Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g97 10/8 tsamba 8-11
  • Paradaiso Wopanda Mavuto—Adzakhalakodi Posachedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Paradaiso Wopanda Mavuto—Adzakhalakodi Posachedwa
  • Galamukani!—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mphamvu Imene Idzabweretsa Paradaiso
  • Zomwe Zikuchitikadi
  • “Tidzaonana M’Paradaiso”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Pambuyo pa Harmagedo, Dziko Lapansi Laparadaiso
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Njira Yobwerera kumudzi wa Paradaiso
    Galamukani!—1997
  • Paradaiso wa Chisangalalo kaamba ka Anthu Onse
    Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
Onani Zambiri
Galamukani!—1997
g97 10/8 tsamba 8-11

Paradaiso Wopanda Mavuto—Adzakhalakodi Posachedwa

“UDZAKHALA ndi ine m’Paradaiso.” Mawu ameneŵa anamlimbikitsa kwambiri chotani nanga munthuyo amene kale anali wambanda! Sikuti munthuyo anaganiza kuti sadzapita kumoto wa helo ndipo kuti adzapita kumwamba atamwalira. M’malo mwake, wakubayo amene anali pamodzi ndi Yesu anatonthozedwa ndi chiyembekezo chakuti adzaukitsidwa kukhalanso ndi moyo pamene Paradaiso adzabwezeretsedwa papulanetili. Chonde, dziŵani, amene ananena mawu amphamvuwo onena za Paradaiso—Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu.—Luka 23:43.

Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera Kristu kulonjeza Paradaiso? Wakubayo anapempha: “Yesu, ndikumbukireni mmene muloŵa Ufumu wanu.” (Luka 23:42) Kodi Ufumu umenewu nchiyani, ndipo pali kugwirizana kotani pakati pa uwo ndi paradaiso wapadziko lapansi? Kodi zimenezi zimatsimikiza motani kuti Paradaisoyo adzakhala wopanda mavuto?

Mphamvu Imene Idzabweretsa Paradaiso

Mukuvomereza kuti paradaiso weniweni akhoza kukhalapo padziko lapansi pokhapokha mavuto onse amene alipo lerolino atatha. Zoyesayesa za anthu kuti awathetsa zalephera, monga momwe mbiri yakale imasonyezera bwino. Mneneri wachihebri Yeremiya anati: “Inu Yehova, ndidziwa kuti . . . sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Tsono, ndani amene angathetse mavuto onse alipowa?

Kupenga kwa Mphepo Ndiponso Kuipitsa Malo. Pamene mkuntho unaomba pa Nyanja ya Galileya kunyamula mafunde aakulu okwanira kuswa ngalawa, amalinyero anadzutsa mnzawo wa paulendo yemwe anali mtulo. Atadzuka, iye anangoti kwa nyanjayo: “Tonthola, khala bata!” Uthenga Wabwino wa Marko umalongosola zimene zinachitika: “Mphepo inaleka, ndipo kunangwa bata lalikulu.” (Marko 4:39) Mnzawo wapaulendoyo sanali winanso koma Yesu. Anali ndi mphamvu zolamulira mphepo.

Ndi Yesu yemweyo amene analosera mwa mtumwi Yohane kuti nthaŵi idzadza pamene Mulungu ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’ (Chivumbulutso 1:1; 11:18) Sikuti iyi ndi ntchito yovuta kwa Iye amene anawononga dziko lonse la anthu osapembedza pa Chigumula m’tsiku la Nowa.—2 Petro 3:5, 6.

Upandu ndi Chiwawa. Baibulo limalonjeza kuti: “Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:9, 11) Kachiŵirinso, ndi Mulungu, Yehova, amene akulonjeza kuchotsapo upandu ndi chiwawa, akumasungira Paradaiso anthu ofatsa.

Umphaŵi ndi Njala. Kupanda chilungamo kumene kulipo m’tsiku lathu kumachititsa maboma kumbali zina kukundika “mulu” wa chakudya, kwinaku maiko osauka akumavutika. Mabungwe achithandizo, omwe amathandizidwa ndi anthu achifundo padziko lonse lapansi, amayesa kupereka zinthu zofunika kwambiri pamoyo koma kaŵirikaŵiri amalephera pamene mapulani awo othandizira alephereka chifukwa cha kusoŵeka kwa bata ndi mtendere. Yerekezerani zimenezi ndi zimene mneneri Yesaya analemba: “M’phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.” (Yesaya 25:6) Kodi zimenezi sizikumveka monga kuti njala sidzakhalakonso? Zoonadi.

Nkhondo. Zoyesa kulamulira dziko lino mwa kukhala ndi ulamuliro umodzi pa maiko onse zalephereka. Bungwe la League of Nations, lomwe linayambika mu 1920, linalephera kuletsa Nkhondo Yadziko II ndipo linagwa. Bungwe la United Nations, lomwe kaŵirikaŵiri amati ndi lokhalo lomwe lidzadzetsa mtendere, limavutika kuti lithetse mikangano kumalo komwe kuli nkhondo. Ngakhale kuti amalengeza kwambiri zoyesayesa zake za mtendere, nkhondo zili ponseponse, kaya zachiŵeniŵeni, za mafuko, kapena za maiko. Boma la Ufumu wa Mulungu limalonjeza kuchotsa magulu omenyana amene aliko masiku ano ndi kuphunzitsa anthu ake njira zamtendere.—Yesaya 2:2-4; Danieli 2:44.

Kuwonongeka kwa Mabanja ndi Makhalidwe Abwino. Kusweka kwa mabanja nkofala. Pali kupanduka kwa ana ponseponse. Anthu amtundu uliwonse amachita chisembwere. Komabe, malamulo a Mulungu sanasinthe kuyambira pachiyambi. Yesu anatsimikizira kuti “mwamuna adzasiya atate wake ndi amake, nadzaphatikizana ndi mkazi wake, ndipo aŵiriwo adzakhala thupi limodzi . . . Chifukwa chake ichi chimene Mulungu anachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mateyu 19:5, 6) Yehova Mulungu analamulanso kuti: “Lemekeza atate wako ndi amako . . . kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko.” (Aefeso 6:2, 3) Makhalidwe ameneŵa adzafunga padziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu.

Matenda ndi Imfa. “Yehova . . . adzatipulumutsa,” analonjeza motero mneneri Yesaya, “ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.” (Yesaya 33:22, 24) “Mphotho yake ya uchimo ndi imfa,” anavomereza motero mtumwi wachikristu Paulo, “koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 6:23.

Yehova Mulungu adzachotsa mavuto onsewa kupyolera m’boma lake lakumwamba limene lili m’manja mwa Mwana wake, Kristu Yesu. Komabe, mungati, ‘Izi zikumveka ngati zosatheka. Kunena zoona, zingakhale zosangalatsa ngati zingachitikedi, koma kodi zidzaterodi?’

Zomwe Zikuchitikadi

Kwa anthu ambiri, zoti nkukhala ndi moyo m’paradaiso wopanda mavuto padziko pompano zimangomveka ngati zosatheka. Ngati ndimo mmene mumamvera, onani umboni wakuti zimenezi zidzathekadi.

Mboni za Yehova ndi gulu la anthu oposa mamiliyoni asanu lopezeka m’maiko osiyanasiyana amene pali pano m’mipingo yawo 82,000 yopezeka m’maiko 233 muli mavuto ochepa. Mukhoza kufikapo pa wina wa misonkhano yawo, magulu akulu kaya ochepa, ndipo kodi mukapeza zotani?

(1) Malo Osangalatsa ndi Aukhondo. Pothirirapo ndemanga za msonkhano wina wa Mboni za Yehova ku Norwich, England, manijala wa sitediyamu ya mpira anati: “Mtendere umene unalipo masiku anayi ameneŵa . . . ngwochititsa chidwi. Umapeza bata losiyana kwambiri ndi masiku anayi alionse amene ungakhale m’dziko la malondali ndi umoyo wotizingawu. Zoonadi Mboni zili ndi kanthu kena kamene kamazisiyanitsa ndi ena ndipo nkovuta kukalongosola.”

