Thanzi Labwino kwa Onse—Kodi Zingatheke?
KODI mukufuna kuti inuyo ndi banja lanu mukhale ndi thanzi labwino? Ndithudi mukutero. Koma pamene ambiri a ife nthaŵi zina timadwala matenda osadetsa nkhaŵa, anthu miyandamiyanda amakhala ndi zofooka za m’thupi kwa moyo wawo wonse.
Komabe, anthu akuyesayesa mwamphamvu kuchepetsa matenda. Talingalirani za bungwe la Word Health Organization (WHO) limene limagwira ntchito pansi pa bungwe la United Nations. Pamsonkhano umene bungwe la WHO linachititsa mu 1978, nthumwi za ku mayiko 134 ndi timabungwe ta UN tokwana 67 anavomereza kuti thanzi sikungomasuka chabe ku matenda. Anati thanzi ndilo “kukhala bwino zedi m’thupi, maganizo ndi chikhalidwe cha anthu.” Ndiyeno nthumwizo zinalimba mtima ndipo zinati thanzi ndilo “ufulu wachibadwidwe wa munthu wofunika kwambiri”! Choncho WHO inakhazikitsa cholinga chopezera “anthu onse padziko lapansi thanzi labwino.”
Cholinga chimenecho n’chosangalatsa kwambiri ndiponso chosiririka. Koma kodi adzachikwaniritsadi? Pa ntchito zonse zimene anthu ayesera, sayansi ya zamankhwala yakhaladi imodzi mwa ntchito zodalirika ndi zoyamikirika koposa. Malinga ndi nyuzipepala ina ya ku Britain ya The European, anthu m’mayiko a Kumadzulo awazoloŵera kwambiri “maganizo oyambirira a sayansi ya zamankhwala ofuna ‘mankhwala odabwitsa’: nthenda iliyonse kukhala ndi pilisi lakelake.” M’mawu ena, timafuna sayansi ya zamankhwala kutipezera mankhwala osavuta ochiritsa nthenda iliyonse kamodzin’kamodzi. Kodi akatswiri a zamankhwala atha kuchitadi zinthu zazikulu ngati zimenezi zimene tikuwayembekeza kuchita?