anaona mitengo ikukwera ndi 600 peresenti. Kutachitika chivomezi, mayi wina wazaka 84 amene nyumba yake inawonongeka analandira telefoni kwa winawake akumanama kuti ndi wantchito wa boma. Mayiyo anaganiza kuti mapepala amene anasaina pambuyo pake anali opemphera chithandizo cha boma ndi zikalata zolandirira chakudya. Koma kwenikweni, zinali pangano lakuti adzawalipira $18,000 atamkonzera nyumba ndi kuti nyumba yakeyo ndiyo chikole iye atalephera kuwalipira, koma zinapezeka kuti zimene anakonza zinangokwana $ 5,000.
Kubera anthu pa Malonda a pa Telefoni
‘Zikomo kwambiri, akazi a S——! Lero ndi tsiku lanu la mwaŵi.’ Awa akhoza kukhala mawu oyamba pa telefoni yobwera mosayembekezereka. ‘Inu ndiye mwapata mphotho yoyamba ya . . .’ Anthu ambiri alandirapo mafoni otero akumati “apata kale mphotho,” kuti mphotho zawo “zilipo.” “Mphothoyo” imakhala mwina galimoto yatsopano, wailesi, makina a disiki, TV, kamera ya vidiyo, mwina mphete ya diamondi.
Kodi munayamba mwalandirapo foni yotero yakuti mudzalandira mphotho yaulere? Kodi mtima wanu unasangalala nazo? Kodi munakayikira? Ngati munakhulupirira zimene anakuuzani, kodi munalandiradi mphothoyo? Kapena mwina ndinu mmodzi woberedwa pa malonda a patelefoni? Ngati zoterezi zakuchitikirani, simuli nokha. Malinga ndi magazini ya Consumers’ Research, mu United States mokha, onyenga apatelefoni amabera anthu ngati khumi mphindi iliyonse. Chaka chilichonse anthu achinyengo opanda khalidweŵa amaba $10,000,000,000 kufika $40,000,000,000 kwa ogula, pafupifupi $7,500 mphindi iliyonse.
“Chaka chilichonse m’Canada,” ikutero Reader’s Digest, “Anthu oposa 150,000 amayankha ndi mafoni ochokera kwa akuba ochita malonda patelefoni omwe amawauza kuti ‘apata mphotho’ kapena ‘asankhidwa’ kuti alandire mphotho yoyamba. Ndipo chaka chilichonse anthu a ku Canada amawapusitsa mafoni ameneŵa, munthu aliyense akumawononga $2,000 kuti akalandire mphotho yawo.” Wapolisi wa m’Chigawo cha Ontario anati: “Chinyengo cha patelefoni ndicho chimodzi cha zinyengo zazikulu m’mbiri ya Canada.” Akuwonjezera kuti: “Tikudziŵa kuti zimatengera anthu a ku Canada mamiliyoni a madola pachaka.” Ziŵerengerozi ndi zija zomwe zinakanenedwa kupolisi. Komabe, popeza akuti ndi okwana ngati 10 peresenti yokha ya oberedwa amene amakanena kupolisi zomwe awabera, nkosatheka kudziŵa bwino ukulu wake wa vutolo.
“Timawauza anthu kuti apambana motero sathanso kulingalira bwino,” anavomereza katswiri wakuba. Anawonjezera kuti: “Ndiye timawalimbikitsa kutumiza ndalama, timawaumiriza kutumiza ndalama ngakhale akane motani.” Akangomubera munthu, dzina lake amaligulitsa kwa makampani ena ochita malonda patelefoni nkulilemba pandandanda ya “osavuta kupusitsa.” Maina awo angawagulitse kwa ena amenenso angamawaimbire telefoni mobwerezabwereza. “Tikamaimbira foni aja okhala pandandanda ya osavuta kupusitsa,” akutero yemwe kale anali wolandira matelefoni a ochita malondawo ku Toronto, “timasonkhezera pafupifupi 75 peresenti ya anthuwo kugula panthaŵi yoyamba yomweyo. Chiŵerengecho chimatsika kufika 50 peresenti pamene tiwaimbira telefoni kachitatu okhala pa ndandandayo. Koma anthu ena akayamba, amangopitirizabe; amakhalabe ndi ganizo lopata ndalama zambiri.”
Kodi amene amagwa mumsampha wa amalonda a patelefoni amafika mpaka pati ndi lingaliro lawo lofuna kupata mphotho yapamwamba? “Timagwirizana ndi a banki kuti asamalole anthu ena achikulire kuchotsa ndalama zawo kuopa kuti zonse zingatheretu,” akutero wapolisi wina. Mayi wina amene mwamuna wake anamwalira chaposachedwa anapezeka kuti anatumiza malipiro 36 kwa amalonda a pa telefoni 16, zomwe ziposa $85,000. M’malo mwake analandira “mphotho zopanda pake zokwana theka la chipinda.”
Kunyenga Anthu Ophunzira Kwambiri Mochenjera Kwambiri
Komabe, amene amachita umbala umenewu, sasankha. Amabera anthu osiyanasiyana m’zachuma. Mwina ngakhale ophunzira kwambiri anyengedwa. Chinyengocho amachichita mochenjera mwakuti ngakhale anthu ochenjera kwambiri amawabera. Akuba mwachinyengo amalengeza zinthu zokwera mtengo pawailesi yakanema ncholinga chobera anthu ophunzira ogula zinthuzo kapenanso m’mabuku okhala ndi zithunzi zokongola omwe amatumiza kwa iwo papositi. Zingakhale kuika ndalama m’mabizinesi amene angaoneke kuti ndi aphindu lalikulu—kuika ndalama m’bizinesi yokonza akanema, golide ndi migodi ya golide, kapena zitsime za mafuta. Ndandandayo njaitali. Komabe, zotsatira zake nzofanana—kuluza kwakukulu.
“Mmene chimakhalira chinyengo chawo simungakhulupirire,” anatero mayi wina wophunzira yemwe ananyengedwa. “Monga mphunzitsi pasukulu, ndinkalingalira kuti ndine wochenjera. . . . Anandilonjeza zambirimbiri.” Analuza $20,000 m’kampani yopanga akanema.
Kubera anthu m’malonda a patelefoni ndi vuto la m’maiko ambiri. Ofufuza milandu akulingalira kuti mwina “lidzakula m’zaka khumi zino.” Koma, chenjerani! Palinso mtundu wina wa kuba, ndipo akatswiri ena achinyengo ali ndi omwe amawaderera—nkhalamba.
[Chithunzi patsamba 18]
Chenjerani ndi akuba omwe amabwera kukachitika mkuntho!
[Chithunzi patsamba 19]
“Mwapata mphotho yaulere!”—koma kodi mwaterodi?