Wolangiza ophunzira wa kampani yomanga yemwe anakachezera maofesi a ku London a Mboni za Yehova anati: “Ndinachita chidwi kwambiri ndi zimene ndinaona ndi kumva ndipo ndinatengeka mtima ndi mkhalidwe wa mtendere ndi bata lomwe lilipo osati m’nyumba zanu zokha komanso pakati pa [amuna ndi akazi]. Ndilingalira kuti kakhalidwe kanu ndi chimwemwe kali ndi zambiri zoti nkuphunzitsa dziko lonse lamavutoli.”

(2) Chisungiko ndi Mtendere. Wolemba nkhani mu Journal de Montréal ku Canada anati: “Sindine Mboni. Koma ndine mboni pankhani yakuti Mboni zimachitira umboni kugwira ntchito mwakhama ndiponso khalidwe labwino. . . . Izo zikanakhala anthu okha m’dziko, bwenzi sitikutseka zitseko zathu usiku ndi kuika maalamu kuopa akuba.”

(3) Mboni zili zokhulupirika ku boma la Ufumu wa Mulungu. Uchete wawo pa zandale umakwiyitsa ena, ngakhale kuti siziyenera kutero. Pamene siziloŵerera pa zoyesayesa zandale zokonza zinthu sikuti sizimafuna kuwongolera kakhalidwe ka anthu ayi. M’malo mwake, zimafuna kumachita zinthu zokondweretsa amene amalamulira kupyolera m’boma lakumwamba, Mlengi, Yehova Mulungu.

Zikhulupiriro za Mboni, zozikidwa pa Mawu a Mulungu okha, Baibulo, zimaziletsa kukhala kagulu kampatuko kapena kotsata munthu. Zimasamala za anthu ena onse, kaya zikhulupiriro za anthuwo za chipembedzo zikhale zotani. Ayi, sizimakakamiza anthu amenewo kusintha malingaliro awo. Izo zimatengera Mtsogoleri wawo, Kristu Yesu, mwa kusonyeza umboni wa m’Malemba wa Paradaiso wopanda mavuto amene adzakhazikitsidwa posachedwapa padziko lapansi.—Mateyu 28:19, 20; 1 Petro 2:21.

(4) Thanzi Lauzimu ndi Chimwemwe. Kunena zoona, Mboni za Yehova sizinena kuti zilibiretu mavuto panthaŵi ino. Zimenezi nzosatheka kwa anthu amene nawonso anabadwa ndi uchimo wochokera kwa Adamu. Koma mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu, zimayesetsa kukulitsa makhalidwe monga “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso.” (Agalatiya 5:22, 23) Ndi kulambira kwawo Yehova kupyolera mwa Kristu Yesu kumene kumawagwirizanitsa ndi kusunga chiyembekezo chawo chili chamoyo.

Tikhulupirira kuti mukapita kumalo osonkhanira a Mboni kwanuko, mudzakhutira kuti Mulungu adzasandutsa dziko lapansili kukhala paradaiso weniweni.

Mavuto aliko leroŵa adzatha. Ngakhale kupanda ungwiro kumene kwakhalako nthaŵi yaitali kudzachoka pang’onopang’ono pamene mapindu a nsembe ya dipo ya Kristu adzagwiritsiridwa ntchito pa anthu omvera. Ndithudi, mukhoza kudzakhala ndi thanzi langwiro ndi chimwemwe.

Kukonzekera kosavuta kudzakuthandizani kudzasangalala ndi zimenezo. Funsani Mboni zikupatseni buku lanulanu la Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha.a Ndi limeneli, mukhoza kuphunzira pakanthaŵi kochepa zimene Mulungu amafuna kwa inu kuti inunso mudzasangalale ndi moyo m’paradaiso wopanda mavuto kwamuyaya.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Mawu Otsindika patsamba 10]

Zikhulupiriro za Mboni, zozikidwa pa Baibulo lokha, zimaziletsa kukhala kagulu kampatuko kapena kotsata munthu

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Maziko a paradaiso wopanda mavuto akuyalidwa tsopano

Posachedwa, padziko lapansi padzakhala paradaiso weniweni

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena