Umoyo Wabwino Kaamba ka Mtundu Wonse wa Anthu—Liti?
“Ntchito yapoyera ya umoyo wabwino ya maiko 67 osauka koposa pa maiko otukuka kumene, kusiyapo China, imawononga zochepa pa kusamalira kwa umoyo konse kuposa ndi zimene maiko olemera amawononga pa mankhwala ochepetsako kudera nkhaŵa okha.”—Health Crisis 2000.
“UMOYO wabwino kaamba ka onse podzafika chaka cha 2000”—kalankhulidwe kameneko kakhala kakubwerezedwabwerezedwa makamaka chiyambire International Conference on Primary Health Care (Msonkhano wa Kusamalira kwa Umoyo m’Mbali za Kumidzi), woperekedwa kumbuyoko mu 1978 ndi WHO (World Health Organization) ndi UNICEF (United Nations Children’s Fund). Mwakusonkhanidwa ndi nthumwi kuchokera mu mitundu 134, msonkhanowo unaitanira kaamba ka chisamaliro cha mitundu yonse ponena za kukulira komwe ndithudi kukusoweka mu mbali ya umoyo padziko.
Mtsogoleri wa lamulo panthaŵiyo wa UNICEF, Henry R. Labouisse, ananena kuti: “Chimodzi cha zifukwa zimene tasonkhanira pano lero kuli kutsimikiza kwathu kokulira kwakuti kulekana koipa pakati pa mwaŵi wa umoyo m’mbali zosiyanasiyana zadziko, ndiponso mkati mwa maiko, sikungalekeleredwe.”
Msonkhano usanachitike, ripoti linalongosola ponena za kusagwirizana kwadziko lonse kokulira pakati pa okhala ndi umoyo wabwino mu mitundu yolemera ndi osakhala ndi umoyo wabwino kwina kuli konse. Ripoti la UNICEF chaka chimenecho linanena kuti mu maiko ena osauka kwambiri “kokha 10% ya anthu amenewa ali ndi potulukira ku kusamalira kolongosoka kwaumoyo wabwino” ndipo “maperesenti makumi aŵiri—mwinamwake—amamwa madzi aukhondo.”
Msonkhanowo unaitanira kaamba ka “kupititsa patsogolo kwa kaperekedwe ka zakudya ndi kadyetsedwe kolongosoka, kupatsidwa kokwanira kwa madzi abwino ndi magwero aukhondo; ndi kusamalira kwa umoyo wabwino wa mayi ndi khanda, . . . kupatsidwa kwamankhwala ofunika.”
Izi ziri zinthu zamtengo kwenikweni, makamaka kwa anthu okhala mu mitundu yosauka. Kodi ndalama za kusowa koteroko zikapezedwa kuti? Msonkhanowo unanena kuti “mtendere, kupuma bwino ndi kuleka kupanga zida zankhondo” kukatulutsa unyinji wa ndalama kaamba ka chifunocho. Chotero, magazini ya World Health, yofalitsidwa ndi WHO, inafulumizidwa kuchitira ndemanga kuti: “Tangolingalirani dziko labwino mu limene luso lonse, zotaidwa ndi anthu ndi chuma chakuthupi chomwe pakali pano chikuperekedwa mu zida za nkhondo m’malo mwake chitaperekedwa ku kuwongolera umoyo wadziko!”
Koma mu zaka zomwe zangopita chiyambire 1978, kodi mwauwona mtendere woterowo, kupuma kwabwino, ndi kuleka kupanga zida zankhondo kukuchitika? Kodi mitundu kwenikweni sikupita mu njira yosiyanako, pamene vuto la umoyo wabwino likupitirizabe kukula?
[Chithunzi patsamba 3]
Ana a sukulu mu Colombia akupatsidwa katemera
[Mawu a Chithunzi]
P. Almasy/WHO