Kuteteza Thanzi la Ana
LIPOTI laposachedwa la bungwe la United Nations Children’s Fund (UNICEF), mu The Progress of Nations, likusonyeza kuti pakhala kuwongokera kwakukulu pa thanzi la ana m’maiko ambiri. Mwa kugwirizana kwa maboma ndi mabungwe a m’maiko osiyanasiyana, chiŵerengero cha imfa za ana osakwanitsa zaka zisanu chatsika m’maiko ambiri. Komabe, The Progress of Nations inasonyezanso kuti chaka chilichonse miyoyo ya ana ena mamiliyoni ikhoza kupulumutsidwa mwa kugwiritsira ntchito njira zosavuta ndi zosalira ndalama zambiri, makamaka m’maiko omatukuka kumene. Makolo m’maiko ameneŵa ndiponso kwina konse akhoza kupeza malingaliro otsatirawa m’lipotilo kukhala othandiza.
Kuyamwitsa. “Kuyamwitsa ndiyo njira yoyamba yabwino kwambiri yopezera thanzi ndi chakudya chabwino,” linalangiza motero lipotilo. Malinga ndi bungwe la World Health Organization (WHO), “miyoyo ya ana oposa miliyoni ingamapulumuke pachaka kudakakhala kuti ana onse amawayamwitsa pamiyezi isanu ndi umodzi yoyambirira.” Popeza zipatala za onse ndiponso za azimayi ndizo zikupereka malangizo bwino, a UNICEF ndi WHO akulimbikitsa “zipatala kutsata njira yoyanja ana.” Cholinga chawo ndicho kulimbikitsa zipatala kuti zizithandiza amayi a ana obadwa kumene ndiponso kupereka malangizo oyenera pa za kuyamwitsa.
Ukhondo ndiponso madzi abwino. “Matenda angachepe mwa kukhala ndi madzi abwino, mwa kugwiritsira ntchito zimbudzi, mwa kusamba m’manja asanagwire chakudya, ndiponso mwa kukonza ndi kusunga chakudya bwino,” linatero lipotilo. Ngakhale kuti m’malo ambiri pamafunika kuyesayesa kwakukulu kuti apeze madzi, madzi abwino ngofunika kwambiri pa thanzi la mwana ndi banja lonse.
Zakudya. Malinga ndi lipotilo, kuwonjezera Vitameni A kukhoza kupulumutsa ana okwana mamiliyoni atatu kuti asamafe chaka ndi chaka. Chothetsera vutolo chilipo ndipo nchoti titha kuchipeza, likutero lipotilo, ndipo tingachipeze mwa kukhala ndi zakudya zamitundumitundu, kukonza chakudya chopatsa thanzi, kapena kumagaŵira mibulu ya vitameni A. Kugaŵira ana aang’ono nthaŵi ndi nthaŵi mibulu ya Vitameni A yogulidwa ndi masenti aŵiri kwayamba kale kuthandiza m’malo amene vitameni A imasoŵa kwambiri. Ndiponso zakudya zina zabwino ndi zonga mapapaya, mango, karoti, zamasamba, ndi mazira.
Mankhwala a Oral Rehydration. UNICEF imati theka la ana amene amafa pachaka chifukwa cha matenda otseguka m’mimba angatetezedwe mwa kugwiritsira ntchito mankhwala osakwera mtengo ndi osavuta kapangidwe kake, chabe kungosanganiza madzi oyera, mchere, ndi shuga kapena ufa wa mpunga.a Makolo ayeneranso kumapitiriza kumpatsa mwanayo chakudya. Pakadali pano, pafupifupi ana miliyoni imodzi akupulumuka mwa njira imeneyi.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti mumve zambiri pa za kuteteza thanzi la ana anu, chonde onani Galamukani! ya April 8, 1995, masamba 3-14.
[Mawu a Chithunzi patsamba 25]
WHO