Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 10/8 tsamba 23-24
  • Kuba M’dzina la Chipembedzo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuba M’dzina la Chipembedzo
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Njira Zambiri za Kuba m’Dzina la Chipembedzo
  • Kubera okalamba
    Galamukani!—1997
  • Mmene Mungadzitetezere Kwa Anthu Oba Mwachinyengo
    Galamukani!—2004
  • Chenjerani! Akuba Ali Pantchito
    Galamukani!—1997
  • Timagulu Totsatira Anthu—Kodi Ito Nchiyani?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 10/8 tsamba 23-24

Kuba M’dzina la Chipembedzo

NGATI mwadabwa ndiponso kuchita chisoni chifukwa cha kubera anthu komwe tatchulaku, simuli nokha. Koma pali kuba kwina koipa kwambiri—m’dzina la chipembedzo. Kofala kwambiri ndi kuja kokhudza chikhulupiriro chakuti sou imakhalabe ndi moyo pambuyo pa imfa ndi kuti amoyo akhoza kuthandiza akufa. Chifukwa cha zimenezo mamiliyoni a anthu oona mtima amakhulupirira kuti mwa kulipira ndalama zambiri, akhoza kuthandiza kapena kutonthoza okondedwa awo akufa.

Lerolino, m’maiko ena pali njira yatsopano yochitira chinyengo chakale chimenechi. Mwachitsanzo, posachedwapa ku Japan, ansembe achibuda amuna ndi akazi omwe ananena kuti ali ndi mphamvu zauzimu anagwidwa powaganizira kuti anabera anthu ndalama zokwana mayeni mamiliyoni mazana ambirimbiri. Ogwidwawo anali atalengeza kuti amachiritsa ndipo amapatsa anthu uphungu wothandiza. Ofuna chithandizowo anaphatikizapo azimayi anayi amabanja amene anauzidwa kuti mizimu ya ana awo akufa ndiyo inali kuwavutitsa. “Kenaka azimayiwo anauzidwa kulipira mayeni 10 miliyoni [$80,000, U.S.] kuti adzawapempherere,” inatero Mainichi Daily News. Mayi wina wazaka 64 anapereka ndalama zoposa mayeni 6.65 miliyoni (pafupifupi $53,000). Mayiyo anafunsira ansembewo za matenda a mwana wake. “Akuti iwo anamuuza mayiyo kuti adzakumana ndi tsoka pokhapokha atachita mapemphero apadera okumbukira mizimu ya makolo ake ndi oingitsa mizimuyo,” inatero The Daily Yomiuri.

Chidziŵitso cholongosoka cha Baibulo chikanathandiza anthu ameneŵa omwe sanadziŵeko kanthu kuti asawabere. Limanena momvekera bwino kuti sou imafa. (Ezekieli 18:4 NW) Akufa “sadziŵa kanthu bi,” amatero Mlaliki 9:5. Motero akufa sangavulaze amoyo. Ndiponso amoyo sangathandize akufa.

Njira Zambiri za Kuba m’Dzina la Chipembedzo

Ena chifukwa cha umbombo wawo amanyengedwa ndi anthu akuba opembedza. Ku Australia banja lina lomwe limadzinenera kuti lili ndi mphamvu zapadera zodalitsa ndalama ndi kuzichulukitsa linapatsidwa $100,000 ndi mwamuna wina amene anali kufuna kuti ndalama zake zichuluke. Anauzidwa kuika ndalamazo m’bokosi ndi kuwapatsa iwo kuti “aziyeretse.” Banjalo linatenga ndalamazo ndi kupita nazo m’chipinda china kukazidalitsa pamene iye akudikira. Pamene linabwerera, linambwezera bokosilo, ndi kumchenjeza kuti asatsegule bokosilo, zivute zitani mpaka chaka cha 2000. Koma nanga bwanji akatsegula? Anauzidwa kuti “matsengawo adzasukuluka, ndipo iyeyo adzachita khungu, tsitsi lake lidzasosoka, adzadwala kansa, ndiye adzafa ndi matenda a sitiroko.” Koma, patatha milungu iŵiri, mwamunayo anayamba kukayikira natsegula bokosilo. Zodabwitsa! Linali lodzaza ndi mapepala ong’ambikang’ambika. Iyeyo amati analakwa yekha, inatero nyuzipepala yomwe inasimba za nkhaniyi, ndipo chodabwitsa nchakuti, “wayamba kuchita dazi.”

Ku Italy kuba m’dzina la chipembedzo kwasintha, kukuchitika m’njira yatsopano: Onyenga amene amanamizira kukhala Akatolika odzipereka abera ansembe ena. Akubawo amapezera mpata pa mwambo wa Akatolika wopereka ndalama za Misa ya anthu ena akufa. Kodi amazichita motani? Magazini yachikatolika yotchedwa Famiglia Cristiana inati onyengawo amalonjeza kulipiriratu za Misa zingapo za akufa kugwiritsira ntchito cheke chabodza cholembapo ndalama zambiri koposa zomwe zikufunika. Amapusitsa wansembe wogona kuti awabwezere chenje pakashi. Akubawo amatenga ndalamazo, ndipo wansembeyo amatenga cheke chimene amakachikana kubanki!

Ku United States, kaŵirikaŵiri okalamba amazingidwa ndi zipembedzo zimene zikufuna atsopano kuti zidzadzitse matumba ndi ndalama. “M’dziko lonseli zipembedzo zikutsata mwambo wofunika wa onyenga wakuti: Tsatani a ndalama,” inalemba motero magazini ya Modern Maturity. “Kuti zipeze ndalamazo, zimalonjeza zosiyanasiyana kuyambira za thanzi, kusintha kwa ndale ndi ufumu wakumwamba womwe.” Munthu wina wothandiza ena kusiya zipembedzo zotero anati: “Okalamba ndiwo amene amabweretsa ndalama m’zipembedzozo.”

Ndalama zimene amawononga zimakhala zochuluka. “Ndikudziŵa zitsanzo zambiri za anthu amene adzisaukitsa okha,” anatero loya wina wa ku New York amene wakambapo milandu yambiri ya zipembedzo. “Imakhudza anthu osiyanasiyana kuyambira aja amene anauzidwa kupereka ndalama zosachepera [$100,000] mpaka aja amene alibe choti angapereke kusiyapo macheke awo a Chithandizo cha Boma basi.” Anawonjezera kuti: “Zimenezo zimawaloŵetsa m’mavuto—anthuwo ndi mabanja awo omwe.”

Motero chenjerani! Anthu akuba ali pantchito yawo. Chinyengo pokonza nyumba, chinyengo pamalonda a patelefoni, ndiponso kuba m’dzina la chipembedzo ndi zitsanzo zochepa chabe za mmene amachitira ntchito yawoyo. Nkosatheka kunena njira zawo zonse mmene amachitira, popeza nthaŵi zonse amakhala ndi njira zatsopano zachinyengo. Koma mosakayikira zimene zanenedwa muno zakusonyezani kufunika kwa kukhala maso, ndipo imeneyo mwina ndiyo njira yanu yokha yachitetezo. (Onani bokosi lakuti “Zimene Mungachite Kuti Asakubereni.”) Chenjezo lakale la mwambi wa m’Baibulo nloyenerera: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.”—Miyambo 14:15.

[Zithunzi patsamba 24]

Mamiliyoni a anthu amakhulupirira kuti mwa kulipira ndalama akhoza kuthandiza kapena kutonthoza okondedwa awo akufa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena